Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 4/1 tsamba 20-22
  • Kodi Ndani Amaumba Maganizo Anu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Amaumba Maganizo Anu?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Okanikizidwa m’Chikombole cha Satana?
  • Dziŵani Zimene Zikuchitika
  • Lolani Kuumbidwa ndi Yehova
  • Tiziyamikira Kuti Yehova Amatiumba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Lolani Kuti Yehova Azikuumbani Ndi Malangizo Ake
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Muzilola Kuti Yehova Aziumba Maganizo ndi Makhalidwe Anu
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Tetezani Maganizo Anu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 4/1 tsamba 20-22

Kodi Ndani Amaumba Maganizo Anu?

“PALIBE angandiuze zoganiza! Ndipo palibe angandiuze zochita!” Nthaŵi zambiri kunena zimenezo motsimikiza mtima kumatanthauza kuti mumadzidalira kwambiri ndi kudaliranso zosankha zanu. Kodi mumaganiza motero? Ndithudi, palibe munthu amene ayenera kukusankhirani zochita. Koma kodi n’kwanzeru kungokaniratu uphungu umene ungakhale wabwino? Kodi palibiretu aliyense amene angakuthandizeni kusankha mwanzeru? Komanso, kodi mulidi wotsimikiza kuti kwenikweni palibe amene akuumba maganizo anu, inu mosazindikira kalikonse?

Mwachitsanzo, nkhondo yadziko yachiŵiri isanaulike, Joseph Goebbels, nduna ya Hitler yoyang’anira zofalitsa manenanena a boma, inayamba kulamulira opanga mafilimu a m’Germany. Chifukwa? Chifukwa inadziŵa kuti ikatero idzakhala ndi chida champhamvu kwambiri “chosonkhezerera zikhulupiriro za anthu ndiyenonso khalidwe lawo.” (Propaganda and the German Cinema 1933-1945) Muyenera kuti mukudziŵa mmene anachitira zinthu zoopsa mwa kugwiritsa ntchito njira imeneyi ndi njira zinanso posonkhezera maganizo a anthu wamba​—anthu abwinobwino, otha kulingalira paokha​—kuti atsatire malingaliro a Nazi m’chimbulimbuli.

Choonadi n’chakuti, m’njira ina yake, malingaliro ndi kaonedwe ka zinthu ka awo amene mumamvetsera zimakhudza maganizo anu, chimodzimodzinso zochita zanu nthaŵi zonse. Inde, chimenechi si chinthu choipa. Ngati amenewo ndi anthu okufunirani zabwino​—monga aphunzitsi, mabwenzi, kapena makolo​—mudzapindula kwambiri ndi uphungu wawo ndi nzeru zawo. Koma ngati ndi anthu ongofuna kupezerapo phindu ndipo amenenso ali osokeretsedwa iwo eni kapena a maganizo oipa, “onyenga,” monga momwe mtumwi Paulo anawafotokozera, chenjerani!​—Tito 1:10; Deuteronomo 13:6-8.

Choncho, musadzidalire kwambiri ndi kuganiza kuti palibiretu amene angakusonkhezereni. (Yerekezani ndi 1 Akorinto 10:12.) N’zotheka kuti panopo zikuchitika​—nthaŵi zambiri motinso mungakane​—inuyo musakudziŵa. Mwachitsanzo, tinene za zinthu zimene mumasankha kugula mutapita kokagula zinthu. Kodi nthaŵi zonse mumasankha zimene inuyo panokha, mwamalingaliro anuanu mwakonda? Kapena kodi anthu ena, nthaŵi zambiri amene simuwaona, mochenjera koma mwamphamvu amasonkhezera zosankha zanu? Mtolankhani wofufuza zinthu Eric Clark akulingalira kuti amaterodi. “Pamene atisatsa malonda owonjezeka,” anatero, “mpamenenso timaona ngati sizikutikhudza, komano mpamene timakhudzidwa kwambiri pafupifupi nthaŵi zonse.” Iye anasimbanso kuti anthu akafunsidwa ngati akuona kuti kusatsa malonda kumagwira ntchito, “ambiri amavomereza kuti kumagwiradi ntchito, koma osati pa iwo.” Anthu amaganiza kuti aliyense amasonkhezeredwa ndi osatsa malonda, kupatulapo iwo. “Zimaoneka ngati kuti iwo okha siziwakhudza.”​—The Want Makers.

Okanikizidwa m’Chikombole cha Satana?

Kaya mumasonkhezeredwa ndi osatsa malonda masiku onse mwina sizingakhale ndi zotsatirapo zoipa kwambiri. Komabe, pali chisonkhezero china chimene chili choopsa kwambiri. Baibulo limasonyeza bwino kwambiri kuti Satana ndiye wopusitsa wamkulu. (Chivumbulutso 12:9) Malingaliro ake angofanana ndi malingaliro a wosatsa malonda wina amene ananena kuti pali njira ziŵiri zokopera makasitomala​—“mwa kuwanyenga kapena mwa kuwasintha malingaliro awo.” Ngati ofalitsa manenanena ndi osatsa malonda angagwiritse ntchito machenjera ameneŵa pofuna kusintha maganizo anu, Satana ayenera kukhala waluso chotani nanga pogwiritsa ntchito njira zofananazo!​—Yohane 8:44.

Mtumwi Paulo anadziŵa zimenezi. Anada nkhaŵa kuti ena mwa Akristu anzake angachepetsa chitetezo chawo ndipo Satana angawanyenge. Analemba kuti: “Ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.” (2 Akorinto 11:3) Chenjezo limenelo muyenera kuliganizira kwambiri. Ngati simutero mungakhale monga anthu aja amene amakhulupirira kuti manenanena ndi kusintha anthu malingaliro zimagwiradi ntchito​—“koma osati pa iwo.” Nkhanza, khalidwe loipa, ndi chinyengo zomwe zachuluka mumbadwo uno ndipo zikuonekera bwino lomwe kulikonseko, zikusonyeza kuti manenanena a Satana amagwiradi ntchito.

Choncho, Paulo anachonderera Akristu anzake kuti ‘asafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano.’ (Aroma 12:2) Wotembenuza Baibulo wina analemba mawu a Paulo m’njira ina kuti: “Musalole dziko lokuzingani kukukanikizirani m’chikombole chake.” (Aroma 12:2, Phillips) Satana adzayesetsa kukukanikizirani m’chikombole chake, monga momwe woumba miphika wakale ankakanikizira dothi m’chikombole kuti litengere zizindikiro ndi zinthu zina zimene anafuna kuti likhale nazo. Satana ali wokonzeka kugwiritsa ntchito ndale, chipembedzo, ndi zosangulutsa za dzikoli pochita zimenezo. Kodi chisonkhezero chake n’chofala motani? N’chofala monga momwe chinalili m’tsiku la mtumwi Yohane. “Dziko lonse lapansi,” anatero Yohane, “ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19; onaninso 2 Akorinto 4:4.) Ngati mukukayikira kuti Satana ali ndi mphamvu yonyengera anthu ndi kuipitsa maganizo awo, kumbukirani mmene anachitira zimenezi ku mtundu wonse wa anthu, Aisrayeli, amene anali opatuliridwa kwa Mulungu. (1 Akorinto 10:6-12) Kodi zimenezo zingachitikenso kwa inu? Zingatheke ngati mulola chisonkhezero chachinyengo cha Satana kuloŵa m’maganizo mwanu.

Dziŵani Zimene Zikuchitika

Kwenikweni, zinthu zosonkhezera zimenezi zidzakhudza maganizo anu pokhapokha mutazilola. M’buku lake lakuti The Hidden Persuaders [Zosonkhezera Zobisika], Vance Packard anafotokoza kuti: “Tidakali ndi mphamvu yodziteteza nayo ku zosonkhezera [zobisika] zimenezi: tingasankhe kusasonkhezeredwa. Pafupifupi pa zochitika zonse tithabe kusankha, ndipo sitingapusitsidwe kwambiri ngati tikudziŵa zimene zikuchitika.” Ndi mmenenso zakhalira ndi manenanena ndi chinyengo.

Inde, kuti ‘mudziŵe zimene zikuchitika,’ muyenera kukhala ndi maganizo omasuka ndi olandira zisonkhezero zabwino. Maganizo abwino, monga thupi lathanzi, amafuna kudyetsedwa bwino kuti agwire ntchito bwino. (Miyambo 5:1, 2) Kusadziŵa kanthu n’koopsa mofanana ndi kukhala ndi chidziŵitso cholakwika. Choncho pamene zili zoona kuti muyenera kuteteza maganizo anu ku malingaliro ndi mafilosofi osokeretsa, yesani kusakayikira uphungu kapena chidziŵitso china chilichonse chimene mukupatsidwa.​—1 Yohane 4:1.

Kusonkhezera koona mtima sikufanana ndi manenanena a zolinga zobisika. Mtumwi Paulo anachenjezadi mnyamatayo Timoteo kuti achenjere ndi “anthu oipa ndi onyenga, [amene] adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” Koma Paulo anawonjezera kuti: “Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene adakuphunzitsa.” (2 Timoteo 3:13, 14) Popeza kuti zilizonse zimene ziloŵa m’maganizo mwanu zimakukhudzani mwa njira ina yake, chinsinsi chake ndicho ‘kudziŵa amene akukuphunzitsani zinthu,’ kuti muonetsetse kuti ndi anthu amene akukufunirani zabwino, osati ongofuna kupezerapo phindu.

Chosankha ndi chanu. Mungasankhe ‘kufanizidwa ndi makhalidwe a pansi pano’ mwa kulola mafilosofi ndi zokonda za dziko lino kusonkhezera maganizo anu. (Aroma 12:2) Koma dzikoli silikukufunirani zabwino. Chotero “penyani,” akuchenjeza motero mtumwi Paulo, “kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu.” (Akolose 2:8) Kukanikizidwa motero m’chikombole cha Satana, kapena kuti ‘akulandeni ngati chuma,’ si kovuta. Kuli ngati utsi wa fodya wosuta munthu wina. Mungakhudzidwe mwa kungopuma mpweya woipitsidwawo.

Komanso, mungapeŵe kupuma “mpweya” umenewo. (Aefeso 2:2, NW) M’malo mwake, tsatirani uphungu wa Paulo wakuti: “Mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Zimenezi zimafuna kuyesetsa. (Miyambo 2:1-5) Kumbukirani kuti Yehova sapusitsa munthu. Iye amapereka chidziŵitso chonse chofunikira, koma kuti mupindule nacho, muyenera kuchimvetsera ndi kuchilola kuti chisonkhezere maganizo anu. (Yesaya 30:20, 21; 1 Atesalonika 2:13) Muyenera kumafuna kudzaza maganizo anu ndi choonadi cha mu “malembo opatulika,” Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo.​—2 Timoteo 3:15-17.

Lolani Kuumbidwa ndi Yehova

N’kofunika kuti muchitepo kanthu mofunitsitsa ndi momvera ngati mukufuna kupindula poumbidwa ndi Yehova. Zimenezi zinasonyezedwa mwa fanizo lamphamvu kwambiri pamene Yehova anauza mneneri Yeremiya kupita kunyumba ya woumba. Yeremiya anaona woumbayo akusintha malingaliro ake pa zoti achite ndi dothi pamene mbiya imene anali kufuna kupanga “inawonongeka m’dzanja la woumba.” Kenako Yehova anati: “Nyumba ya Israyeli inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? . . . Taonani, monga dothi m’dzanja la woumba, momwemo inu m’dzanja langa, nyumba ya Israyeli.” (Yeremiya 18:1-6) Kodi zimenezo zinatanthauza kuti anthu a m’Israyeli anali ngati dothi lopanda moyo m’manja mwa Yehova kuti azingoliumba kukhala mbiya za mitundumitundu malinga ndi zimene iye akufuna?

Yehova sagwiritsa ntchito mphamvu yake yaikuluyo kupangitsa anthu kuchita zinthu zimene iwo sakufuna kuchita; ndipo salakwitsa poumba, monga momwe woumba waumunthu amachitira. (Deuteronomo 32:4) Zolakwika zimakhalapo pamene awo amene Yehova amayesa kuwaumba bwino akana chitsogozo chake. Kumeneku ndiko kusiyana kwakukulu pakati pa inuyo ndi dothi lopanda moyo. Inuyo muli ndi ufulu wa kudzisankhira. Mwa ufulu umenewo, mungasankhe kulabadira kuti muumbidwe ndi Yehova kapena mungasankhe kukana.

Limenelotu ndi phunziro lochititsa kuganiza mozama! Ndi kwabwinotu kwambiri kumvetsera liwu la Yehova m’malo mongonena mouma khosi kuti “Palibe angandiuze zochita!” Tonse tifunikira chitsogozo cha Yehova. (Yohane 17:3) Khalani monga wamasalmo Davide, amene anapemphera kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.” (Salmo 25:4) Kumbukirani zimene Mfumu Solomo inanena: “Munthu wanzeru adzamvetsera ndi kulandira malangizo owonjezeka.” (Miyambo 1:5, NW) Kodi mudzamvetsera? Mukatero, ndiye kuti ‘kulingalira kudzakudikirani, kuzindikira kudzakuchinjirizani.’​—Miyambo 2:11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena