Zoyenera za Wodwala Zilemekezedwa
‘Sindingachite opaleshoni imeneyi popanda mwazi. Ngati ukufuna opaleshoni, ufunikira kuvomereza njira yanga yochiritsira. Ngati si choncho, ufunikira kukafuna dokotala wina.’
MAWU a dokotalawo sanagwedeze chikhulupiriro cha Cheng Sae Joo, mmodzi wa Mboni za Yehova amene amakhala ku Thailand. Atapezedwa ndi meningioma, mtundu wina wa chotupa mu ubongo, Cheng anafunikira kwambiri kuchitidwa opaleshoni. Komanso anali wotsimikiza kumvera lamulo la Baibulo: “Musale . . . mwazi.”—Machitidwe 15:28, 29.
Cheng anapita ku zipatala zina ziŵiri, akumasankha kuchiritsidwa m’dzikolo ngati zinali zotheka. Kumeneko madokotala anakananso kuchita opaleshoni yopanda mwazi, zimene sanayembekezere. Potsirizira pake, Cheng anathandizidwa kupita ku Neurological Institute ya Tokyo Women’s Medical College ndi Hospital Information Services (HIS) ya ku Thailand. Chipatala chimenecho chachiritsa odwala zotupa mu ubongo oposa 200 mogwiritsira ntchito mpeni wa gamma, imodzi ya njira zatsopano kwambiri m’kuchiritsa ndi rediyeshoni.
Panapangidwa makonzedwe akuti Cheng akhale ndi Mboni zachijapani zokhala pafupi ndi chipatalacho. Kagulu kena kanamlandira pa bwalo la ndege, kuphatikizapo Mboni za Yehova ziŵiri zimene zimalankhula Chithayi ndi woimira HIS. Pambuyo pa kupimidwa pafupifupi mlungu umodzi, Cheng anagonekedwa m’chipatala mmene anachitidwa opaleshoni ya mpeni wa gamma. Opaleshoniyo inangotenga pafupifupi ola limodzi. Mmaŵa mwake atatuluka m’chipatalamo, Cheng ananyamuka ulendo wobwerera kwawo ku Thailand tsiku lotsatira.
“Sindinaganizepo kuti thandizo lalikulu lotero lingaperekedwe kupyolera m’makonzedwe ameneŵa,” akutero Cheng. “Ndinachitadi chidwi ndi chikondi chimene anandisonyeza ndiponso ndi kugwirizana kumene kunalipo kumbali zosiyanasiyana zoloŵetsedwamo.”
Posimba nkhaniyi, nyuzipepala yachijapani Mainichi Shimbun inati: “Kufikira pano, kukana kuikidwa mwazi pa zifukwa za chipembedzo kwasonyezedwa. Komabe, kuika mwazi kuli ndi zotulukapo zina zoipa zonga ngati AIDS, ngozi ya kutenga kachilombo konga kaja ka hepatitis C, ndi kuwengedwa. Pa chifukwa chimenechi pali odwala amene samafuna kuikidwa mwazi mosasamala kanthu za zikhulupiriro zawo zachipembedzo.”
Nyuzipepalayo inapitiriza kunena kuti: “Odwala ambiri amene amakana kuikidwa mwazi akakamizika kusamukira kuchipatala china, koma pamenepa pafunikira kuti zipatala zisinthe kuti zizilemekeza chifuno cha wodwala. Pafunika chilolezo cha munthu wodziŵa (wodwalayo akumauzidwa zonse zophatikizidwapo ndiyeno kuvomereza machiritso), ndipo zimenezi zimaphatikizapo kuika mwazi. Iwo ayenera kuzindikira kuti imeneyi si nkhani yongokhudza chipembedzo chakutichakuti.”
Mofanana ndi Cheng Sae Joo, ambiri amene amakonda machiritso opanda mwazi amapita ku zipatala zina. Komabe, amayamikira zoyesayesa za madokotala amene ali okonzekera kulemekeza zoyenera za odwala awo.
Hospital Information Services inalinganizidwa ndi Mboni za Yehova m’nthambi za Watch Tower Society poyesa kuchita zinthu mogwirizana ndi madokotala amene amalemekeza zikhulupiriro zawo. Kuzungulira dziko lonse, HIS imapanga maunansi abwino ndi zipatala, madokotala, antchito zaumoyo, maloya, ndi oweruza.