Zamkatimu
January 15, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
MAGAZINI YOPHUNZIRA
MARCH 3-9, 2014
Lambirani Yehova, Mfumu Yamuyaya
TSAMBA 7 • NYIMBO: 106, 46
MARCH 10-16, 2014
Kodi Ufumu Umene Walamulira kwa Zaka 100 Umakukhudzani Bwanji?
TSAMBA 12 • NYIMBO: 97, 101
MARCH 17-23, 2014
Achinyamata, Muzisankha Zochita Mwanzeru
TSAMBA 17 • NYIMBO: 41, 89
MARCH 24-30, 2014
Tumikirani Yehova Masiku Oipa Asanafike
TSAMBA 22 • NYIMBO: 54, 17
MARCH 31, 2014–APRIL 6, 2014
Kodi Ufumu wa Mulungu Ubwera Liti?
TSAMBA 27 • NYIMBO: 108, 30
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Lambirani Yehova, Mfumu Yamuyaya
Nkhaniyi ititsimikizira kuti Yehova wakhala Mfumu kuyambira kale. Itithandiza kudziwa mmene Yehova wasonyezera kuti ndi Mfumu kwa angelo ndiponso anthu. Itilimbikitsanso kutsatira zitsanzo za anthu akale amene anasankha kulambira Yehova, yemwe ndi Mfumu yamuyaya.
▪ Kodi Ufumu Umene Walamulira kwa Zaka 100 Umakukhudzani Bwanji?
Nkhaniyi itithandiza kumvetsa bwino zimene Ufumu wa Mesiya wachita pa zaka 100 zoyambirira zimene wakhala ukulamulira. Itilimbikitsanso kugonjera mokhulupirika Ufumuwu komanso itithandiza kuganizira kwambiri tanthauzo la lemba lathu la chaka cha 2014.
▪ Achinyamata, Muzisankha Zochita Mwanzeru
▪ Tumikirani Yehova Masiku Oipa Asanafike
Kodi ndidzachita chiyani pa moyo wanga? Munthu aliyense amene wadzipereka kwa Yehova ayenera kudzifunsa funsoli. Nkhanizi zikufotokoza mfundo zimene zingathandize Akhristu achinyamata kuchita zambiri potumikira Mulungu. Ikusonyezanso kuti Akhristu achikulire ali ndi mwayi wochita zambiri mu utumiki.
▪ Kodi Ufumu wa Mulungu Ubwera Liti?
Masiku ano, anthu ambiri amasokonezedwa ndi zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli kapena ndi zinthu zimene iwowo akuchita. Nkhaniyi ikufotokoza zifukwa zitatu zotsimikizira Akhristu kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uwononga dziko loipali.
M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI
PATSAMBA LOYAMBA: Akulalikira anthu ochokera kumayiko ena amene akuphunzira payunivesite ina mumzinda wa Lviv
UKRAINE
KULI ANTHU OKWANA
45,561,000
KULI OFALITSA OKWANA
150,887
Kuli mipingo 1,737 ndiponso magulu 373 mu zinenero 15. Zinenerozi zikuphatikizapo Chihangare, Chiromaniya, Chirasha, chinenero chamanja cha Chirasha ndiponso Chiyukireniya