Zamkatimu
March 15, 2012
© 2012 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA
APRIL 30, 2012–MAY 6, 2012
Thandizani Anthu Kuti ‘Adzuke ku Tulo’
TSAMBA 10 • NYIMBO: 65, 96
MAY 7-13, 2012
TSAMBA 15 • NYIMBO: 92, 47
MAY 14-20, 2012
Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu
TSAMBA 20 • NYIMBO: 129, 134
MAY 21-27, 2012
Musamayang’ane “Zinthu za M’mbuyo”
TSAMBA 25 • NYIMBO: 119, 17
CHOLINGA CHA NKHANI ZOPHUNZIRA
NKHANI ZOPHUNZIRA 1, 2 TSAMBA 10-19
Ziphunzitso zonyenga zachititsa kuti anthu ambiri akhale m’tulo tauzimu. Nkhani ziwirizi zikufotokoza mmene tingadzutsire anthu komanso chifukwa chake tiyenera kuchita zimenezi mwachangu. Ikufotokozanso tanthauzo la kulalikira modzipereka komanso zimene tingachite kuti ifeyo tikhale maso.
NKHANI YOPHUNZIRA 3 TSAMBA 20-24
Mtumwi Petulo analemba kuti Akhristu odzozedwa ali ndi “chiyembekezo cha moyo.” (1 Pet. 1:3) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani ndipo zikukhudza bwanji a “nkhosa zina”? (Yoh. 10:16) Nkhaniyi ikuthandizani kuona chifukwa chake muyenera kusangalala ndi chiyembekezo chanucho komanso kuyembekezera mwachidwi kukwaniritsidwa kwake.
NKHANI YOPHUNZIRA 4 TSAMBA 25-29
Yesu anachenjeza kuti: “Kumbukirani mkazi wa Loti.” (Luka 17:32) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Nkhaniyi ifotokoza mbali zitatu zimene tiyenera kutsatira chenjezo limeneli. Mwinatu pa mbali zimenezi pali mbali imodzi kapena zingapo zimene muyenera kusintha kuti mutsatire bwinobwino chenjezoli.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 “Kudzanja Lanu Lamanja Kuli Chimwemwe Mpaka Muyaya”
7 Kodi Mumatani Ena Akakupemphani Malangizo?
30 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
PATSAMBA LOYAMBA: Achinyamata ambiri ku Malawi amalalikira kwa anzawo kusukulu ndipo amawafotokozera mfundo zosangalatsa ndiponso zofunika kwambiri za m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa
MALAWI
KULI ANTHU OKWANA
13,077,160
KULI OFALITSA OKWANA
79,157
NYUMBA ZA UFUMU ZIMENE ZAMANGIDWA
1,031 kuyambira mu 1998