Chochitika Chimene Simuyenera Kuphonya
“Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro” zimachokera kwa Mulungu, Atate wathu wakumwamba. (Yakobo 1:17) Mphatso yoposa zonse imene Mulungu wapereka kwa anthu ochimwa ndiyo makonzedwe a chipulumutso chawo mwa Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu. Imfa ya Yesu monga Momboli wathu imatheketsa moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Pa Luka 22:19, timalamulidwa kukumbukira imfa yake.
Mboni za Yehova zikukupemphani ndi mtima wonse kuti mukakhale nazo pamodzi posunga lamulo la Yesulo. Chochitika chapachaka chimenechi chidzachitidwa dzuŵa litaloŵa padeti logwirizana ndi Nisani 14 pa kalenda ya mwezi ya Baibulo, pamene padzakhala pa Lachiŵiri, April 2, 1996. Sungani deti limeneli kuti musadzaiŵale. Mboni za Yehova zakwanuko zingakuuzeni za malo enieni ndi nthaŵi.