Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 12/1 tsamba 3
  • Kodi N’zotheka Anthu Padziko Lonse Kugwirizana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’zotheka Anthu Padziko Lonse Kugwirizana?
  • Nsanja ya Olonda—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Banja la Yehova Lili ndi Umodzi Wamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Sungani Umodzi m’Masiku Ano Otsiriza
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Padziko Lonse Anthu Akugwirizana—Kodi Zikutheka Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Kugwirizana
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2007
w07 12/1 tsamba 3

Kodi N’zotheka Anthu Padziko Lonse Kugwirizana?

KODI dziko lathuli lili ndi tsogolo la mtendere kapena loopsa? Zikuoneka kuti pali mfundo zogwira mtima zotsimikizira mbali ziwiri zonsezi.

Pali atsogoleri ena amene amanena motsimikiza kuti n’zotheka dziko lonse kukhala lamtendere, ndipo mwina amatero chifukwa popanda mtendere zinthu zingaipe kwambiri. Komano pali anthu ena amene amachita mantha akaganizira mafunso monga awa: Kodi ndi mayiko ati amene ali ndi zida zoopsa kwambiri? Kodi sadzazigwiritsa ntchito m’tsogolo? Kodi atatero zinthu zingakhale bwanji?

Zochitika m’mbiri ya anthu zikuonetsa kuti kupikisana ndiponso tsankho n’zimene zachititsa kuti padziko pano pakhale kusagwirizana, ndipo nthawi zambiri zipembedzo zimawonjezera vutoli m’malo molithetsa. Wolemba nkhani wina, dzina lake James A. Haught anati: “Pakakhala chinachake chogawanitsa anthu, mtendere umavuta, ndipotu zipembedzo zili m’gulu la zinthu zogawanitsa anthu kwambiri. Ngakhale kuti anthu ambiri amakhulupirira kuti zipembedzo zimathandiza anthu kukhala abwino, zikuonekeratu kuti zikupangitsa anthu ena kuchita zinthu zoipa kwambiri.” Wolemba mabuku wina, dzina lake Steven Weinberg, ali ndi maganizo ofanana. Iye anati: “Munthu wabwino angachite zinthu zoipa kwambiri, ngati atalimbikitsidwa kutero ndi chipembedzo chake.”

Kodi pali chiyembekezo chilichonse chakuti anthu padziko lonse adzakhala ogwirizana? Inde chilipo. Koma monga tionere, anthu kapena zipembedzo zimene amayambitsa, si zimene zingachititse anthu padziko lonse kukhala ogwirizana.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Kodi dzikoli lili ngati bomba lotcheratchera, lomwe lingathe kuphulika nthawi ina iliyonse?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena