Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 9/15 tsamba 2-7
  • Kodi Zipembedzo Zonse Zimakondweretsa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zipembedzo Zonse Zimakondweretsa Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Azindikiridwa ndi Zipatso Zawo
  • Kufunika kwa Kusamala
  • Santhulani Zipatso Zake
  • Nthaŵi ya Kuchitapo Kanthu Motsimikizira
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
    Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 9/15 tsamba 2-7

Kodi Zipembedzo Zonse Zimakondweretsa Mulungu?

Kodi mumalingalira kuti zipembedzo zonse zimakondweretsa Mulungu? Mwinamwake mtundu uliwonse wa kulambira umene mumadziŵa umalimbikitsa khalidwe labwino, m’njira ina. Koma kodi zofunika ndi zokhazo kuti Mulungu akondwere?

ENA amati, ‘Ingokhala woona mtima pa kulambira kwako, ndipo Mulungu adzakondwera. M’zipembedzo zonse muli zabwino.’ Mwachitsanzo, chipembedzo cha Bahai Faith chatenga lingaliro limeneli kwakuti pa zikhulupiriro zawo awonjezerapo zipembedzo zazikulu zisanu ndi zinayi za m’dziko. Gulu lachipembedzo limeneli limakhulupirira kuti zonsezi zinachokera kwa Mulungu ndipo zili mbali za choonadi chimodzi. Kodi zimenezi zingakhale bwanji choncho?

Ndiponso, muyeneradi kudabwa mmene chipembedzo chimakondweretsera Mulungu pamene chimalamula anthu ake kuika gasi yakupha m’malo a anthu onse, imene ikhoza kupha anthu ambiri. Gulu lina lachipembedzo ku Japan linapatsidwa mlandu umenewo. Kapena kodi Mulungu amakondwera ndi chipembedzo chimene chimachititsa anthu ake kudzipha? Zaka zingapo zapitazo, zimenezo zinachitika kwa otsatira mtsogoleri wachipembedzo Jim Jones.

Tikayang’ana kumbuyo m’nthaŵi zakale, tingafunsenso kuti, Kodi zipembedzo zingakondweretse Mulungu pamene zimasonkhezera nkhondo, monga Nkhondo Yazaka Makumi Atatu, imene inamenyedwa kuyambira mu 1618 mpaka mu 1648? Malinga ndi kunena kwa The Universal History of the World, nkhondo yachipembedzo imeneyo pakati pa Akatolika ndi Aprotesitanti inali “imodzi ya nkhondo zoipa koposa m’mbiri ya Europe.”

Nkhondo za Mtanda zachipembedzo kuyambira mu zaka za zana la 11 mpaka mu zaka za zana la 13 zinachititsanso kukhetsa mwazi koipitsitsa. Mwachitsanzo, m’Nkhondo ya Mtanda yoyamba, omenya nkhondoyo otchedwa Akristu anapha mwankhanza Asilamu ndi Ayuda okhala mu Yerusalemu.

Talingaliraninso za zimene zinachitika mkati mwa Inquisition, imene inayamba mu zaka za zana la 13 ndi kutha zaka pafupifupi 600. Anthu zikwi zambiri anazunzidwa ndi kutenthedwa mpaka imfa molamulidwa ndi atsogoleri achipembedzo. M’buku lake lakuti Vicars of Christ​—The Dark Side of the Papacy, Peter De Rosa akunena kuti: “M’dzina la papa, [a m’bwalo la inquisition] ndiwo anali ndi mlandu wa kuwononga mkhalidwe waumunthu mwankhanza yoipitsitsa ndipo kwa nthaŵi yaitali m’mbiri ya fuko [la anthu].” Ponena za wa m’bwalo la inquisition Torquemada, Mdominikani wa ku Spain, De Rosa akuti: “Anaikidwapo mu 1483 ndipo analamulira mwankhanza kwa zaka khumi ndi zisanu. Anthu amene anazunza anafika 114,000 mwa amene 10,220 a iwo anatenthedwa.”

Zoona, si zipembedzo za Dziko Lachikristu zokha zimene zili ndi liwongo la mwazi. M’buku lake lakuti Pensées, wafilosofi wa ku France, Blaise Pascal, anati: “Anthu samachita zinthu zoipa kwambiri ndipo mokondwera monga mmene amazichitira atasonkhezeredwa ndi chikhulupiriro cha chipembedzo.”

Azindikiridwa ndi Zipatso Zawo

Kwa Mulungu, kuvomerezedwa kwa chipembedzo sikumazikidwa pa chinthu chimodzi chokha. Kuti chipembedzo chikhale chovomerezeka kwa iye, ziphunzitso ndi ntchito zake ziyenera kugwirizana ndi Mawu ake olembedwa a choonadi, Baibulo. (Salmo 119:160; Yohane 17:17) Zipatso za kulambira kovomerezedwa ndi Mulungu ziyenera kugwirizana ndi miyezo ya Yehova Mulungu.

Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu Kristu anasonyeza kuti kudzakhala aneneri amene monyenga adzati akuimira Mulungu. Yesu anati: “Yang’anirani mupeŵe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.” (Mateyu 7:15-20) Mawu ameneŵa amasonyeza kuti tiyenera kukhala tchire mwauzimu. Tingaganize kuti mtsogoleri wachipembedzo kapena gulu lachipembedzo lili lovomerezeka kwa Mulungu ndi Kristu, koma tingakhale titaphonya.

Kufunika kwa Kusamala

Ngakhale kuti chipembedzo chimati nchovomerezedwa ndi Mulungu ndipo atumiki ake amaŵerenga ndime za m’Baibulo, zimenezo sizimatanthauza kuti mtundu wake wa kulambira umakondweretsa Mulungu. Mwinamwake atsogoleri ake angachite zinthu zodabwitsa zimene zimachichititsa kuoneka monga kuti Mulungu akuchigwiritsira ntchito. Ngakhale zili choncho, chipembedzocho chingakhalebe chonyenga, chosapatsa zipatso zovomerezeka kwa Mulungu. Ansembe amatsenga achiaigupto a m’tsiku la Mose ankatha kuchita zinthu zodabwitsa, koma iwo analibiretu chiyanjo cha Mulungu.​—Eksodo 7:8-22.

Lerolino monga kale, zipembedzo zambiri zimachirikiza malingaliro ndi nzeru za anthu m’malo momamatira ku chimene Mulungu amanena kuti ndicho choonadi. Chotero, chenjezo la Baibulo lili loyenerera kwambiri: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”​—Akolose 2:8.

Atanena za zipatso zabwino ndi zoipa, Yesu anati: “Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu ufumu wakumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wakumwamba. Ambiri adzati kwa ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”​—Mateyu 7:21-23.

Santhulani Zipatso Zake

Motero, nzomveka kuti nkofunika kuyang’ana zipatso za chipembedzo musanagamule kuti nchovomerezeka kwa Mulungu. Mwachitsanzo, kodi chipembedzocho chimaloŵa m’ndale? Ndiyeno onani mawu olembedwa pa Yakobo 4:4: “Iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” Ndiponso, ponena za otsatira ake oona Yesu anati: “Siali a dziko lapansi monga ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Chipembedzo chimene chili chabwino m’maso mwa Mulungu sichimaloŵa m’ndale za dzikoli, limene “ligona mwa woipayo,” cholengedwa chauzimu chosaonekacho Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) M’malo mwake, chipembedzo chimene Mulungu amayanja chimachirikiza mokhulupirika Ufumu wake umene uli m’manja mwa Yesu Kristu ndipo chimalengeza uthenga wabwino wonena za boma lakumwambalo.​—Marko 13:10.

Kodi chipembedzo chimakhala chovomerezeka kwa Mulungu ngati chimasonkhezera kukana malamulo a boma? Yankho nlodziŵikiratu ngati tilabadira uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino.” (Tito 3:1) Inde, Yesu anasonyeza kuti otsatira ake ayenera ‘kupereka zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.’​—Marko 12:17.

Nanga bwanji ngati chipembedzo chimalimbikitsa kutengamo mbali m’nkhondo za mitundu. Petro Woyamba 3:11 amatilimbikitsa ‘kuchita chabwino’ ndi ‘kufunafuna mtendere ndi kuulondola.’ Kodi chipembedzo chingakondweretse Mulungu motani ngati anthu ake ali ofunitsitsa kupha alambiri anzawo a m’dziko lina m’nkhondo? Anthu a m’chipembedzo chimene chili ndi chiyanjo cha Mulungu amasonyeza mkhalidwe wake waukulu​—chikondi. Ndipo Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Chikondi chimenecho sichingagwirizane ndi udani wachiwawa wosonkhezeredwa m’nkhondo za mitundu.

Chipembedzo choona chimasintha anthu okonda nkhondo kukhala okonda mtendere. Zimenezi zinanenedweratu m’mawu awa: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) M’malo motulutsa mawu achidani, awo amene amachita kulambira koona amatsatira lamulo lakuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.”​—Mateyu 22:39.

Awo amene amachita kulambira koona amalimbikira kutsatira miyezo yapamwamba ya Yehova Mulungu, akumakana kutengera moyo wamakhalidwe oipa. Mawu a Mulungu amanena kuti: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa mzimu wa Mulungu wathu.”​—1 Akorinto 6:9-11.

Nthaŵi ya Kuchitapo Kanthu Motsimikizira

Nkofunika kuzindikira kusiyana pakati pa kulambira konyenga ndi chipembedzo choona. M’buku la Baibulo la Chivumbulutso, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga umatchedwa “Babulo Wamkulu,” mkazi wachigololo wophiphiritsira “amene mafumu a dziko anachita chigololo naye.” Ali ndi liwongo la mwazi ndipo akugwira chikho chagolidi “chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake.” (Chivumbulutso 17:1-6) Palibe chimene Mulungu amavomereza ponena za iye.

Ino ndiyo nthaŵi ya kuchitapo kanthu motsimikizira. Kwa anthu oona mtima amene akali m’Babulo Wamkulu, Mlengi wathu wachikondi akupereka chiitano ichi: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.”​—Chivumbulutso 18:4.

Ngati mumafuna kupembedza m’njira imene imakondweretsa Mulungu, bwanji osadziŵana kwambiri ndi Mboni za Yehova? Tchati cha m’nkhaniyi chandondomeka zina za zikhulupiriro zawo, pamodzi ndi zifukwa zake za m’Malemba. Onani m’Baibulo lanu ngati zikhulupiriro za Mboni zimagwirizana ndi Mawu a Mulungu. Fufuzani kuti mudziŵe ngati chipembedzo chawo chimatulutsa mtundu wa zipatso zimene mungayembekezere kutuluka pa kulambira koona. Ngati mwapeza kuti chimatero, mudzakhala mutapeza chipembedzo chimene chimakondweretsa Mulungu.

[Bokosi patsamba 5]

ZIMENE MBONI ZA YEHOVA ZIMAKHULUPIRIRA

CHIKHULUPIRIRO MAZIKO A M’BAIBULO

Dzina la Mulungu ndi Yehova Eksodo 6:3; Salmo 83:18

Baibulo ndi Mawu a Mulungu Yohane 17:17; 2 Timoteo 3:16, 17

Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu Mateyu 3:16, 17; Yohane 14:28

Mtundu wa anthu sunasinthike Genesis 1:27; 2:7

koma unalengedwa

Imfa ya anthu ili chifukwa cha Aroma 5:12

uchimo wa munthu woyamba

Sou imaleka kukhalako pa imfa Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4, NW

Helo ndi manda a anthu onse Yobu 14:13; Chivumbulutso 20:13,

King James Version

Chiukiriro ndicho chiyembekezo Yohane 5:28, 29; 11:25;

cha akufa Machitidwe 24:15

Kristu anapereka moyo wake Mateyu 20:28; 1 Petro 2:24;

wa padziko lapansi monga 1 Yohane 2:1, 2

dipo la anthu omvera

Mapemphero ayenera kuperekedwa Mateyu 6:9; Yohane 14:6, 13, 14

kwa Yehova yekha kudzera

mwa Kristu

Malamulo a Baibulo a makhalidwe 1 Akorinto 6:9, 10

abwino ayenera kumvedwa

Mafano sayenera kugwiritsiridwa Eksodo 20:4-6; 1 Akorinto 10:14

ntchito pa kulambira

Tiyenera kupeŵa kukhulupirira Deuteronomo 18:10-12;

mizimu Agalatiya 5:19-21

Mwazi suyenera kuikidwa m’thupi Genesis 9:3, 4;

la munthu Machitidwe 15:28, 29

Otsatira Yesu oona Yohane 15:19; 17:16;

amadzilekanitsa ndi dziko Yakobo 1:27; 4:4

Akristu amachitira umboni, Yesaya 43:10-12;

kulengeza uthenga wabwino Mateyu 24:14; 28:19, 20

Ubatizo mwa kumiza m’madzi Marko 1:9, 10; Yohane 3:22;

kotheratu umasonyeza Machitidwe 19:4, 5

kudzipatulira kwa Mulungu

Maina aulemu achipembedzo Yobu 32:21, 22; Mateyu 23:8-12

si a m’Malemba

Tikukhala mu “nthaŵi ya Danieli 12:4; Mateyu 24:3-14;

chimaliziro” 2 Timoteo 3:1-5

Kukhalapo kwa Kristu nkosaoneka Mateyu 24:3; Yohane 14:19;

1 Petro 3:18

Satana ndiye wolamulira Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19

wosaoneka wa dziko lino

Mulungu adzawononga dongosolo Danieli 2:44;

loipa lilipoli la zinthu Chivumbulutso 16:14, 16;18:1-8

Ufumu wa Mulungu pansi pa Yesaya 9:6, 7; Danieli 7:13, 14;

Kristu udzalamulira Mateyu 6:10

dziko lapansi m’chilungamo

“Kagulu ka nkhosa” kadzalamulira Luka 12:32;

ndi Kristu kumwamba Chivumbulutso 14:1-4; 20:4

Enanso amene Mulungu amayanja Luka 23:43; Yohane 3:16;

adzalandira moyo wosatha Chivumbulutso 21: 1-4

padziko lapansi la paradaiso

[Chithunzi patsamba 4]

Anthu zikwi zambiri anaphedwa mkati mwa Inquisition

[Chithunzi patsamba 6]

Nkhondo za Mtanda zinachititsa kukhetsa mwazi koipitsitsa

[Chithunzi patsamba 7]

Chipembedzo choona chimadziŵika ndi zipatso zake zabwino

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Cover: Garo Nalbandian

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena