‘Mbuzi ya Kumapiri ya Maonekedwe Osiririka’
AMBIRIFE sitingagwiritse ntchito mawu akuti kusiririka pofotokoza mbuzi. Tingaganize kuti mbuzi ndi nyama zofunikira kwambiri zomwe zimadya zinthu zosiyanasiyana ndiponso zimene zimakhala ndiwo yokoma komanso zomwe zimatipatsa mkaka—komatu n’kovuta kuti tizitche za maonekedwe osiririka.
Ngakhale zili choncho, Baibulo limafotokoza mkazi kuti ali “ngati mbaŵala yokonda ndi chinkhoma chachisomo [“mbuzi yakumapiri yosiririka,” NW].” (Miyambo 5:18, 19) Solomo, mlembi wa buku la Miyambo, anali woyang’anitsitsa wachidwi zinthu zachilengedwe za ku Israyeli ndipo mosakayikira anali ndi chifukwa chomveka pogwiritsa ntchito fanizo limeneli. (1 Mafumu 4:30-33) Mwinamwake, mofanana ndi atate wake Davide, ankaona mbuzi za kumapiri zimene zinkapezeka kudera lozungulira Engedi kufupi ndi kugombe la Nyanja Yakufa.
Magulu ochepa a mbuzi za kumapiri zimene zimakhala kufupi ndi Chipululu cha Yudeya kaŵirikaŵiri zimadzafika ku akasupe a ku Engedi. Kwa zaka mazana ambiri mbuzi za kumapiri zakhala zikukamwa madzi ku Engedi chifukwa ndi kokhako kumene kuli akasupe odalirika m’dera loumali. Kwenikweni dzina lakuti Engedi limatanthauza “kasupe wa mwana wa mbuzi,” umboni wakuti kumapezeka ana a mbuzi ku dera limeneli. Mfumu Davide inakabisalako malo ameneŵa pamene inkathaŵa Mfumu Sauli, n’chifukwa chake ankabisala “m’matanthwe a zinkhoma [“mbuzi za kumapiri,” NW].”—1 Samueli 24:1-5.
Mutakhala ku Engedi mungaone mbuzi ya kumapiri yaikazi ikuyenda mwa phee ili chinyachinya kutsika patherezi lamiyala motsatira yaimuna ulendo wakumadzi. Ndiyetu mungayambe kumvetsa kufanana kwa mbuzi ya kumapiri yaikazi ndi mkazi wokhulupirika. Kufatsa kwake komanso kaumbidwe ka thupi lake kokongola ndizonso mikhalidwe ya akazi. Mawu akuti “kusiririka” kwenikweni amanena za maonekedwe ochititsa kaso ndi okongola a mbuzi ya kumapiri.a
Mbuzi ya kumapiri yaikazi iyenera kukhala yamphamvu komanso yokongola. Ngati momwe Yehova anasonyezera kwa Yobu, mbuzi ya kumapiri imaberekera m’mapanga a therezi, kumapiri, malo osafikika kumene chakudya chingakhale chosoŵa ndiponso nyengo yozizira. (Yobu 39:1) Ngakhale pali zovuta zimenezi, mbuzi ya kumapiri imasamalira ana ake ndiponso imawaphunzitsa kukwera ndi kudumpha pakati pa miyala mofulumira kwambiri monga momwe nayonso imachitira. Mbuzi ya kumapiri imatetezanso ana ake mwamphamvu kwa adani ake. Munthu wina anaona mbuzi ya kumapiri ikuteteza mwana wake kwa chimphamba kwa theka la ola, pamenepo n’kuti kamwanako katabisala kumimba.
Akazi achikristu omwenso ndi amayi kaŵirikaŵiri amalera ana awo m’mikhalidwe yovuta. Mofanana ndi mbuzi ya kumapiri, amasonyeza kudzipereka ndi chikondi posamalira udindo wawo wopatsidwa ndi Mulungu. Komanso amayesetsa mwamphamvu kuteteza ana awo ku ngozi zauzimu. Ndiyetu, m’malo monyoza akazi ndi fanizo limeneli, kwenikweni Solomo ankafuna kusonyeza maonekedwe ochititsa kaso ndi kukongola kwa mkazi—mikhalidwe yauzimu imene imaonekera ngakhale m’malo ovuta kwambiri.
[Mawu a M’munsi]
a Malinga n’kunena kwa buku lotchedwa The New Brown-Driver-Briggs-Gesenius Hebrew and English Lexicon, m’nkhani imeneyi mawu achihebri akuti chen, otembenuzidwa kuti “chosiririka,” amatanthauza ‘maonekedwe ndi kaumbidwe ka thupi kochititsa kaso kapena kokongola.’
[Zithunzi pamasamba 30, 31]
Mkazi wachikristu yemwenso ndi mayi amasonyeza makhalidwe abwino auzimu pokwaniritsa udindo wake wopatsidwa ndi Mulungu