Zamkatimu
April 15, 2012
© 2012 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA
MAY 28, 2012–JUNE 3, 2012
‘Mwana Amakonda Kuululira Ena za Atate’
TSAMBA 3 • NYIMBO: 106, 112
JUNE 4-10, 2012
Kusakhulupirika Ndi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza
TSAMBA 8 • NYIMBO: 63, 32
JUNE 11-17, 2012
Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu
TSAMBA 13 • NYIMBO: 52, 57
JUNE 18-24, 2012
Yehova Amadziwa Kupulumutsa Anthu Ake
TSAMBA 22 • NYIMBO: 133, 131
JUNE 25, 2012–JULY 1, 2012
Yehova Amatiteteza Kuti Tidzapulumuke
TSAMBA 27 • NYIMBO: 110, 60
CHOLINGA CHA NKHANI ZOPHUNZIRA
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 3-7
Kodi Yesu anaulula za Atate kwa ophunzira ake ndiponso ena m’njira ziwiri ziti? Nanga tingatsanzire bwanji Yesu poululira ena za Atate wake? Nkhani iyi idzatithandiza kuyankha mafunsowa.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 TSAMBA 8-12
Kusakhulupirika kwafala kwambiri m’dzikoli. Koma tisalole kuti kusakhulupirikako kusokoneze mtendere ndiponso mgwirizano zimene Akhristufe tili nazo m’banja komanso mu mpingo. Nkhani iyi ikusonyeza kuti tingapitirize kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndiponso kwa anzathu.
NKHANI YOPHUNZIRA 3 TSAMBA 13-17
Kodi timasonyeza bwanji kuti tikutumikira Yehova ndi mtima wathunthu? Kodi tiyenera kuteteza mtima wathu ku chinthu choopsa chiti? N’chiyani chingatithandize kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wathunthu? Mayankho a mafunsowa ali m’nkhani imeneyi.
NKHANI ZOPHUNZIRA 4, 5 TSAMBA 22-31
Pa “chisautso chachikulu” anthu a Mulungu adzaukiridwa moopsa. (Mat. 24:21) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova adzatipulumutsa? Kodi amatithandiza bwanji kuti tipitirize kukhala okhulupirika n’kumayembekeza mapeto a dzikoli? Mudzapeza mayankho olimbitsa chikhulupiriro m’nkhani zimenezi.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
18 Ndagwira Chovala cha Myuda kwa Zaka Zoposa 70
PATSAMBA LOYAMBA: Mlongo akupereka kabuku ka chinenero cha Inuktitut ali kudera la chipale chofewa ku Frobisher Bay mumzinda wa Iqaluit kuchigawo cha Nunavut m’dziko la Canada
CANADA
KULI ANTHU OKWANA
34,017,00
KULI OFALITSA OKWANA
113,989
NTCHITO YOMASULIRA MABUKU
Nthambi ya ku Canada imayang’anira ntchito yomasulira mabuku m’zinenero 12 za kumeneko