Zamkatimu
February 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
April 4-10, 2011
Mzimu Woyera Unagwira Ntchito Polenga Zinthu
TSAMBA 6
April 11-17, 2011
Anthu Ovomerezeka ndi Mulungu Adzapeza Moyo Wosatha
TSAMBA 13
April 18-24, 2011
Muzikonda Chilungamo ndi Mtima Wanu Wonse
TSAMBA 24
April 25, 2011–May 1, 2011
Kodi Mumadana ndi Kusamvera Malamulo?
TSAMBA 28
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 6-10
Mfundo za m’nkhani ino zitithandiza kumvetsa bwino mmene Mulungu anagwiritsira ntchito mzimu woyera polenga kumwamba ndi dziko lapansi. Nkhani imeneyi itithandizanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu kuti Yehova ndi Mlengi wanzeru ndiponso wamphamvu.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 TSAMBA 13-17
Nthawi zambiri anthu amadera nkhawa zinthu zakuthupi. Koma Baibulo limasonyeza kuti tiyenera kumaganizira kwambiri za kukhala wovomerezeka ndi Mulungu. Nkhaniyi ifotokoza bwino kufunika kokhulupirira kwambiri Yehova ndipo isonyezanso zimene tingachite kuti tikhale ovomerezeka ndi iye.
NKHANI ZOPHUNZIRA 3, 4 TSAMBA 24-32
‘Yesu ankakonda chilungamo ndipo ankadana ndi kusamvera malamulo.’ (Aheb. 1:9) Nkhanizi zitiuza mmene tingamutsanzirire. Zifotokoza bwino kufunika kokonda chilungamo ndiponso kudana ndi kusamvera malamulo.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI:
11 Kodi Tiyeneradi Kuchita Khama?
12 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
18 Kodi Mumayamikiradi Madalitso Amene Mwalandira?