Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 10/15 tsamba 14-17
  • Kufikira Anthu a Mitundu Yonse mu Atene Wamakono

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufikira Anthu a Mitundu Yonse mu Atene Wamakono
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Gawo la Anthu Osiyanasiyana
  • Ofunika a Amitundu Akufika
  • Odalitsidwa ndi Zotulukapo Zabwino
Nsanja ya Olonda—1995
w95 10/15 tsamba 14-17

Kufikira Anthu a Mitundu Yonse mu Atene Wamakono

PAMENE mtumwi Paulo anapita kukacheza ku Atene cha mu 50 C.E., mzindawo unali ukali malo apakati a zamalonda, ngakhale kuti unalibenso ulemerero wake wakale. Buku lina la mbiri likuti: “[Atene] anapitirizabe kukhala malo apakati a zauzimu ndi zamaphunziro a Greece, ndiponso malo amene anthu ophunzira ndi okhala ndi mphamvu a panthaŵiyo anakhumba kukawaona.”

Pamene Paulo anali kumeneko, mwina anali ndi mpata wa kulalikira Ayuda, Aatene achikunja, ndi anthu ochokera ku malo osiyanasiyana. Pokhala mphunzitsi watcheru ndi waluso, m’nkhani ina ananena kuti Mulungu anapatsa “zamoyo zonse moyo ndi mpweya,” kuti “ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu,” ndi kuti “onse ponseponse atembenuke mtima” chifukwa Iye adzaweruza “dziko lokhalamo anthu.”​—Machitidwe 17:25-31.

Gawo la Anthu Osiyanasiyana

M’zaka makumi zaposachedwapa Atene wakhalanso mzinda wokopa anthu kuchokera konsekonse. Akazembe a kumaiko ena ndi asilikali ankhondo afika monga otumidwa pa nkhani za boma. Achichepere ochokera ku Afirika ndi maiko a ku Middle East akukhala kumeneko monga ophunzira a m’mayunivesite. Alendo ogwira ntchito a ku Afirika, Asia, ndi maiko a ku Eastern Europe aloŵamo. Muli anthu ambiri a ku Phillipines ndi ena ochokera ku Southeast Asia, amene abwera kudzafuna ntchito za m’nyumba. Ndipo othaŵa kwawo a ku maiko oyandikana nawo ndi kumene kulibe mtendere kuzungulira dziko lonse lapansi akufika mosalekeza.

Mkhalidwe umenewu ukupereka chitokoso kwa alaliki a uthenga wabwino wa Ufumu akumaloko. Anthu ambiri okhalako kwakanthaŵi amalankhula Chingelezi koma ena amangolankhula zinenero zawo. Anthu amenewa ali ndi miyambo yawo ndi zipembedzo zawo zambiri zosiyanasiyana. Pakati pa alendowa, mungapeze odzitcha kukhala Akristu, Asilamu, Ahindu, Abuda, okhulupirira mizimu, osadalira Mulungu ndi okana Mulungu. Mboni za Yehova ziyenera kuphunzira kusintha njira zawo za maulaliki kuti ziyenerane ndi mikhalidwe yosiyanasiyana ya anthuwa.

Popeza ambiri a alendo ameneŵa apyola m’nthaŵi zovuta, kaŵirikaŵiri amakhala ndi mafunso ponena za tanthauzo la moyo ndi ziyembekezo za mtsogolo. Ena amalemekeza Baibulo kwambiri ndipo samakana zimene limanena. Ambiri m’gawo la anthu osiyanasiyana limeneli ngodzichepetsa, ofatsa, ndi anjala ya choonadi. Amaona kukhala aufulupo kufunafuna choonadi chifukwa chakuti ali kutali ndi mabanja awo ndi makhalidwe a kwawo.

Mu 1986, mpingo wa Chingelezi woyamba unalinganizidwa mu Atene kuti ufole gawoli. Chiwonjezeko chake chakhala chachikulu. M’zaka zisanu zapitazo, pafupifupi atsopano 80 abatizidwa. Chotulukapo chake nchakuti kwakhazikitsidwa mpingo Wachiluya, mpingo wa Chipolishi, ndi kwakanthaŵi, kagulu ka Chifrenchi mu Atene kakhazikitsidwa. Ena ochokera ku mpingo wa Chingelezi apita kukathandiza mipingo ina imeneyo ndi magulu chakumpoto ku Tesalonika, ku Heraklion, Krete, ndi ku Piraeus, doko la Atene. Kodi mungakonde kukumana ndi ena a anthu ochokera kunja amene aphunzira choonadi mu Atene?

Ofunika a Amitundu Akufika

Thomas anabadwira ku Asmara, Eritrea, ndipo anakula monga Mkatolika wodzipereka. Pamene anali ndi zaka 15, analoŵa umonke. Anafunsa mkulu wa amonke kuti: “Kodi kuli kotheka motani kuti Mulungu mmodzi ali Milungu itatu?” Mkuluyo anayankha nati: “Chifukwa timavomereza zimene papa amanena pa zinthu zauzimu. Ndiponso, chimenechi ndi chinsinsi, ndipo ndiwe wochepa kwambiri kuchimvetsetsa.” Pambuyo pa zaka zisanu m’nyumba ya amonkeyo, Thomas anachoka, wogwiritsidwa mwala ndi wokhumudwitsidwa ndi khalidwe ndi ziphunzitso za tchalitchicho. Komabe sanaleke kufunafuna kwake Mulungu woona.

Tsiku lina atangosamukira ku Atene, anapeza kope la Nsanja ya Olonda pakhomo pake, limene linali ndi mutu wakuti “Thanzi ndi Chimwemwe Zikhoza Kukhala Zanu.” Anaiŵerenga nthaŵi zingapo. M’magazini amodzimodziwo, anaŵerenga kuti tiyenera kuthanga tafuna Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake. (Mateyu 6:33) Thomas anagwada ndi kupempha Mulungu kuti amsonyeze mmene angachitire zimenezi, akumalonjeza kuti: “Ngati mundisonyeza mmene ndingafunire Ufumu wanu, ndidzapereka miyezi isanu ndi umodzi ya moyo wanga kuti ndiphunzire mmene ndingakutumikirireni.” Mkati mwa mlungu wachinayi pambuyo pake, Mboni ziŵiri zinagogoda pa chitseko chake. Pamenepo Thomas anavomera phunziro la Baibulo, ndipo miyezi khumi pambuyo pake anabatizidwa. Iye akuti: “Yehova anayankhadi pemphero langa, ndipo anandipatsa mwaŵi wa kukhala mmodzi wa Mboni zake. Chikondi chake tsopano chikundisonkhezera kufunafuna Ufumu wake choyamba ndi chilungamo chake m’moyo wanga.”

Pamene Mboni zina ziŵiri zinali kulalikira kukhomo ndi khomo, zinapeza dzina lachilendo pafupi ndi belu.

“Mukufunanji?” Liwu lamkazi linamveka m’cholankhulirana.

Mmodzi wa Mbonizo ananena kuti iwo anali kuyesa kupeza anthu olankhula Chingelezi amene anali okondweretsedwa ndi Baibulo.

“Ndinu achipembedzo chanji?” mkaziyo anafunsa.

“Ndife Mboni za Yehova.”

“Eya, chabwino! Tabwerani pamwamba pano.”

Iwo anachita motero ndipo, pamene chitseko cha chikepe chinatseguka, mwamuna wamkulu thupi kwambiri wankhope yoipidwa anali ataima mmenemo. Koma mkaziyo analankhula mokuwa ali mkati.

“Aloleni aloŵe. Ndikufuna kulankhula nawo.”

Mkaziyo anauza Mbonizo kuti anazungulira dziko lapansi ndi gulu la maseŵero la mwamuna wake, ndipo dzulo lakelo, anali kupemphera kuti apeze Mboni za Yehova. Motero panthaŵi yomweyo phunziro la Baibulo linayamba. Popeza nthaŵi yawo yokhala m’Greece inali yochepa, analinganiza kuphunzira katatu pa mlungu, anamaliza buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha m’milungu khumi chabe.

Nyengo ya maseŵera yotsatirapo inawabweretsanso ku Greece. Mkaziyo anapitiriza phunziro lake ndi kupanga kupita patsogolo kwabwino kwambiri. Pambuyo pa miyezi ingapo, anagwirizana ndi Mboni m’ntchito yolalikira monga wofalitsa wosabatizidwa ndi kuyambitsa phunziro lake loyamba la Baibulo mwamsanga. Ndi yani? Mwamuna wake, amene akuchita chidwi kwambiri ndi Mboni ndi kusintha kwa mkazi wake.

Allan, mwana wa mphunzitsi Wachiprotesitanti, anakulira ku South Africa. Kuyambira pa ubwana wake, anakhulupirira kuti Baibulo ndilo vumbulutso louziridwa la Mulungu. Posakhutira ndi chipembedzo chake, anatembenukira ku filosofi ndi ndale, koma izi zinangomgwiritsanso mwala koposa ndi kale lonse. Atasamukira ku Greece, malingaliro ake a kugwiritsidwa mwala anakula. Anaona kuti moyo wake unalibe chifuno, ndi kuti anali panjira yogoma.

Usiku wina kanthu kena kanachitika. “Ndinagwada ndi kutsegulira Mulungu mtima wanga,” Allan akusimba motero. “Ndili ndi misozi ya chisoni chifukwa cha moyo wanga, ndinapempha Mulungu kuti anditsogolere kwa otsatira ake oona. Ndinalonjeza kuti ndizayenda m’kuunika kwa chitsogozo chake.” Mlunguwo usanathe, anali m’sitolo ina ndipo analoŵa m’makambitsirano ndi mwini sitoloyo, mkazi, amene anali Mboni. Makambitsiranowo analidi posinthira moyo wa Allan. “M’masiku otsatirapo, ndinaona zikhulupiriro zanga zokondeka kwambiri zikusukuluka: Utatu, moto wa helo, kusafa kwa moyo​—mwachionekere zonse sizinali ziphunzitso za Baibulo.” Ku Nyumba ya Ufumu, Mboni ziŵiri zokwatirana zinampempha kuphunzira naye Baibulo. Anavomera ndi kupita patsogolo mofulumira. “Choonadi chinandichititsa kukha misozi ya chimwemwe,” akukumbukira motero Allan, “ndipo chinandimasula.” Chaka chimodzi pambuyo pake anabatizidwa. Lerolino ali wachimwemwe kutumikira monga mtumiki wotumikira mumpingo wakumaloko.

Elizabeth ndi wa ku Nigeria, kumene anafunafuna Mulungu m’matchalitchi osiyanasiyana koma sanakhutirebe. Chimene chinamuwopsa kwambiri chinali chiphunzitso cha chizunzo chosatha m’moto wa helo. Pamene anafika ku Atene ndi banja lake, Mboni ziŵiri zinafika pakhomo pake, ndipo phunziro la Baibulo linayambika. Elizabeth anasangalala kudziŵa kuti Mulungu samazunza anthu, koma amapereka chiyembekezo cha moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. Anali ndi pakati pa mwana wake wachinayi, pamene anafuna kupachotsa. Ndiyeno anaphunzira kuchokera m’Baibulo lingaliro la Yehova la kupatulika kwa moyo. Tsopano ali ndi mwana wamkazi wokongola. Elizabeth anapita patsogolo mofulumira ndipo posapita nthaŵi anabatizidwa. Ngakhale kuti ali ndi ana anayi ndipo akugwira ntchito ya nthaŵi yonse, pafupifupi mwezi uliwonse amatha kuchita upainiya wothandiza. Wadala poona mwamuna wake akuyamba kuphunzira Baibulo. Iye akuti: “Ndapeza Mulungu woona ndi kulambira koona pomalizira pake, chifukwa cha Yehova ndi gulu lake lachikondi”.

Anthu ambiri m’gawo limeneli la anthu osiyanasiyana amafikiridwa mu ulaliki wa m’khwalala, koma pamafunika kupirira kuti akulitse chikondwerero chawo. Izi zinali motero ndi mkazi wina wochokera ku Sierra Leone wotchedwa Sallay. Mboni ina inampatsa trakiti, ndi kutenga keyala yake, ndi kulinganiza kukamchezera. Sallay anakondwerera ndi kuvomera phunziro la Baibulo, koma chifukwa cha kuchuluka kwa zochita kuntchito ndi mavuto ena, silinachitidwe nthaŵi zonse. Ndiyeno mwadzidzidzi anasamuka popanda kusiya keyala yatsopano. Mboniyo inalimbikira mwa kupita komwe anali kumpeza kale, ndipo potsirizira pake Sallay anatumiza uthenga kuti Mboniyo ifike ku nyumba kwake kwatsopano.

Phunzirolo tsopano linachitidwa mokhazikika kwambiri ngakhale kuti Sallay anali m’miyezi yomalizira ya pakati pake. Pambuyo pa kubadwa kwa mwana, Sallay anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Zonsezi zikumveka ngati zosavuta, komatu sizinali choncho. Pa 6:30 a.m., anayenera kukhala wokonzeka kuyenda ulendo wa pabasi wa theka la ola kukasiya mwana wake kusukulu ya mkaka, ndiyeno kupanga ulendo wina wa ola limodzi wa pabasi wopita kuntchito. Ataŵeruka pa ntchito yake ya kuyeretsa, amatenganso ulendo wobwerera kunyumba. Pamausiku a misonkhano, kapena pamene ankapita ku utumiki wa ku munda, ankayenda ola linanso kupita ndi kubwera pabasi, ngakhale kuti anatsutsidwa ndi mwamuna wake. Pamene anali kumsonyeza chikondi ndi chipiriro, anapita patsogolo kufikira pa kudzipereka ndi kubatizidwa. Bwanji ponena za mwamuna wake? Anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu ndipo anavomera kukhala ndi phunziro la Baibulo.

Odalitsidwa ndi Zotulukapo Zabwino

Kwa anthu ambiri ameneŵa kukhala kwawo mu Atene ndi kwakanthaŵi. Ambiri amabwerera ku maiko a kwawo kukauza achibale awo ndi mabwenzi awo uthenga wabwinowo. Ena amapita ku maiko osiyanasiyana a kumadzulo ndi kupitiriza kutumikira Yehova. Awo amene amatsala m’Greece amasangalala ndi zotulukapo zabwino polalikira anzawo a ku maiko akwawo omwe asamukira kumeneko. M’zochitika zina mbewu za choonadi zinabala zipatso pamene alendowo anapita ku dziko lina kumene anakumana ndi Mboni.

Zonsezi zimasonyeza kuti Yehova alibe tsankhu. Amalandira anthu ochokera mu mtundu uliwonse amene amamuwopa ndi kukonda chilungamo chake. (Machitidwe 10:34, 35) Kwa anthu onga nkhosa amenewo, kupita kwawo ku dziko lina kukafuna mapindu a zinthu zakuthupi kunakhala dalitso lalikulu kuposa mmene anaganizira poyamba​—kudziŵa Mulungu woona, Yehova, ndi lonjezo lake la moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama. Inde, Yehova wadalitsadi kopambana zoyesayesa za kufikira anthu a zinenero zachilendo mu Atene wamakono!

[Zithunzi patsamba 16]

Anthu ochokera ku maiko ambiri akumva uthenga wabwino mu Atene

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena