Chifutukuko ndi Dalitso la Yehova
PROGRAMU yakupatulira pa madzulo a pa September 18, 1995, inagogomezera kuti Yehova Mulungu wadalitsadi chifutukuko cha Mboni zake pa malikulu awo adziko lonse ku Brooklyn, New York.
Anthu oposa 6,000 anamvetsera programu ya kupatulira imeneyi. Anasonkhana ku Brooklyn, kumene kunali programuyo, ndi kumalo enanso, kuphatikizapo pa malo aakulu a maofesi a Mboni za Yehova pafupi ndi Patterson ndi Wallkill, New York, ndi panthambi yawo pafupi ndi Toronto, Canada. Awo amene sanali ku Brooklyn anamvetsera zochitikazo pa mafoni olunzanitsidwa.
Programu Yogwira Mtima
Omvetsera programuyo, Abeteli, monga mmene antchito odzifunirawo amatchedwera, anapanga mbali yaikulu ya banja la Beteli la padziko lonse la anthu oposa 16,400. Ameneŵa amatumikira m’maiko oposa zana limodzi, kumene amasindikiza mabuku a Baibulo ndi kuchita mautumiki ochirikiza mipingo yoposa 78,600 ya Mboni za Yehova m’dziko lonse lapansi.
Chiyembekezo chinali chachikulu pamene programu ya kupatulira inayamba ndi nyimbo pa 6:30 p.m., yotsatiridwa ndi pemphero loperekedwa ndi Karl Klein. Tcheyamani wa programuyo, Lloyd Barry, analonjera onse mwachikondi ndi ndemanga zachidule za kufunika kwa chochitikachi. Albert Schroeder anachititsa phunziro la mlunguwo la Nsanja ya Olonda mwachidule, ndiyeno Daniel Sydlik, analankhula kwa mphindi 15 pamutu wakuti “Utumiki Wathu Wopatulika pa Beteli.” Oyambirira m’programu onseŵa anali a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.
Nkhani ziŵiri zotsatira za programuyo—“Kukwaniritsa Zofunika Zathu za Kufutukula Malo Okhala, 1974—1995,” ndi “Mfundo Zazikulu za Kukonza ndi Kumanga Beteli mu Brooklyn”—zinali ndi mfundo zazikulu za kumanga kapena kupeza nyumba zimene zinapatuliridwazo. Ndemanga zinasumikidwa pa nyumba yokhalamo imene inamalizidwa posachedwapa imene tsopano mukukhala Abeteli pafupifupi chikwi chimodzi. Nyumba imeneyi yautali wa mamita 115 pa 90 Sands Street njogwirizanitsidwa ndi nyumba ya fakitale yosindikizira.
Programu imeneyo inali ndi nkhani ya kupatulira yokambidwa ndi Milton Henschel, pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society. Anagogomezera pa zitsanzo zakale za m’Baibulo za kupereka nyumba zogwiritsira ntchito mu utumiki wa Yehova. Pambuyo pa nyimbo zochitika zonse zinamalizidwa ndi pemphero loperekedwa ndi Carey Barber, nayenso amene ali wa Bungwe Lolamulira. Koma kodi mfundo zina za programuyo zinali zotani?
Nyumbazo Zipatuliridwa
Woyang’anira Nyumba za Beteli, George Couch, anafotokoza kuti nyumba 17 zokhalamo zawonjezeredwa kuyambira pamene nyumba yokhalamo ya Beteli inapatuliridwa mu Brooklyn pa May 2, 1969.a Zimenezi zinali nyumba zomangidwa chatsopano kapena nyumba zogulidwa ndi kukonzedwa. Kupatulira kumeneku kwenikweni kunali kwa nyumba 17 zokhalamo zimenezi, kwa nyumba ziŵiri zazing’ono—zogulidwa m’ma 1940 koma zokonzedwa monga nyumba zokhalamo za Beteli—ndiponso kwa fakitale ndi maofesi amene anamangidwa kapena kugulidwa kuyambira pamene nyumba ya maofesi aakulu a Mboni za Yehova anapatuliridwa pa March 15, 1982.b
Nyumba yaikulu koposa pa nyumba zimene zinapatuliridwa ndiyo ija ya pa 360 Furman Street. Yomangidwa mu 1928, inagulidwa ndi Mboni za Yehova pa March 15, 1983, ndi kukonzedwa yonse. Ili ndi malo okwanira mamita 93,000 monsemonse, kapena pafupifupi ma hekitala 9. Nyumba zina zophatikizidwa pa kupatuliridwako zinali fakitale imene ili pa 175 Pearl Street ndi magalaja aakulu amene anamangidwa m’zaka zaposachedwapa.
Chifukwa Chimene Nyumba Zokhalamo Zowonjezereka Zikufunika
Mu 1969, pamene nyumba yokhalamo yomaliza ya Beteli ya ku Brooklyn inapatuliridwa, panali chiŵerengero chapamwamba cha Mboni 1,336,112 zimene zinali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu dziko lonse lapansi. Koma mu 1995 panali 5,199,895 amene anali kuchita motero, kuŵirikiza kuposa nthaŵi zitatu ndi theka! Motero, kuti ziyendere pamodzi ndi kufunika komakula kwa mabuku ofotokoza Baibulo, banja la Beteli ya ku Brooklyn lakula kuchokera pa anthu okhalamo 1,042 mu 1969 kufika pa oposa 3,360, amene tsopano amakhala mu nyumba 22!
George Couch anafotokoza mmene nyumba zina zofunika zinapezedwera kuyambira mu 1974 mpaka 1995. Kumayambiriro kwa ma 1970, zipinda zingapo za mu Towers Hotel imene inali pafupi zinali kuchitidwa lendi ndi Mboni za Yehova kuti muzikhala banja la Beteli lomakulalo. Mu December 1973, Nathan Knorr, amene anali pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, analembera kalata Ofesi ya Beteli ndi oyang’anira Towers omwe, yonena kuti Sosaite yaganiza ‘zotuluka mu Towers Hotel podzafika October 1, 1974.’
Mbale Couch ananena kuti anadabwa kwambiri chifukwa kunalibenso kwina kumene Abeteli amene ankakhala mu Towers akanakhalako. Oyang’anira Towers nawonso anadabwa kwambiri, popeza ankadalira pa ndalama za lendi za Sosaite kuti apitirize malonda awo. Chotulukapo chake chinali chakuti oyang’anira Towers analimbikitsa Mboni za Yehova kugula hotelayo. “Kuyambira pamene tinakhalirana pafupi mwakhala muli kuwonjezereka,” iwo anatero, “ndipo mufunikira nyumbayi.”
“Njodzala ndi alendi,” linali yankho la oimira Sosaite. “Titaigula tidzafuna kuikamo anthu athu.”
“Tidzakuchotserani onse amene ali m’nyumba imeneyi,” oyang’anira Towers analonjeza motero. Eya, posapita nthaŵi pambuyo pake Mboni za Yehova zinagula nyumba ya Towers pamtengo wabwino. “Kodi nchifukwa ninji Mbale Knorr analemba kalata imeneyo?” Couch anafunsa omvetsera ake ochititsidwa chidwi. “Mwinamwake nayenso sanadziŵe, koma zimenezo nzimene zinachititsa Towers Hotel kugulitsidwa ku Watch Tower Society.”
Mlankhuliyo anafotokozanso mmene Mboni za Yehova zinagulira 97 Columbia Heights, malo akale a Margaret Hotel yotchukayo, kungodutsa msewu wochokera ku Nyumba ya Beteli yoyamba. Malo ake ngabwino, popeza akhoza kulumikizidwa ku nyumba ya Beteli mosavuta ndi njira yapansi pa msewu. Mu February 1980, pamene nyumbayo inali mkati mwa kukonzedwanso, inapsa. Ndiyeno, chifukwa chakuti mwini wake zinamvuta kumangapo nyumba yatsopano, anagulitsa malowo kwa Mboni za Yehova.
Mbale Couch anati: “Kwenikweni iliyonse ya nyumba zimenezi ili ndi mbiri yokondweretsa imene ikusonya pa chinthu chimodzi—kuti Yehova Mulungu ndiye amene anatsogolera gulu loonekali kupeza nyumba iliyonse.”
Mbiri ya 90 Sands
Nyumba yokhalamo yatsopano kwambiri ndipo yaikulu koposa ndiyo 90 Sands Street. Pamene malowo anagulidwa ndi Mboni za Yehova mu December 1986, anali ndi fakitale yaikulu pa 160 Jay Street.c Fakitaleyo inapasulidwa, ndipo pa August 30, 1990, banja la Beteli linauzidwa kuti chilolezo chinaperekedwa kuti amange nyumba yokhalamo pamalowo yokhala ndi zipinda 30 zosanja.
Pakufunsa kumene kunachitidwa ndi wa Bungwe Lolamulira Theodore Jaracz, woyang’anira fakitale ya ku Brooklyn ya Sosaite, Max Larson, anafotokoza mmene chilolezo chinaperekedwera cha kumanga nyumba yokhalamo ya 90 Sands Street. Zimene zinachitika kalelo mu 1965, Mbale Larson anafotokoza motero, zinali zovutadi.
Kalelo panthaŵiyo Sosaite inali kufuna kumanga fakitale ya zipinda khumi zosanja pamalo oyandikana ndi mafakitale ake ena, koma magaŵidwe a malowo mwalamulo anangolola kumangapo nyumba ya zipinda ziŵiri zosanja. Wodziŵa za mapulani a nyumba anavomera kukonza pulani ya fakitale yatsopanoyo imene inafunikira kumangidwa, koma iye anati: “Sindifuna kudzichititsa manyazi mwa kukaipereka ku bungwe lake loyang’anira.” Anali wotsimikizira kuti Bungwe la Miyezo ndi Mapempho silingasinthe malamulo awo a magaŵidwe a malowo. Pamene pulani ya nyumbayo inaloledwa, anadzuma kuti: “Mwazipeza motani zimenezo m’dziko lino!”
Chifukwa chake, Larson anapitiriza motero, chinali chakuti pamene malowo anagaŵidwanso mwalamulo kaamba ka fakitale yathu ya zipinda khumi zosanja, malo oyandikana nawo nawonso anagaŵidwanso, kuphatikizapo pamene pali nyumba ya pa 160 Jay Street. Ndipo, modabwitsa, kugaŵidwako kunalola kumangapo hotela. Koma, Larson anati, chinali chinthu chimene anthu sanachidziŵe konse—kwenikweni mpaka kudzafika zaka 25 pambuyo pake, titayamba kufunafuna malo oti timangepo nyumba yatsopano ya Beteli. Pamenepo mpamene lamulo la kugaŵidwako linatulukiridwa!
Mbale Larson anafotokoza zimene zinachitika kuti: “Pamene tinakonza pulani ya nyumba yokhalamoyo ya zipinda 30 zosanja ndi kuipereka ku dipatimenti ya kumanga nyumba, tinauzidwa kuti: ‘Simungakhale ndi nyumba yokhalamo pamalo amenewo. Ponsepo ndi pamalo a mafakitale, ndipo sangakusinthireni.’
“‘Safunikira kusintha,’ tinauza akuluakuluwo. ‘Anagaŵidwa kale kaamba ka hotela.’ Pamene anayang’ana m’zolembedwa, anadabwa kwambiri! Eya, ndimo mmene tinapezera nyumba yathu ya zipinda 30 zosanja,” Larson anamaliza motero.
Dalitso la Yehova Liwonekeratu
Wamasalmo wa Baibulo analemba kuti: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.” (Salmo 127:1) Mwachionekere, dalitso la Yehova lakhala pantchito ya kumanga ya Mboni za Yehova kuti zichite ntchito yapadziko lonse ya kulalikira ndi kuphunzitsa imene Yesu anauza otsatira ake kuti aichite.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Awo amene anali ndi mwaŵi wa kumvetsera programuyo pa September 18, 1995, anasangalala kwambiri ndi umboni wa dalitso lotere pa chifutukuko kumalikulu adziko lonse a atumiki a Yehova. Anthu a Yehova ali otsimikizira za madalitso ake opitiriza pamene akupitiriza kuchita zimene akulamula.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda yachingelezi, June 15, 1969, masamba 379-82.
b Nsanja ya Olonda yachingelezi, December 1, 1982, masamba 23-31.
c Galamukani! wachingelezi wa December 22, 1987, masamba 16-18.
[Chithunzi patsamba 23]
90 Sands St. • 1995
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
Nyumba zina zokhalamo zimene zinapatuliridwa
97 Columbia Hts. • 1986
Bossert Hotel, 98 Montague St. • 1983
34 Orange St. • 1945
Standish Hotel, 169 Columbia Hts. • 1981
67 Livingston St. • 1989
108 Joralemon St. • 1988
Towers Hotel, 79-99 Willow St. • 1975
[Zithunzi patsamba 26]
175 Pearl St. • 1983
69 Adams St. • 1991
360 Furman St. • 1983