Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 9/15 tsamba 10-15
  • Onse Ayenera Kudziŵerengera Mlandu kwa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Onse Ayenera Kudziŵerengera Mlandu kwa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Angelo Ngofunikira Kudziŵerengera Mlandu
  • Mwana wa Mulungu Ngofunikira Kudziŵerengera Mlandu
  • Kudziŵerengera Mlandu Monga Mitundu
  • Zitsanzo za Kudziŵerengera Mlandu Kwaumwini
  • Kudziŵerengera Mlandu mu Mpingo Wachikristu
  • Yehova Aŵerengeretu Bwino Mlandu Wanu
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Mzimu Wochirikiza Dongosolo Lakale Liripo’li
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Akristu Amafunika Kuthandizana
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 9/15 tsamba 10-15

Onse Ayenera Kudziŵerengera Mlandu kwa Mulungu

“Aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.” ​—AROMA 14:12.

1. Kodi ndi malire otani amene anaikidwa pa ufulu wa Adamu ndi Hava?

YEHOVA MULUNGU analenga makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, monga anthu okhoza kudzisankhira. Ngakhale kuti anali ochepsedwa pang’ono ndi angelo, iwo anali zolengedwa zanzeru zokhoza kupanga zosankha zanzeru. (Salmo 8:4, 5, NW) Komabe, ufulu wopatsidwa ndi Mulungu umenewo sunali chilolezo cha kudzisankhira mosayang’aniridwa. Anali ndi mlandu kwa Mlengi wawo, ndipo kukhala kwawo ndi mlandu kumeneku kwafutukukira kwa mbadwa zawo zonse.

2. Kodi Yehova adzaŵerengera mlandu wotani posachedwapa, ndipo chifukwa ninji?

2 Tsopano popeza kuti tikuyandikira pachimake cha dongosolo ili loipa la zinthu, Yehova adzaŵerenga mlandu pa dziko lapansi. (Yerekezerani ndi Aroma 9:28.) Posachedwapa, anthu osapembedza adzafunikira kudziŵerengera mlandu kwa Yehova Mulungu chifukwa cha kusakaza chuma cha dziko lapansi, kuwononga moyo wa munthu, ndipo makamaka kaamba ka chizunzo cha atumiki ake.​—Chivumbulutso 6:10; 11:18.

3. Kodi ndi mafunso otani amene tidzakambitsirana?

3 Pokhala titayang’anizana ndi chiyembekezo chochititsa kuganiza kwambiri chimenechi, nkopindulitsa kwa ife kulingalira za zochita za Yehova zolungama ndi zolengedwa zake m’nthaŵi zakale. Kodi Malemba angatithandize motani, kumbali yathu, kudziŵerengera mlandu movomerezeka kwa Mlengi wathu? Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zingakhale zothandiza, ndipo tiyenera kupeŵa kutsanzira ziti?

Angelo Ngofunikira Kudziŵerengera Mlandu

4. Kodi timadziŵa motani kuti Mulungu amaŵerengera mlandu angelo kaamba ka zochita zawo?

4 Zolengedwa zaungelo za Yehova kumwamba nazonso nzofunikira kudziŵerengera mlandu kwa iye monga momwe ife tilili. Chigumula cha tsiku la Nowa chisanadze, angelo ena mosamvera anavala matupi a anthu kuti agonane ndi akazi. Monga zolengedwa zokhoza kudzisankhira, zolengedwa zauzimu zimenezi zinatha kupanga chosankha chimenechi, koma Mulungu anaziŵerengera mlandu. Pamene angelo osamverawo anabwerera ku malo amizimu, Yehova sanawalole kubwerera m’malo mwawo. Wophunzira Yuda amatiuza kuti iwo “adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.”​—Yuda 6.

5. Kodi Satana ndi ziŵanda zake wakumana ndi kugwa kotani, ndipo kodi mlandu wa chipanduko chawo udzathetsedwa motani?

5 Angelo osamvera ameneŵa, kapena ziŵanda, ali ndi Satana Mdyerekezi monga wolamulira wawo. (Mateyu 12:24-26) Mngelo woipa ameneyu anapandukira Mlengi wake nakayikira kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova. Satana anatsogolera makolo athu oyamba kuloŵa mu uchimo, ndipo potsirizira pake zimenezi zinachititsa imfa yawo. (Genesis 3:1-7, 17-19) Ngakhale kuti Yehova analola Satana kuloŵa kumabwalo akumwamba kwa nthaŵi ina pambuyo pa zimenezo, buku la Baibulo la Chivumbulutso linaneneratu kuti panthaŵi ya Mulungu yokwanira, woipa ameneyu adzagwetsedwa pansi ku dziko. Umboni ukusonyeza kuti zimenezi zinachitika Yesu Kristu atangolandira mphamvu ya Ufumu mu 1914. Potsirizira pake, Mdyerekezi ndi ziŵanda zake adzaloŵa m’chiwonongeko chosatha. Pokhala nkhani ya ulamuliro itatha, pamenepo mlandu wa chipandukowo udzakhala utathetsedwa molungama.​—Yobu 1:6-12; 2:1-7; Chivumbulutso 12:7-9; 20:10.

Mwana wa Mulungu Ngofunikira Kudziŵerengera Mlandu

6. Kodi Yesu amaona motani kudziŵerengera mlandu kwake kwa Atate wake?

6 Nchitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga chimene chaperekedwa ndi Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu! Monga munthu wangwiro wolingana ndi Adamu, Yesu anakondwera kuchita chifuniro cha Mulungu. Anali wokondweranso kudziŵerengera mlandu wa kuchita mogwirizana ndi lamulo la Yehova. Ponena za iye, wamasalmo moyenerera analosera kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali mkati mwa mtima mwanga.”​—Salmo 40:8; Ahebri 10:6-9.

7. Popemphera tsiku limodzi imfa yake isanachitike, kodi nchifukwa ninji Yesu anatha kunena mawu olembedwa pa Yohane 17:4, 5?

7 Ngakhale kuti Yesu anakumana ndi chitsutso cha njiru, anachita chifuniro cha Mulungu ndi kusunga umphumphu kufikira imfa ya pamtengo wozunzirapo. Mwa kutero iye anapereka mtengo wa dipo loombolera anthu pa zotulukapo zakupha za uchimo wa Adamu. (Mateyu 20:28) Motero, tsiku limodzi imfa yake isanachitike, Yesu anatha kupemphera mwachidaliro kuti: “Ine ndalemekeza inu padziko lapansi, mmene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite. Ndipo tsopano, Atate inu, lemekezani ine ndi inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nawo ndi inu lisanakhale dziko lapansi.” (Yohane 17:4, 5) Yesu anatha kunena mawu amenewo kwa Atate wake wakumwamba chifukwa chakuti anali kupambana pa chiyeso cha kudziŵerengera mlandu ndipo anali wovomerezeka kwa Mulungu.

8. (a) Kodi Paulo anasonyeza motani kuti tiyenera kudziŵerengera mlandu kwa Yehova Mulungu? (b) Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupeza chivomerezo cha Mulungu?

8 Mosiyana ndi munthu wangwiroyo Yesu Kristu, ife ndife opanda ungwiro. Komabe, tili ofunikira kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu. Mtumwi Paulo anati: “Uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira ku mpando wakuweruza wa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati [Yehova, NW], mabondo onse adzagwadira ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu. Chotero munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:10-12) Kuti tichite motero ndi kuvomerezedwa ndi Yehova, iyeyo mwachikondi watipatsa zonse ziŵiri chikumbumtima ndi Mawu ake ouziridwa, Baibulo, kuti zititsogolere pa zimene tikunena ndi kuchita. (Aroma 2:14, 15; 2 Timoteo 3:16, 17) Kugwiritsira ntchito mokwanira zogaŵira zonse zauzimu za Yehova ndi kutsatira chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo kudzatithandiza kupeza chivomerezo kwa Mulungu. (Mateyu 24:45-47) Mzimu woyera wa Yehova, kapena mphamvu yogwira ntchito, ndiwo magwero enanso a nyonga ndi chitsogozo. Ngati tichita mogwirizana ndi chitsogozo cha mzimu ndi kutsogoleredwa ndi chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo, timasonyeza kuti ‘sitimataya Mulungu,’ kwa amene tidzadziŵerengerako mlandu wa zochita zathu zonse.​—1 Atesalonika 4:3-8; 1 Petro 3:16, 21.

Kudziŵerengera Mlandu Monga Mitundu

9. Kodi Aedomu anali ayani, ndipo nchiyani chimene chinawachitikira chifukwa cha mchitidwe wawo kwa Israyeli?

9 Yehova amaŵerengera mlandu mitundu. (Yeremiya 25:12-14; Zefaniya 3:6, 7) Lingalirani za ufumu wakale wa Edomu, wokhala kummwera kwa Nyanja Yakufa ndi kumpoto kwa Gulf of Aqaba. Aedomu anali mtundu wachisemu, wokhala pachibale chapafupi ndi Aisrayeli. Ngakhale kuti kholo la Aedomu linali Esau mdzukulu wa Abrahamu, anakaniza Aisrayeli kudutsa mu Edomu mu “msewu wachifumu” pamene anali paulendo kumka ku Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 20:14-21) M’zaka mazana ambiri udani wa Edomu unakula kukhala udani wouma mtima pa Israyeli. Potsirizira pake Aedomu anafunikira kudziŵerengera mlandu chifukwa cha kulimbikitsa kwawo Ababulo kuwononga Yerusalemu mu 607 B.C.E. (Salmo 137:7) M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., magulu ankhondo a Ababulo motsogoleredwa ndi Mfumu Nabonidus anagonjetsa Edomu, ndipo anakhala bwinja, monga momwe Yehova analamulirira.​—Yeremiya 49:20; Obadiya 9-11.

10. Kodi Amoabu anachita motani kwa Aisrayeli, ndipo Mulungu anaimba mlandu Moabu motani?

10 Nayenso Moabu sizinamuyendere bwino. Ufumu wachimoabu unali kumpoto kwa Edomu ndi kummaŵa kwa Nyanja Yakufa. Aisrayeli asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Amoabu anawachitira chipongwe, akumawapatsa mkate ndi madzi kokha kaamba ka kupeza phindu la ndalama monga momwe umboni umasonyezera. (Deuteronomo 23:3, 4) Mfumu Balaki ya Amoabu inalemba ganyu mneneri Balamu kuti atemberere Israyeli, ndipo akazi achimoabu anagwiritsiridwa ntchito kukolera amuna achiisrayeli kuchita chigololo ndi kulambira mafano. (Numeri 22:2-8; 25:1-9) Komabe, Yehova sanalekerere udani wa Moabu pa Israyeli. Monga momwe analoserera, Moabu anapasulidwa ndi Ababulo. (Yeremiya 9:25, 26; Zefaniya 2:8-11) Inde, Mulungu anaŵerengera mlandu Moabu.

11. Kodi Moabu ndi Amoni anakhala ngati mizinda iti, ndipo maulosi a Baibulo amasonyezanji ponena za dongosolo la zinthu loipa lilipoli?

11 Si Moabu yekha amene anafunikira kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu komanso Amoni. Yehova anali ataneneratu kuti: “Zedi Moabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha.” (Zefaniya 2:9) Maiko a Moabu ndi Amoni anapasulidwa, monga momwedi Mulungu anawonongera mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Malinga ndi kunena kwa Geological Society of London, ofufuza akunena kuti apeza malo a mabwinja a Sodomu ndi Gomora kugombe la kummaŵa kwa Nyanja Yakufa. Umboni wina uliwonse umene uti udzapezeke pa nkhaniyi udzangochirikiza maulosi a Baibulo osonyeza kuti dongosolo la zinthu loipa lilipoli lidzadziŵerengeranso mlandu kwa Yehova Mulungu.​—2 Petro 3:6-12.

12. Ngakhale kuti Israyeli anafunikira kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu kaamba ka machimo ake, kodi nchiyani chimene chinanenedweratu ponena za Ayuda otsalira?

12 Ngakhale kuti Israyeli anayanjidwa kwambiri ndi Yehova, anafunikira kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu kaamba ka machimo ake. Pamene Yesu Kristu anadza ku mtundu wa Israyeli, ambiri anamkana. Otsalira ake okha ndiwo amene anamkhulupirira nakhala otsatira ake. Paulo anagwiritsira ntchito maulosi ena kwa otsalira achiyuda ameneŵa pamene analemba kuti: “Yesaya afuula za Israyeli, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israyeli ukhala monga mchenga wakunyanja, [otsalira ndiwo adzapulumuka, NW]. Pakuti [Yehova adzaŵerengera mlandu, NW] padziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule. Ndipo monga Yesaya anati kale, Ngati [Yehova, NW] wa makamu akumwamba sanatisiyira ife mbewu, tikadakhala monga Sodoma, ndipo tikadafanana ndi Gomora.” (Aroma 9:27-29; Yesaya 1:9; 10:22, 23) Mtumwiyo anatchula chitsanzo cha amuna 7,000 mu nthaŵi ya Eliya amene sanagwadire Baala, ndiyeno anati: “Choteronso nthaŵi yatsopano [alipo otsalira, NW] monga mwa kusankha kwa chisomo.” (Aroma 11:5) Otsalira amenewo anapangidwa ndi anthu amene anafunikira kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu.

Zitsanzo za Kudziŵerengera Mlandu Kwaumwini

13. Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa Kaini pamene Mulungu anamuŵerengera mlandu wa kupha mbale wake Abele?

13 Baibulo limatchula za anthu ambiri amene anadziŵerengera mlandu kwa Yehova Mulungu mwaumwini. Mwachitsanzo, tiyeni tinene za Kaini, mwana woyamba wa Adamu. Iye ndi mphwake yemwe Abele anapereka nsembe kwa Yehova. Nsembe ya Abele inalandiridwa ndi Mulungu, koma ya Kaini sinatero. Pamene anaŵerengeredwa mlandu wa kupha mbale wake mwankhanza, Kaini mokakala mtima anauza Mulungu kuti: “Kodi ndine woyang’anira mphwanga?” Chifukwa cha uchimo wakewo, Kaini anapitikitsidwira ku “dziko la Nodi, kummaŵa kwake kwa Edene.” Sanasonyeze kulapa koona pa upandu wake, anangochita chisoni kokha ndi chilango chake choperekedwa molungamacho.​—Genesis 4:3-16.

14. Kodi kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu kunasonyezedwa motani mu nkhani ya Eli ndi ana ake?

14 Kudziŵerengera mlandu kwa munthu kwa Mulungu kwasonyezedwanso mu nkhani ya mkulu wa ansembe wa Israyeli Eli. Ana ake aamuna, Hofeni ndi Pinehasi, anatumikira monga ochita unsembe koma “anali ndi mlandu wa kuchitira anthu mopanda chilungamo, ndi wa kusawopa Mulungu, ndipo anachita choipa chilichonse,” amatero wolemba mbiri Josephus. Anthu “oipa” ameneŵa sanadziŵe Yehova, anachita khalidwe lachipongwe chachikulu, ndipo anali ndi mlandu wa makhalidwe achisembwere oipitsitsa. (1 Samueli 1:3; 2:12-17, 22-25) Monga atate wawo ndi mkulu wa ansembe wa Israyeli, Eli anali ndi thayo la kuwalanga, koma iyeyo anangowadzudzula moziya. Eli ‘anapitiriza kuchitira ana ake ulemu koposa Yehova.’ (1 Samueli 2:29) Nyumba ya Eli inalandira chilango. Ana ake aŵiri onsewo anafa patsiku limodzimodzilo ndi atate wawo, ndipo mzera wawo waunsembe potsirizira pake unadukiratu. Motero mlanduwo unatha.​—1 Samueli 3:13, 14; 4:11, 17, 18.

15. Kodi nchifukwa ninji Jonatani mwana wa Mfumu Sauli anafupidwa?

15 Chitsanzo chosiyana kwambiri ndi zimenezo chinaperekedwa ndi ndi Jonatani mwana wa Mfumu Sauli. Davide atangopha kumene Goliati, “mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide,” ndipo anachita pangano la ubwenzi. (1 Samueli 18:1, 3) Mwinamwake, Jonatani anazindikira kuti mzimu wa Mulungu unali utasiya Sauli, koma changu chake pa kulambira koona sichinazimiririke. (1 Samueli 16:14) Kuzindikira kwa Jonatani za ulamuliro wa Davide woperekedwa ndi Mulungu sikunagwedezeke. Jonatani anazindikira za kudziŵerengera kwake mlandu kwa Mulungu, ndipo Yehova anamfupa chifukwa cha njira yake yolungama mwa kuonetsetsa kuti mzera wa banja lake unapitiriza kukhalako m’mibadwomibadwo.​—1 Mbiri 8:33-40.

Kudziŵerengera Mlandu mu Mpingo Wachikristu

16. Kodi Tito anali yani, ndipo nchifukwa ninji tinganene kuti anadziŵerengera bwino mlandu wake kwa Mulungu?

16 Malemba Achigiriki Achikristu amayamikira amuna ndi akazi ambiri amene anadziŵerengera mlandu bwino. Mwachitsanzo, panali Mkristu wachigiriki wotchedwa Tito. Kwalingaliridwa kuti iyeyo anakhala Mkristu mkati mwa ulendo woyamba waumishonale wa Paulo wa ku Kupro. Popeza kuti Ayuda ndi otembenukira kuchiyuda a ku Kupro angakhale anali mu Yerusalemu mkati mwa Pentekoste wa 33 C.E., mwina Chikristu chinafika pachisumbucho mwamsanga pambuyo pake. (Machitidwe 11:19) Ngakhale zili choncho, Tito anakhaladi mmodzi wa antchito anzake okhulupirika a Paulo. Anatsagana ndi Paulo ndi Barnaba pa ulendo wa ku Yerusalemu cha ku ma 49 C.E., pamene nkhani yovuta ya mdulidwe inathetsedwa. Kukhala wosadulidwa kwenikweniko kwa Tito kunapereka mphamvu pa chigomeko cha Paulo chakuti otembenukira ku Chikristu sayenera kukhala pansi pa Chilamulo cha Mose. (Agalatiya 2:1-3) Utumiki wabwino wa Tito umachitiridwa umboni m’Malemba, ndipodi Paulo anamlembera kalata youziridwa. (2 Akorinto 7:6; Tito 1:1-4) Mwachionekere, Tito anapitiriza kudziŵerengera mlandu bwino kwa Mulungu kufikira mapeto a moyo wake wa padziko lapansi.

17. Kodi Timoteo anadziŵerengera mlandu wotani, ndipo kodi chitsanzo chimenechi chingatisonkhezere motani?

17 Timoteo anali munthu winanso wachangu amene anadziŵerengera mlandu wa iye mwini movomerezeka kwa Yehova Mulungu. Ngakhale kuti Timoteo anali ndi mavuto ena m’thupi, anasonyeza “chikhulupiriro chosanyenga” ndipo ‘anatumikira pamodzi ndi Paulo uthenga wabwino.’ Motero mtumwiyo anatha kuuza Akristu anzake ku Filipi kuti: “Ndilibe wina wa mtima womwewo [wa Timoteo], amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona.” (2 Timoteo 1:5; Afilipi 2:20, 22; 1 Timoteo 5:23) Pokhala ndi zophophonya zaumunthu ndi ziyeso zina, nafenso tingathe kukhala ndi chikhulupiriro chosanyenga ndipo tingadziŵerengere mlandu wovomerezeka wa ife eni kwa Mulungu.

18. Kodi Lidiya anali yani, ndipo anasonyeza mzimu wotani?

18 Lidiya anali mkazi wowopa Mulungu amene mwachionekere anadziŵerengera mlandu wake bwino kwa Mulungu. Iyeyo ndi a nyumba yake anali pakati pa anthu oyamba ku Ulaya kulandira Chikristu chifukwa cha ntchito ya Paulo mu Filipi cha ku ma 50 C.E. Pokhala nzika ya ku Tiyatira, mwina Lidiya anali wotembenukira kuchiyuda, komano mwina munali Ayuda oŵerengeka ndipo mwina mu Filipi munalibe sunagoge. Iyeyo ndi akazi ena odzipereka pa kulambira anali kusonkhana m’mbali mwa mtsinje kumene Paulo analankhula kwa iwo. Monga chotulukapo chake, Lidiya anakhala Mkristu ndipo anaumiriza Paulo ndi mabwenzi ake kukhala naye. (Machitidwe 16:12-15) Kuchereza alendo kumene Lidiya anasonyeza kudakali chizindikiro cha Akristu oona.

19. Kodi Dorika anadziŵerengera bwino mlandu wake kwa Mulungu ndi ntchito zabwino zotani?

19 Dorika anali mkazi wina amene anadziŵerengera mlandu wake bwino kwa Yehova Mulungu. Pamene anamwalira, Petro anapita ku Yopa poyankha pempho la ophunzira amene anali kukhala kumeneko. Anthu aŵiri amene anakakumana ndi Petro “anapita naye ku chipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nawo pamodzi.” Dorika anaukitsidwa. Koma kodi tiyenera kumkumbukira kokha chifukwa cha mzimu wake wa kupatsa kwake waukuluwo? Ayi. Iyeyo anali “wophunzira” ndipo anachita nawo ntchito ya kupanga ophunzira. Mofananamo akazi achikristu lerolino ‘ngodzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo.’ Amasangalalanso kukhala ndi phande ndi ena m’kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira.​—Machitidwe 9:36-42; Mateyu 24:14; 28:19, 20.

20. Kodi ndi mafunso otani amene tingadzifunse?

20 Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti mitundu ndi anthu paokha afunikira kudziŵerengera mlandu kwa Ambuye Mfumu Yehova. (Zefaniya 1:7) Ngati tili odzipatulira kwa Mulungu, pamenepo tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimaona motani mwaŵi wanga ndi mathayo opatsidwa ndi Mulungu? Kodi ndi mbiri yotani imene ndikupanga kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu?’

Kodi Mayankho Anu Ngotani?

◻ Kodi mungasonyeze motani kuti angelo ndi Mwana wa Mulungu ngofunikira kudziŵerengera mlandu kwa Yehova?

◻ Kodi pali zitsanzo za m’Baibulo zotani zosonyeza kuti Mulungu amaŵerengera mlandu mitundu?

◻ Kodi Baibulo limanenanji ponena za kudziŵerengera mlandu kwa munthu kwa Mulungu?

◻ Kodi ndi anthu ena ati olembedwa m’Baibulo amene anadziŵerengera bwino mlandu kwa Yehova Mulungu?

[Chithunzi patsamba 10]

Yesu Kristu anadziŵerengera bwino mlandu wake kwa Atate wake wakumwamba

[Chithunzi patsamba 15]

Monga Dorika, lerolino akazi achikristu amadziŵerengera bwino mlandu wawo kwa Yehova Mulungu

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

Imfa ya Abele/​The Doré Bible Illustrations/​Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena