Zamkatimu
January 15, 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
MAGAZINI YOPHUNZIRA
FEBRUARY 25, 2013–MARCH 3, 2013
Ukhale Wolimba Mtima Chifukwa Yehova Ali Nawe
TSAMBA 7 • NYIMBO: 60, 23
MARCH 4-10, 2013
Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi Yehova
TSAMBA 12 • NYIMBO: 106, 51
MARCH 11-17, 2013
TSAMBA 17 • NYIMBO: 52, 65
MARCH 18-24, 2013
Tumikirani Yehova Popanda Kunong’oneza Bondo
TSAMBA 22 • NYIMBO: 91, 39
MARCH 25-31, 2013
Akulu Achikhristu Ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe
TSAMBA 27 • NYIMBO: 123, 53
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Ukhale Wolimba Mtima Chifukwa Yehova Ali Nawe
Anthu ambiri a m’Baibulo anasonyeza chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima. Kuganizira zitsanzo zawo kungatithandize kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kutumikira Yehova molimba mtima. Nkhaniyi ikufotokoza za lemba lathu la chaka cha 2013.
▪ Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi Yehova
▪ Pitirizani Kuyandikira Yehova
Pali zinthu zambiri pa moyo zomwe sitingathe kusankha. Mwachitsanzo, sitingathe kusankha makolo athu, abale athu kapena kumene tingabadwire. Koma n’zosiyana pa nkhani ya ubwenzi wathu ndi Yehova. Tikhoza kusankha kumuyandikira kapena ayi. Nkhanizi zikufotokoza zinthu 7 zimene zikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.
▪ Tumikirani Yehova Popanda Kunong’oneza Bondo
Tonsefe tachita zinthu zina zimene timanong’oneza nazo bondo. Koma tisalole zimenezi kutisokoneza potumikira Mulungu. M’nkhaniyi, tiphunzira mmene tingatsatirire chitsanzo cha mtumwi Paulo popitiriza kutumikira Yehova popanda kunong’oneza bondo.
▪ Akulu Achikhristu Ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe
M’kalata yake yachiwiri yopita kwa Akorinto, Paulo anafotokoza kuti iye ndi anzake apamtima anali ‘antchito anzawo kuti akhale ndi chimwemwe.’ (2 Akor. 1:24) Kodi mawu a Paulo amenewa angathandize bwanji akulu achikhristu? Kodi aliyense wa ife angathandize bwanji kuti anthu mu mpingo akhale achimwemwe? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Norway
32 Anabala Zipatso Chifukwa Chokonzekera Bwino
TSAMBA LOYAMBA: Banja lina limene linapuma pa ntchito likuchititsa phunziro la Baibulo pakhonde la nyumba ina mumzinda wa Camp Perrin. Anthu ena a ku Haiti amene anali kukhala kudziko lina, ngati banjali, abwerera kwawo ku Haiti kuti atumikire kumene kulibe ofalitsa okwanira
HAITI
WOFALITSA ALIYENSE KU HAITI AYENERA KULALIKIRA ANTHU
557
KULI OFALITSA
17,954
MAPHUNZIRO A BAIBULO
35,735