Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w03 12/15 tsamba 32
  • Kodi Mumachita Chidwi ndi Zinthu Zodabwitsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumachita Chidwi ndi Zinthu Zodabwitsa?
  • Nsanja ya Olonda—2003
Nsanja ya Olonda—2003
w03 12/15 tsamba 32

Kodi Mumachita Chidwi ndi Zinthu Zodabwitsa?

KODI mwaona kuti mobwerezabwereza, olemba Baibulo amatipangitsa kuti tidabwe pamene akuyamikira ntchito ndi makhalidwe a Mulungu? Wamasalmo anati: ‘Chipangidwe changa ndi chodabwitsa.’ (Salmo 139:14) Mneneri Yesaya analemba kuti: “Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa.” (Yesaya 25:1) Kapena taganizirani kudabwa ndi kugoma kumene kuli m’mawu a Mtumwi Paulo akuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu!”​—Aroma 11:33.

Buku la Mtanthauzira Mawu wa Chinyanja limatanthauzira mawu oti “dabwa” kuti ndi ‘kudzidzimuka chifukwa chosakhulupirira zomwe munthu waona, kumva kapena kugwira.’

Kodi sizosangalatsa kuona ana aang’ono akudabwa kwambiri akaona, kukhudza kapena kumva zinthu zomwe zili zatsopano kwa iwo? N’zomvetsa chisoni kuti kudabwa chifukwa chokhala ndi chidwi kapena chifukwa cha zinthu zatsopano kumeneku nthaŵi zambiri kumatha munthu akamakula.

Komabe, kwa anthu olemba Baibulo omwe angogwidwa mawuwa, kudabwa kunali chikhalidwe chawo m’moyo wawo wonse. N’chifukwa chiyani zinali choncho? Iwo anakulitsa kuchita chidwi ndi zinthu zodabwitsa mwa kusinkhasinkha ntchito za Mulungu moyamikira. Wamasalmo anapemphera kuti: “Ndikumbukira zaka za kale lomwe, ndilingalira zija zonse munazichita; zodabwitsa za chilengedwe chanu zidzaza maganizo anga.”​—Salmo 143:5, The New English Bible.

N’zoyamikirika kwambiri kuti olambira Mulungu amakono amachita chidwi ndi zinthu zodabwitsa. Kodi inu muli nacho chidwicho? Kodi mukuchikulitsa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena