Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 10/1 tsamba 26-27
  • Miyambi Yaumulungu ndi Chifuno cha Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Miyambi Yaumulungu ndi Chifuno cha Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Miyambi ya m’Baibulo N’njochuluka
  • Kuvumbula Zinsinsi za Mulungu
  • Kuunika ‘Mawu Ophiphiritsa’
  • Kuyang’ana Kuunika
  • Pezani Nzeru Ndipo Landirani Mwambo
    Nsanja ya Olonda—1999
  • ‘Mulungu, Tumizani Kuunika Kwanu’
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Chinsinsi Chimene Akristu Sayenera Kusunga!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Yehova—Mulungu Wovumbula Zinsinsi
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 10/1 tsamba 26-27

Miyambi Yaumulungu ndi Chifuno cha Mulungu

NGATI wina sadziŵa tanthauzo lake, ndiye kuti n’nchomwecho; koma ngati wina adziŵa tanthauzo lake, ndiye kuti sindicho. Chiyani chimenecho? Mwambi.

M’chikhalidwe chamakono cha moyo wotanganidwa kwambiriwu, anthu amaona kuti kupherana miyambi n’zachibwana, koma kalero, miyambi “inali choyesera nzeru,” monga mmene The Interpreter’s Dictionary of the Bible ikunenera.​—Yerekezani ndi Miyambo 1:5, 6.

M’malo mongotchula cholinga kapena chifuno chake mwachindunji, nthaŵi zina Yehova, mwa kufuna kwake, wanena mawu ake aulosi mophiphiritsa, poyerekeza zinthu zosiyana, pokuluŵika m’zining’a, kapena miyambi yovuta zedi. (Salmo 78:2; Numeri 12:8) Ngakhale kuti liwu la Chihebri lotanthauza phiphiritso lagwiritsidwa ntchito nthaŵi 17 zokha m’Baibulo, m’Malemba muli mawu ophiphiritsa ndi miyambi yambirimbiri.

Miyambi ya m’Baibulo N’njochuluka

Mfumu Solomo akuti ankatha kumasulira mafunso othetsa nzeru, kapena miyambi yopomboneza imene anthu anadza nayo kwa iye. (1 Mafumu 10:1) Izi zinatheka chifukwa cha nzeru yopatsidwa ndi Mulungu. Ngati nkhani yolembedwa ndi olemba mbiri akale ili yoona yakuti panthaŵi ina yake Solomo analephera mpikisano womasulira miyambi wa pakati pa iye ndi Mfumu Huramu ya ku Turo, mwinamwake zimenezo zinachitika mzimu wa Yehova utachoka pa iye chifukwa cha kupanduka kwake. Woweruza Samsoni anaonetsanso kuti anali wokonda miyambi. Panthaŵi ina, anatsogozedwa ndi mzimu woyera, anapha mwambi umene unachititsa mantha adani a Mulungu.​—Oweruza 14:12-19.

Miyambi yambiri ya m’Baibulo, imakhudzana mwachindunji ndi chifuno cha Yehova. Mwachitsanzo, talingalirani za Genesis 3:15. Ulosi umenewu, womwe umayala maziko a mutu wa nkhani wa Baibulo, mwa iwo wokha ndi phiphiritso, “chinsinsi chopatulika.” (Aroma 16:25, 26) Kuwonjezera pa kupatsidwa masomphenya ndi mavumbulutso aumulungu, mtumwi Paulo anaonanso zina mwa zifuno za Mulungu “ngati chimbuuzi,” kapena kuti “liwu losadziŵika bwino tanthauzo lake.” (1 Akorinto 13:12; 2 Akorinto 12:1-4) Bwanji ponena za malingaliro osiyanasiyana omwe akupitirizabe kufalikira, onena za nambala yophiphiritsa ya chilombo​—“mazana asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi”​—yongoonekera mwadzidzidzi pa Chivumbulutso 13:18, popandanso kutanthauzira kwake? Kodi angakhoze kumasulira miyambi yaumulungu imeneyi ndani, ndipo cholinga chake n’chiyani?

Kuvumbula Zinsinsi za Mulungu

Kwa ambiri a ife, kuona ndiyo mphamvu ya mtengo wapatali zedi mwa mphamvu zonse zisanu za thupi. Koma popanda kuwala, maso a munthu angakhale opanda ntchito. Tingakhale ngati akhungu. Zilinso chimodzimodzi ndi maganizo a munthu. Amakhoza kusiyanitsa mikhalidwe yosiyanasiyana modabwitsa, kupereka mfundo, ngakhalenso kupeza mayankho a mawu okuluwika. Komabe, pakufunikabe chinthu china kuti zinsinsi za Mulungu zivumbulidwe. Ngakhale kuti ena angayese kutanthauzira miyambi ya m’Baibulo malinga ndi maganizo awo, Mlembi wake yekhayo, Yehova, Mulungu wa kuunika, ndiye amene angavumbule matanthauzo ake enieni.​—1 Yohane 1:5.

Mwatsoka, anthu n’ngonyada kotheratu ndiponso safuna kudikira Yehova kuwapatsa mayankho. Pochita chidwi ndi zinsinsi, pali ena amene amangofuna kuoneka ngati anzeru, koma osati kudziŵa zoona zake zenizeni, ndipo iwo amafunafuna mayankho ake kwina ndi kwina osati m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, zinsinsi za Ayuda zofotokozedwa m’chiphunzitso chamakono chotchedwa Cabala zimafotokoza za kufunika kwa matsenga a manambala ndi zilembo za alifabeti ya Chihebri. Okhulupirira chiphunzitso cha chinositisizimu a m’zaka za zana lachiŵiri, ankagwiritsanso ntchito Malemba Achihebri ndi Achigiriki poyesa kuvumbula matanthauzo a zinsinsi zopezeka m’Malembawo.

Komabe, kafukufuku yenseyo, anapitiriza kuwatsogolera ku ziphunzitso zakunja kapena miyambo ndi kuwalekanitsa kutali ndi zoona zenizeni zaumulungu. Okhulupirira chiphunzitso cha chinositisizimu anati: ‘Ndithudi, ngati dziko ladzala ndi kuipa, ndiye kuti Mlengi wakenso, Yahweh, sangakhale Mulungu wabwino.’ Kodi anayenera kugamula mwa mtundu umenewu? Zangosonyezeratu kuti maganizo amunthu n’ngochepa zedi! N’zosadabwitsa kuti mtumwi Paulo, polimbana ndi malingaliro olakwika omwe anayambitsidwa ndi mpatuko wa okhulupirira chiphunzitso cha chinositisizimu anachenjeza m’kalata yake kuti: ‘Musapitirire zimene zilembedwa!’​—1 Akorinto 4:6.

Kuunika ‘Mawu Ophiphiritsa’

Komabe n’chifukwa chiyani Mulungu wa kuunika analankhula ‘m’mawu ophiphiritsa’? Ndi iko komwe, miyambi mwa iyo yokha imatsutsa kalingaliridwe ka munthu ndi nzeru yozindikirira zinthu. Choncho, ikupezeka m’Malemba monse ngati zokometsera chakudya chapamwamba zedi. Nthaŵi zina inagwiritsidwa ntchito kungodzutsa chidwi cha omvetsera kapena kuti uthengawo umveke bwino lomwe. Pamene yagwiritsidwa ntchito mwa njira imeneyi, mawu omasulira mwambiwo amaperekedwa nthaŵi yomweyo pambuyo powufotokoza.​—Ezekieli 17:1-18; Mateyu 18:23-35.

Yehova amapatsa nzeru modzala manja koma sapereka mosasamala. (Yakobo 1:5-8) Lingalirani za buku la Miyambo, muli mawu ovuta kuwamva ambirimbiri ouziridwa, ndipo ena aiwo amamveka ngati miyambi. Kuti umvetsetse matanthauzo ake, pamafunika nthaŵi ndi kusinkhasinkha. Koma kodi ndi anthu angati amene ali ofunitsitsa kuyesetsa? Nzeru yomwe ili mmenemo n’njopezeka kwa okhawo amene akufunitsitsadi kuikumba.​—Miyambo 2:1-5.

Yesu anagwiritsanso ntchito mafanizo povumbula poyera malingaliro a omvetsera ake. Makamu anasonkhana mom’zinga iye. Anasangalala ndi nkhani zake. Anakonda zozizwitsa zomwe anachita. Koma, kodi ndi angati aiwo amene anali ofunitsitsa kusintha njira zawo za moyo ndi kum’tsatira iye? N’zosiyana kotheratu ndi ophunzira a Yesu, omwe nthaŵi zonse anasonyeza kuti akumvetsetsa ziphunzitso za Yesu ndipo mofunitsitsa anadzikana okha ndi kukhala om’tsatira iye!​—Mateyu 13:10-23, 34, 35; 16:24; Yohane 16:25, 29.

Kuyang’ana Kuunika

“Kuchita chidwi ndi miyambi,” nkhani ina ikutero, “kukuoneka kuti kukuombana ndi nyengo ya kugalamuka m’maphunziro.” Lerolino tili ndi mwayi chifukwa tikukhala m’nyengo imene ‘kuunika kwauzimu kwafesekera’ anthu a Mulungu. (Salmo 97:11; Danieli 12:4, 9) Kodi tingayembekeze moleza mtima kuti Yehova avumbule chifuno chake m’nthaŵi yake yoikika? Chofunika koposa, kodi timachitapo kanthu mwamsanga kuti tisinthe miyoyo yathu pamene tazindikira mmene tingagwirizanire kotheratu ndi chifuno cha Mulungu chovumbulidwacho? (Salmo 1:1-3; Yakobo 1:22-25) Ngati tikutero, Yehova adzadalitsa kuyesetsa kwathu, ndipo, monga momwe mandala amathandizira kuona bwino lomwe, mzimu woyeranso udzationetsa masomphenya okongola a chifuno chaumulungu m’maso a malingaliro athu, ndi kunola masomphenya athu auzimu.​—1 Akorinto 2:7, 9, 10.

Ndithudi, miyambi ya m’Malemba imachitira umboni ukulu wa Yehova monga “Wakuvumbulutsa zinsinsi.” (Danieli 2:28, 29) Komanso, iye amasanthula mitima. (1 Mbiri 28:9) Sitiyenera kudabwa poona kuti kuvumbulidwa kwa zoona zenizeni za umulungu kwakhala kukupitabe patsogolo. (Miyambo 4:18; Aroma 16:25, 26) M’malo mofunafuna chidziŵitso cha zakuya zake za Mulungu m’zinsinsi kapena m’nzeru zochepa kwambiri za anthu, zomwe zingatsogolere ku utsiru, tiyeni mwachidaliro tiyang’ane kwa Yehova Mulungu ndi kuti iye ativumbulire choonadi chopezeka ‘m’zinsinsi zake’ kudziŵikitsa chifuno chake chozizwitsa kwa atumiki ake okhulupirika panthaŵi yake yoikika.​—Amosi 3:7; Mateyu 24:25-27.

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Biblia Hebraica Stuttgartensia, Deutsche Bibelgesellschaft Stuttgart

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena