Kodi Atsogoleri Onse Achipembedzo Amakhulupirira Zimene Amaphunzitsa?
MKAZI wina mwamuna wake wangomwalira kumene. Wansembe wawo akufotokoza kuti mwamuna wakeyo sanali wabwino woti nkupita kumwamba nthaŵi yomweyo komanso kuti sanali woipa woti nkuponyedwa m’moto wa helo. Chotero, malinga ndi wansembeyo, mwamunayo akuzunzika kufikira atayenerera kupita kumwamba. Mkaziyo akulipira wansembeyo ndalama kuti apempherere mwamuna wakeyo ncholinga choti amasuke mwamsanga kumene akuyeretsedwako. Zimenezi zikumtonthoza mkazi wamasiyeyo poganiza kuti wansembenso amakhulupirira ndi mtima wonse zimene iyenso amakhulupirira.
Kodi mukuganiza kuti mkazi wamasiyeyo angakhumudwe atadziŵa kuti wansembe wawo sakhulupiriradi kuti kumakhala chilango pambuyo pa ifa? Ambiri amadabwa atadziŵa kuti atsogoleri ochuluka achipembedzo sakhulupirira zambiri zimene iwo okha amaphunzitsa. National Catholic Reporter, pofotokoza zomwe inatcha “vuto lalikulu koposa chiwerewere limene alimo atsogoleri achipembedzo,” inati: “Mwa atsogoleri achipembedzo onse, ambiri asiya kukhulupirira kuti Mulungu aliko. Sakhulupiriranso chiphunzitso chakuti munthu adzalandira mphoto kapena chilango ngakhalenso chiukiriro . . . moti kusakhulupirirako kwakhala khalidwe lawo atsogoleri achipembedzo.”
Matchalitchi enanso ali ndi vuto ngati limeneli. Abusa a Church of England atafunsidwa kunapezeka kuti ambiri “sakhulupirira mbali zazikulu za chikhulupiriro choyambirira chachikristu monga kubala kwa namwali, zozizwitsa za Yesu ndi kubweranso kwa mesiya,” inatero Canberra Times ya ku Australia.
Wolemba za chipembedzo George R. Plagenz anafunsa mbusa kuti amatha bwanji kulakatula mawu olengeza zikhulupiriro zawo, amene sawakhulupirira, popanda chikumbumtima chake kumtsutsa. Mbusa wina anatero kuti amangosintha mawu ake oyamba akuti, “Ndimakhulupirira.” Anati: “Ndimayamba mawuwo olengeza zikhulupiriro zathu mwa kunena kuti, ‘AMAKHULUPIRIRA Mulungu Atate Wamphamvuyonse . . . ’” Plagenz anati chimenecho ndi “chinyengo chachikulu koposa m’dzikoli.”
Chisoni chake nchakuti kupanda chikhulupiriro kumeneko kwa atsogoleri achipembedzo ndi kusaona kwawo mtima zimapangitsa anthu ambiri kukhumudwa ndi zipembedzo zonse. Koma si mfundo yokhayi yokhudzana ndi chipembedzo imene imakhumudwitsa lerolino. Atchalitchi ambiri aphunzitsidwa kuti Baibulo lili Mawu a Mulungu. Kodi angadabwe atadziŵa kuti Baibulo siliphunzitsa ziphunzitso zina za tchalitchi zimene zakhalako kwanthaŵi yaitali? Nkhani yotsatira ikufotokoza chitsanzo chimodzi.