Zamkatimu
March 15, 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
MAGAZINI YOPHUNZIRA
APRIL 29, 2013–MAY 5, 2013
Anthu Okonda Yehova ‘Alibe Chowakhumudwitsa’
TSAMBA 3 • NYIMBO: 45, 32
MAY 6-12, 2013
Kodi Muli ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?
TSAMBA 8 • NYIMBO: 62, 60
MAY 13-19, 2013
Popeza “Mwadziwa Mulungu,” Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?
TSAMBA 13 • NYIMBO: 81, 135
MAY 20-26, 2013
TSAMBA 19 • NYIMBO: 51, 95
MAY 27, 2013–JUNE 2, 2013
Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova
TSAMBA 24 • NYIMBO: 27, 101
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Anthu Okonda Yehova ‘Alibe Chowakhumudwitsa’
Akhristu onse ali pa mpikisano wokalandira mphoto ya moyo wosatha. Koma popeza ndife opanda ungwiro, timapunthwa. M’nkhaniyi tikambirana zinthu zisanu zimene zingatipunthwitse. Ifotokozanso mmene tingapewere zinthu zimenezi kuti tipambane mpikisanowu.
▪ Kodi Muli ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?
Buku la Yeremiya limatiuza zambiri pa nkhani ya mtima wophiphiritsa. Nkhaniyi itithandiza kudziwa ‘mtima wosadulidwa’ komanso kuopsa kokhala ndi mtima wotero ngakhale kwa Akhristu. Itithandizanso kudziwa zimene tingachite kuti tikhale ndi “mtima wodziwa” Yehova.—Yer. 9:26; 24:7.
▪ Popeza “Mwadziwa Mulungu,” Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?
Kodi munthu amachita zinthu ziti kuti adziwe Mulungu komanso kuti adziwidwe ndi Mulunguyo? N’chifukwa chiyani munthu afunika kukulabe ngakhale atakhala m’choonadi kwa zaka zambiri ndipo angachite bwanji zimenezi? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa.
▪ Yehova Ndi Malo Athu Okhalamo
Ngakhale kuti tikukhala m’dziko loipa sitiyenera kuchita mantha. Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova Mulungu amateteza anthu ake nthawi zonse.
▪ Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova
Kodi kudziwika ndi dzina la Mulungu kumatanthauza chiyani? Nanga kuyenda m’dzinali kumatanthauza chiyani? Kodi Mulungu amaona bwanji anthu amene amanyoza dzina lake? Nkhaniyi ili ndi mayankho a mafunso amenewa.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
29 Kodi Josephus Analembadi Zimenezi?
PATSAMBA LOYAMBA: Dziko la Finland lili m’mphepete mwa nyanja ndipo lili ndi zilumba zambiri. Kulinso nyanja zambiri makamaka kudera la pakati ndiponso kum’mawa kwa dzikoli. Ofalitsa akamapita kukalalikira kumadera amene kulibe ofalitsa ambiri amayenda pa boti
FINLAND
KULI ANTHU:
5,375,276
WOFALITSA ALIYENSE AYENERA KULALIKIRA ANTHU:
283
KULI APAINIYA OKHAZIKIKA:
1,824