Kodi Nchiyani Chikuchitikira Achinyamata?
UTHENGA wabwino kapena uthenga wachisoni—kodi mukufuna kumva uti choyamba? Atafunsidwa funsoli, ambiri amasankha kumva uthenga wachisoni kaye nchiyembekezo choti adzatsala akuganiza za uthenga wabwino.
Tikafufuza zimene zikuchitikira achinyamata, talingalirani kaye za mkhalidwe womwe ulipowu. Achikulire nthaŵi zambiri amati achinyamata amakono ngosiyana ndi achinyamata akale. Komabe, achinyamata amanyansidwa ndi zonse zonena kuti sakwanitsa makhalidwe a m’zaka zapitazi. Ngakhale zili choncho, openda makhalidwe a anthu mwaluso amavomereza kuti achinyamata amakono ngosiyana.
Kodi Kusiyana Kwake Kuli Pati?
Ngakhale kuti anthu ambiri amakhulupirira kuti achinyamata ayenera kukhala ndi khalidwe labwino, kukhala osamala, ndiponso kulemekeza ena, zomwe zikuchitika nzosiyana kutali ndi malingalirowa. Malinga ndi kufufuza kofalitsidwa m’nyuzipepala ya The Independent ya ku London, achinyamata “ayamba kukhala ndi ‘mzimu watsopano wachipanduko’ wopandukira dziko limene amaliona kuti lalephera kotheratu kuwalamulira.” “Mzimu watsopano wachipanduko” umenewu ukuonekera pa zomwe anapeza zoti ndi achinyamata amakono ochepa lerolino amene amafuna kudziona monga “anzeru ndi osamala.” M’malo mwake, ambiri amadziona monga “oyaluka ndi osatsimikizirika.”
Mwachitsanzo, ku Britain, upandu womwe anauchitira lipoti—wochuluka wochitidwa ndi achinyamata—unawonjezeka nthaŵi khumi kuchokera mu 1950 mpaka mu 1993. Kuwonjezeka kwa kumwa mankhwala osokoneza bongo ndi moŵa nakonso kwakhala chimodzimodzi. Panthaŵi imodzimodziyo, ikutero The Times ya ku London, pafupifupi m’maiko onse otukuka mwakhala “kuwonjezeka kwakukulu kwa makhalidwe osokonezeka chifukwa cha malingaliro oipa a achinyamata chiyambire Nkhondo Yadziko Yachiŵiri.” Malinga nkunena kwa David J. Smith, profesa wa zaupandu, mavuto ameneŵa “sakudziŵika bwino kuti kaya akuyambitsidwa motani ndi umphaŵi kapena kukhupuka.” Zofufuza zikusonyeza kuti pali kusiyana kwakukulu tsopano pakati pa achinyamata ndi achikulire.
Ana ndi achinyamata aang’ono lerolino akukumana ndi zopsinja maganizo zowonjezereka. Kudzipha, kapena kuyesa kudzipha kwafala. Chiŵerengero cha ana ofuna kudzipha osakwanitsa zaka 12 zakubadwa chinaŵirikiza pazaka zosakwanira khumi, inatero Herald ya ku Glasgow, Scotland. Ana aakulupo amachitanso zimenezo atataya mtima. “Kuyesa kudzipha ndiko chotsatirapo choopsa cha mavuto owonjezereka a m’maganizo a achinyamata ndipo mavutowo akuoneka kuti sadzathetsedwa ndi thandizo limene likuperekedwa,” nyuzipepalayo ikutero.
Kodi ndi Mlandu wa Yani?
Achikulire sachedwa kuimba mlandu achinyamata chifukwa cha malingaliro “ampatuko” a achinyamata. Komabe, kunenadi zoona, kodi achikulire sindiwo ali ndi mlandu waukulu pa zimene zikuchitikira achinyamata tsopano? Kuzunza, kulekerera kwa makolo, kusoŵeka kwa anthu achitsanzo chabwino amene achinyamata angadalire, nthaŵi zambiri anena kuti ndizo zochititsa zake. “Kuchita tondovi, malinga ndi chiŵerengero cha anthu, nkofala monga momwe kunalili zaka 30 zapitazo,” akutero Profesa Bwana Michael Rutter, mkulu wa Medical Research Council Child Psychiatry Unit ya ku Britain. “Koma,” iye akuwonjezera motero, “achinyamata ochita tondovi awonjezeka koopsa. . . . Sitingakayikire kuti kuwonongeka kwa mabanja nakonso kwachititsa zimenezi; osati chisudzulo chokha, koma kusagwirizana kosiyanasiyana ndi kukangana kwa achikulire.”
Wofufuza wina akunena kuti achinyamata “akukana makhalidwe akale.” Chifukwa ninji? “Chifukwa chakuti makhalidwe akalewo sangagwire ntchito kwa iwo.” Tiyeni tinene za kusintha kwa malingaliro ponena za makhalidwe a amuna ndi akazi. Asungwana ambiri akutengera malingaliro a amuna a kukhala ankhanza ndi achiwawa, pamene kuli kwakuti anyamata akuyamba kukhala ngati asungwana. Nzosiyana chotani nanga ndi makhalidwe akale!
Koma kodi nchifukwa ninji tikuona kusintha kwakukulu kumeneku tsopano? Ndipo kodi pali uthenga wabwino wotani wa achinyamata lerolino? Kodi angakhale motani ndi tsogolo labwino? Nkhani yathu yotsatira ikufotokoza mayankho a mafunsowa.