Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 6/15 tsamba 10-13
  • Kodi Muyenera Kukulitsa Kaonedwe Kanu ka Zinthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muyenera Kukulitsa Kaonedwe Kanu ka Zinthu?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Onani Nkhani Yonse Bwinobwino
  • Mmene Mumaonera Anthu Ena
  • Pa Kupatsa Mwakuthupi
  • Popereka Uphungu
  • Yesetsani Kufutukuka
  • Kodi Mumaona Anthu Mmene Yehova Amawaonera?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Pezani Chimwemwe mwa Kukhala Wopatsa!
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Tisasiye Kutumikira Mulungu Chifukwa cha Zochita za Ena
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tiziyendera Maganizo a Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 6/15 tsamba 10-13

Kodi Muyenera Kukulitsa Kaonedwe Kanu ka Zinthu?

CHIVOMEZI chowononga kwambiri chinakantha Mzinda wa Kobe kumadzulo kwa Japan, ndipo antchito odzifunira odzipereka mwamsanga anafika kudzathandiza anthu a mumzindawo amene anali kuvutika. Komabe, munthu wina wa ku Bungwe la Zaumoyo la mumzindawo anakana pempho la gulu la madokotala obwera lakuti awapatse mankhwala. Mkulu ameneyo, amenenso anali wamkulu pa chipatala china chachikulu m’tauni ina, anafuna kuti anthu ovutikawo apite kuzipatala za ku Kobe m’malo moti madokotalawo awabaye majakisoni odula ndi kuwapatsa madiripi a mankhwala okwera mtengo m’malo olandiriramo chithandizo. Pomalizira pake, madokotalawo analandira zimene anapemphazo, koma anthu kulikonse anali kudzudzula mchitidwe woumirira chinthu chimodzimodzi ndiponso kupanda chifundo kwa mkulu wa zaumoyoyo.

Mwinamwake inunso panthaŵi ina munthu wina waudindo sanafune kugwirizana ndi zimene munali kunena. Mwinanso inuyo simunagwirizane ndi zimene wina anali kufuna. Kodi mungapindule mwa kumaona mbali zosiyanasiyana za nkhani?

Onani Nkhani Yonse Bwinobwino

Anthu kaŵirikaŵiri amangoyang’ana mbali imodzi ya zinthu, kapena kukhala ndi malingaliro amodzi okha, motero akumachepetsa kulingalira ndi kumvetsetsa kwawo kwa zinthu. Kaŵirikaŵiri izi zimakhala choncho chifukwa cha zinthu ngati maphunziro, zimene munthu wakumanapo nazo, ndi mmene anakulira. Munthu angasankhe zochita zanzeru pamene ayesetsa kukhala ndi chithunzi chonse cha nkhaniyo. Mwachitsanzo, ngati munali kudutsa pamphambano ya misewu yomwe mumadutsa magalimoto ambiri pomwe palibe maloboti, kodi kungakhale kwanzeru kungonyang’ana kutsogolo? Kutalitali! Mofananamo, kukulitsa kalingaliridwe kanu kuti mukhale ndi chithunzi chonse kungakuthandizeni kwambiri posankha chochita ndi pochita zinthu mwauchikulire. Kungapulumutsenso moyo.

Mwachionekere, tonsefe tingawongolere pambali imeneyi. Motero dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi mbali zina ziti zimene ndingapindule nazo mwa kukulitsa kalingaliridwe kanga?’

Mmene Mumaonera Anthu Ena

Kodi mumaona chiyani pamene muyang’ana anthu ena? Kodi muli ndi chizoloŵezi choona zimene amanena kapena kuchita monga ngati kuti zonse ndi zabwino kapena kuti zonse ndi zoipa, ngati kuti palibenso mbali zina zankhaniyo zoyenera kuziganizira? Kodi zimene wina amakunenerani mumaziona ngati akukuyamikirani kapena ngati akukuchitani chipongwe? Kodi munthu wina amakhala wolondola kwambiri kapena wolakwiratu? Kukhala ndi malingaliro oterowo kungakhale ngati munthu wojambula zithunzi amene amanyalanyaza maonekedwe amitundu yosiyanasiyana a malo ena m’dzinja, ngati kuti panali kokha mtundu wakuda ndi woyera. Kapena kodi mumakonda kulingalira kwambiri za mbali zolakwika za umunthu wa munthu wina, mofanana ndi mlendo wokaona malo amene amalephera kusangalala pamalo okongola chifukwa cholingalira za tizinyalala tosiyidwa pamalopo ndi alendo ena osaganizira anzawo?​—Yerekezerani ndi Mlaliki 7:16.

Tingaphunzire zambiri mwa kulingalira mmene Yehova amaonera zolakwa za anthu. Ngakhale kuli kwakuti amazindikira zofooka ndi zolephera zambirimbiri za anthu, iye amasankha kusaika malingaliro ake kapena kusangoyang’ana zomwezo basi. Wamasalmo woyamikirayo anati: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani?” (Salmo 130:3) Yehova ali wofunitsitsa kutaya kutali zolakwa za ochimwa olapa, inde kuzichotseratu ndi mtima wonse, kotero kuti sizikuipitsanso unansi wathu ndi iye. (Salmo 51:1; 103:12) Ponena za Mfumu Davide, amene panthaŵi ina anachita machimo aakulu ndi Bateseba, Yehova anati Davide anali munthu amene ‘ananditsata ndi mtima wake wonse kuchita zolunjika zokhazokha pamaso panga.’ (1 Mafumu 14:8) Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu ananena zimenezi ponena za Davide? Chifukwa chakuti iye anali kuyang’ana pa mikhalidwe yabwino ya Davide wolapayo. Analingalira chilichonse chimene chinali kumukhudza Davide ndipo anasankha kupitirizabe kuchitira mtumiki wakeyo chifundo.

Kristu Yesu mosaphonya anasonyeza kulingalira mbali zosiyanasiyana za zolakwa za ena kumeneku. (Yohane 5:19) Atumwi ake akalakwitsa zinthu, Yesu anali wachifundo ndipo anali kumvetsetsa. Ponena za anthu opanda ungwiro, iye anazindikira kuti ngakhale pamene ‘mzimu uli wofuna, thupi limakhala lolefuka.’ (Mateyu 26:41) Polingalira zimenezi, Yesu anali kuchita ndi zofooka ndi zolakwa za ophunzira ake moleza mtima ndi momvetsetsa. Sanali kusumika malingaliro pa zolakwa zawo koma m’malo mwake, anali kulingalira za mikhalidwe yawo yabwino.

Panthaŵi ina atadzudzula atumwi ake chifukwa cha kukangana za amene anali kuoneka kukhala wamkulu, Yesu anatinso: “Koma inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Luka 22:24-30) Inde, mosasamala kanthu kuti atumwiwo anali ndi zolakwa zambirimbiri, Yesu anakumbukira za kukhulupirika kwawo ndiponso chikondi chimene anali nacho pa iye. (Miyambo 17:17) Yesu anali wokhutira ndi zimene akanatha kuchita komanso zimene anali kudzachita, motero anapangana nawo pangano la Ufumu. Inde, ‘Yesu anakonda ophunzira ake kufikira chimaliziro.’​—Yohane 13:1.

Chotero ngati umunthu wa munthu wina ndipo zolakwa zake zimakukwiyitsani, khalani ngati Yehova ndi Yesu. Kulitsani kalingaliridwe kanu, ndipo yesani kulingalira za mbali iliyonse. Mwa kuika zinthu m’malo ake oyenera, mudzaona kuti ndi kosavuta kukonda ndi kuyamikira abale anu.

Pa Kupatsa Mwakuthupi

Mwayi wa kupatsa ndi chimodzi cha zinthu zimene Akristu amasangalala nazo. Koma kodi tiyenera kumangopatsa m’njira imodzi yokha, mwachitsanzo, kupita mu utumiki wakumunda? (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kapena kodi mungakulitse kalingaliridwe kanu kuti muphatikizepo zosoŵa zakuthupi ndiponso ubwino wa ena? Zoonadi, Akristu onse amazindikira kuti kupatsa mwauzimu ndiko kofunika kwambiri. (Yohane 6:26, 27; Machitidwe 1:8) Komabe, pamene kuli kwakuti kupatsa mwauzimu ndi kofunika kwambiri, kupatsa mwakuthupi ndithudi sikufunika kunyalanyazidwa.​—Yakobo 2:15, 16.

Pamene tisinkhasinkha za zinthu zimene abale athu auzimu mumpingo mwathu ndiponso padziko lonse akufunikira mwamsanga, tikhoza kuzindikira bwino kwambiri zimene tingachite kuti tiwathandize. Pamene awo amene angathe kuchita zimenezi agaŵirako anzawo mowolowa manja, pamakhala kulingana. Mwa njirayi timasamalira zosoŵa za abale athu onse. Mkulu wina wachikristu analongosola motere: “Ngati abale a mbali ina yadziko akusoŵa zinthu, abale ku mbali inanso yadziko adzawathandiza. Ngati iwo sangathe kuthandiza, ndiye kuti abale akwina adzathandizapo. Choncho zosoŵa za abale athu padziko lonse lapansi zimakhala zikusamaliridwa. Ubale wa padziko lonse ulidi wodabwitsa.”​—2 Akorinto 8:13-15; 1 Petro 2:17.

Mlongo wina wachikristu amene anafunitsitsadi kukapezeka pa msonkhano wina wa mitundu yonse umene unachitikira ku Eastern Europe sanathe kutero. Iye anamva kuti abale akumeneko anali kusoŵa mabaibulo kwambiri, motero iye anapereka chopereka kaamba ka mabaibulowo kupyolera mwa munthu wina amene anakapezekapo. Motero iye anapeza chimwemwe pa kupatsa, kuthandiza abale ake m’dziko lina.​—Machitidwe 20:35.

Mwinamwake mwa kufutukula kalingaliridwe kanu mungathandize kwambiri ntchito yomwe ikukulirakulira yophunzitsa Baibulo padziko lonse, zomwe zingapatse inuyo ndiponso anthu ena chimwemwe.​—Deuteronomo 15:7; Miyambo 11:24; Afilipi 4:14-19.

Popereka Uphungu

Pamene tapemphedwa kuti tikapatse munthu wina uphungu kapena kumuwongolera, kulingalira momuganizira ndi mosamala kudzathandiza kuti abale athu auzimu azitipatsa ulemu ndi kuti tizithadi kuthandiza anthu. Ndi kosavuta kungolingalira mfundo zochepa zokha basi ndi kugamula mwamsangamsanga, mokonderanso. Izi zimapereka chithunzi chakuti timalingalira pang’ono, mwinanso kuti sititha kulingalira, monga ngati atsogoleri achipembedzo a m’tsiku la Yesu, amene anali kukonda kusenzetsa ena mtolo wa malamulo awo osatha. (Mateyu 23:2-4) Kumbali ina, ngati tipeŵa kuchita mopambanitsa ndi kumapereka uphungu wabwino wozikidwa kwambiri pa mapulinsipulo a m’Malemba, kusonyeza kalingaliridwe ka Yehova kolungama komanso kosamala ndi kachifundo, kudzakhala kosavuta kuti ena alandire ndi kugwiritsa ntchito malingaliro athu.

Zaka zingapo zapitazo, abale achinyamata ochokera m’mipingo ingapo anasonkhana ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi. Mwatsoka, panaloŵa mzimu wampikisano womwe unachititsa kuyamba kukhadzulirana mawu. Kodi akulu akumeneko anachita motani ndi nkhaniyo? Pozindikira kufunika kwakuti achinyamata azisanguluka, iwo sananene kuti angolekeratu. (Aefeso 5:17; 1 Timoteo 4:8) M’malo mwake, iwo anawachenjeza mwamphamvu koma molingalira za zimene zingatsatire mzimu wampikisano. Anawapatsanso malingaliro othandiza, monga ngati kukhala ndi anthu ena achikulire ndi audindo. Achinyamatawo anayamikira kuti uphunguwo unali wanzeru ndiponso wabwino ndipo anautsatira. Ndiponso, anayamba kulemekeza ndi kukonda akulu kwambiri.

Yesetsani Kufutukuka

Pamene kuli kwakuti mosafuna kapena mosadziŵa mungakhale atsankhu, mudzafunikabe kutsimikiza mtima kuti muyesetse kukulitsa kalingaliridwe kanu. Pamene mukuphunzira Mawu a Mulungu, sinkhasinkhani pa zimene mukuphunzirazo kotero kuti mupeze ndi kuzindikira kalingaliridwe ka Yehova. (Salmo 139:17) Yesani kumvetsa zifukwa zimene mawu amene ali m’Baibulo analembedwera ndiponso mapulinsipulo amene akuloŵetsedwamo, ndipo yesetsani kuchita zinthu monga Yehova amachitira. Zimenezi zidzagwirizana ndi pemphero la Davide lakuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse.”​—Salmo 25:4, 5.

Mudzadalitsidwa pamene mukulitsa kaonedwe kanu ka zinthu. Dalitso lina limene mungapeze pokulitsa kaonedwe kanu ka zinthu ndi kukhala ndi mbiri yabwino yakuti ndinu wosamala ndi womvetsetsa. Mudzakhala wokhoza kuchita zinthu bwino ndiponso momvetsetsa pamene mukupereka chithandizo pankhani zosiyanasiyana. Ndipo zimenezi zidzawonjezera kugwirizana kodabwitsa kwa ubale wachikristu.

[Zithunzi patsamba 12]

Kupatsa mowolowa manja kumathandiza ena, kumabweretsa chimwemwe kwa wopatsayo, ndipo kumasangalatsa Atate wathu wakumwamba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena