Zamkatimu
December 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
January 30, 2012–February 5, 2012
Kodi Solomo Ndi Chitsanzo Chabwino Kapena Choipa?
TSAMBA 8
February 6-12, 2012
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu?
TSAMBA 13
February 13-19, 2012
Anthu Okhulupirika Akale Amene Anatsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu
TSAMBA 18
February 20-26, 2012
Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Akhristu Oyambirira Ndipo Ukutsogoleranso Akhristu Masiku Ano
TSAMBA 22
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 8-12
Anthu ena otchulidwa m’Baibulo anapereka chitsanzo chabwino koma anachita zinthu zinanso zimene tiyenera kupewa. Nkhani ino itithandiza kuona zinthu zabwino komanso zoipa zimene Solomo anachita. Tiyeni tione zimene iye anachita n’cholinga choti tizichita bwino pa moyo wathu monga Akhristu.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 TSAMBA 13-17
M’chilengedwechi muli mphamvu ina imene ingathe kutitsogolera bwinobwino m’dziko loipali. Kodi mphamvu imeneyi ndi iti ndipo n’chifukwa chiyani iyenera kutitsogolera? Kodi tingatani kuti izitithandiza kwambiri pa moyo wathu?
NKHANI ZOPHUNZIRA 3, 4 TSAMBA 18-26
Atumiki a Mulungu ambiri a m’mbuyomu anapatsidwa mzimu woyera. Kodi mzimuwo unkawathandiza bwanji? Kuona mmene Yehova ankawathandizira kungatilimbikitse kwambiri pamene tikuchita utumiki wathu.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 Ndapindula Kwambiri Chifukwa Chololera Kusintha Zinthu
27 Musalole Kuti Matenda Akulandeni Chimwemwe
32 Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda a 2011