Ulendo Wosaiwalika Usangalatsa Anthu Apachisumbu
Cuba, chisumbu chokongola m’Nyanja ya Caribbean, posachedwapa chinali ndi nyengo yotsitsimula mwauzimu imene sinachitikepo. Kwa Mboni za Yehova za m’dziko la ku West Indian limeneli, mapeto a chaka cha 1998 anadza ndi madalitso amene akhala akuwayembekezera kwanthaŵi yaitali. Kwanthaŵi yoyamba patatha zaka zoposa 30, mamembala a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anapita kumeneko, ndipo anapita ndi alendo ena 15. Alendoŵa anali nzika za ku Australia, Austria, Belgium, Great Britain, Italy, New Zealand, ndi Puerto Rico.
ICHI chinali chochitika chosaiŵalika kwa ofalitsa Ufumu 82,258 a kumeneko ndi anthu ena 87,890 amene anali nawo pachikondwerero cha Chakudya Chamadzulo cha Ambuye m’ngululu ya mu 1998.
Kuyambira pa December 1 mpaka 7, 1998, Lloyd Barry, John Barr, ndi Gerrit Lösch anachezera Nyumba ya Beteli ku Havana ndipo anakakhala nawo pa Misonkhano Yachigawo ina ya “Njira ya Moyo ya Mulungu” yomwe inachitika m’Cuba. Anali osangalala kuonana ndi akulu oyendayenda ndiponso kudziŵana bwino ndi akuluakulu a boma la Cuba.
“Ichi chinali chochitika chapadera chateokalase m’moyo wathu wonse kwa ine ndi mkazi wanga,” anatero John Barr. “Abale ndi alongo athu okondeka a ku Cuba ndi achangu kwambiri pachoonadi! Chimenecho chinandipangitsa kuona kuti ubale wathu wa padziko lonse ndi wamtengo wapatalidi!” “Mlungu wofunika kwambiri umenewu unandithandiza kudziŵa bwino mmene zinthu zilili kwa abale anthu kumeneko,” anawonjezera motero Lloyd Barry.
M’zaka zisanu zapitazo, Mboni za Yehova ku Cuba zapatsidwa ufulu waukulu wakulambira, ndipo zimene akuluakulu a boma la Cuba ananena zingapangitse wina kukhulupirira kuti iwo akufunadi kuti kusintha kumeneku kupitirire.
Mu September 1994, m’Nyumba ya Beteli ku Havana anayamba kusindikiziramo mabuku. Kachiŵirinso, Mboni za Yehova zinali zokhoza kusonkhana poyera ndiponso kuchita umboni wa kunyumba ndi nyumba. Kenako, mu 1998, akuluakulu a boma analola alendo 18 a Mboni za Yehova ochokera m’mayiko ena, kuphatikizapo mamembala atatu a m’Bungwe Lolamulira kufika m’dzikomo.
Chisangalalo Pogwirizananso
Pamene alendowo anafika pabwalo la ndege la José Martí ku Havana, analandiridwa bwino ndi gulu la akuluakulu a boma ndi anthu ochokera ku Nyumba ya Beteli, ndipo pakati pawo panali mbale yemwe amakumbukirabe ulendo womaliza umene mbale wa m’Bungwe Lolamulira anapita ku Cuba—Milton Henschel—mu 1961. Mbaleyu panthaŵiyo anali ndi zaka 12; tsopano ndi woyang’anira woyendayenda.
Pamene alendoŵa anafika pa Nyumba ya Beteli anapeza maluŵa a gladiolus, rose, jasmine, ndi maluŵa a daisy achikasu ndi ofiira, odzalidwa ndi mbale makamaka chifukwa cha chochitikachi. Misozi inkangogwa yokha pamene banja la Beteli linali kulandira alendoŵa. Pambuyo pake, anadya chakudya chachikyuba cha nyama yankhumba yootcha, mpunga ndi nyemba, salad (masamba osaphika), yucca ndi mojo (msuzi wopangidwa ndi adyo ndi mafuta a azitona), komanso zipatso. Pamapeto a chakudyachi aliyense wa m’Bungwe Lolamulira anapereka nkhani yolimbikitsa yonena za kufunika kwa utumiki wa pa Beteli. Polankhula ndi abale m’Chisipanya, makamaka nkhani ya mbale Lösch inali yolimbikitsa kwambiri. Banja la Beteli lili ndi antchito odzifunira 48 okhazikika ndi othandiza 18.
Ngakhale kuti mabuku ndi mabaibulo a abale a ku Cuba amasindikizidwa ku Italy, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a zithunzi zamtundu wakuda ndi woyera (black and white) amasindikizidwa m’dziko lomwelo, pa makina aŵiri a mimeograph. Amafunika kugwira ntchito yamanja maola ambirimbiri m’malo opanikiza kuti asindikize magazini onse amene akufunika. Antchito odzifunirawo amayamikira mwayi wawo wotumikira Yehova mwanjira yapadera.—2 Akorinto 4:7.
Mfundo za Msonkhano
Alendo 18 ameneŵa anagaŵikana m’magulu atatu kuti akapezeke pamisonkhano yachigawo yomwe inachitikira m’malo atatu—Havana, Camagüey, ndi Holguín. Tsiku lililonse pamasiku atatuŵa, abale ndi alongo ambiri, kuphatikizapo akulu ndi apainiya ambiri, anali kuitanidwa kuti akapezeke pamalo amodzi mwa malo ameneŵa. Mboni zakumaloko zinauzidwa kuti ichi chinali chochitika chapadera, koma sanadziŵe kuti mamembala a m’Bungwe Lolamulira akapezekapo. Tangolingalirani mmene anadabwira pamene anaona abale awo okondedwaŵa ndi akazi awo akutsika m’mabasi amene anachita hayala patsiku Lachisanu m’maŵa!
Misonkhanoyi inachitikira m’mabwalo opanda denga amene abale anamanga mololedwa ndi akuluakulu a boma. Pamalo a msonkhano ku Havana, lemba la “Salmo 133:1” linazokotedwa pamwala umodzi pafupi ndi khomo. Izi zinakumbutsa abale mawu opezeka pa lembali akuti: “Onani, n’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” Ndithudi, m’kati mwa msonkhanowo, pamalopo panali mayanjano achikristu abwino ndiponso osangalatsa.
Alendowo anayamikira kakambidwe kabwino ka nkhani ndi zokumana nazo, ndipo anachita chidwi ndi mmene anachitira seŵero, lomwe linazikidwa pankhani ya m’Baibulo ya pa Danieli chaputala 3, yochitikira m’Babulo wakale. Mlongo wina ananena kuti: “Ochita seŵero onse anachita bwino kwambiri, ndipo mawu anali kutuluka bwino kwambiri moti sungadziŵenso kuti anali ojambulidwa kale mukaseti. . . M’Babulo woipayo anaonekadi woipitsitsa, ndipo Ahebri atatuwo anali olimba ndi otsimikiza.”
Anthu oimira Ofesi ya Zachipembedzo ndi akuluakulu ena a boma amene anabwera kudzaonerera misonkhanoyi anayamikira abale chifukwa cha dongosolo ndi khalidwe lawo labwino. Mbale Barry anayamikira kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha zimene akuluakulu a boma la Cuba anachita kwa alendoŵa. Ndipo mwa kuwomba m’manja kwa mphindi zambiri, abalewo anasonyeza kuyamikira nkhanizo, komanso akuluakulu a boma polola misonkhanoyo kuti ichitike. “Izi si zimene timayembekezera—msonkhano wa mitundu yonse waung’ono!” linatero banja lina lachikristu. “Zakhala zosangalatsa kwambiri, chifukwa zapereka umboni wakuti Yehova ali ndi mphamvu zedi ndipo angakwaniritse malonjezo ake onse.”
Misonkhanoyi inathandiziranso ena kudziŵa bwino Mboni. M’modzi wa madalaivala a mabasi anafika pamsonkhanowo Loŵeruka ndi Lamlungu. Anati wakhala akumva zinthu zambiri zokhudza Mboni za Yehova, koma tsopano wadziŵa kuti ndi anthu abwino ndi amtendere.
“Zinthu Zimene Sitidzaiŵala”
Alendoŵa anachita chidwi ndi chisangalalo ndi ubwenzi wa anthu a ku Cuba. Akyuba ndi achangu, omvera malamulo, ndi okoma mtima. Mlendo wina anati: “Kambirimbiri, anthu osawadziŵa n’komwe anadzipereka kutithandiza.”
Alendoŵa anachita chidwi kwambiri ndi chikhulupiriro, chimwemwe, komanso chikondi chomwe Mboni zinzawo za ku Cuba zinaonetsa. Mosasamala kanthu za zopinga zambiri, apanga Yehova kukhala linga lawo. (Salmo 91:2) John Barr anati: “Paulendo wangawu woyamba wa ku Cuba, zinthu zambiri zedi zinandisangalatsa komanso zinandidabwitsa—kukongola kwa dzikoli, chisangalalo cha anthu amene ndinakumana nawo, komanso makamaka chisangalalo chosefukira cha Mboni za ku Cuba. Ndinali ndisanamvepo kuimba kochokera pansi pa mtima kwa nyimbo za Ufumu ndi kuomba m’manja kwambiri pamene zinthu zauzimu zinawagwira mtima! Izi ndi zinthu zimene sitidzaiŵala. Tidzazikumbukira nthaŵi zonse.”
Salmo 97:1 limati: “Zisumbu zambiri zikondwerere.” Ndithudi, Mboni za Yehova pachisumbu cha Cuba zikukondwera chifukwa cha ufulu wawo wowonjezereka wolambira Mulungu, ndi chifukwa cha kucheza kosaiŵalika kumeneko kwa alendo a m’mayiko ena.
[Zithunzi patsamba 8]
Mabanja ambiri anapezeka pa Misonkhano Yachigawo yapadera ya “Njira ya Moyo ya Mulungu” ya ku Cuba
[Chithunzi patsamba 8]
Nyumba ya Beteli ku Havana inatsegulidwanso mu 1994
[Chithunzi patsamba 8]
A m’Bungwe Lolamulira akusaina mphatso ya mabaibulo opita kwa akuluakulu a boma