Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 3/1 tsamba 6
  • Mwambo Womwe Simuyenera Kuuphonya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwambo Womwe Simuyenera Kuuphonya
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu Udzachitika Liti?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Tizikumbukira Bwanji Imfa ya Yesu?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 3/1 tsamba 6
Yesu watambasula dzanja lake kukuitanirani ku Chikumbutso

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI ZINTHU ZITI ZIMENE MULUNGU WAKUCHITIRANI?

Mwambo Womwe Simuyenera Kuuphonya

Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu analamula ophunzira ake kuti azichita mwambo wokumbukira imfa yake. Yesu anagwiritsa ntchito mkate wopanda chofufumitsa komanso vinyo wofiira, ndipo anayambitsa mwambo umene umatchedwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Iye analamula ophunzira ake kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—Luka 22:19.

Chaka chilichonse, pa tsiku limene Yesu anayambitsa mwambowu, Mboni za Yehova padziko lonse zimasonkhana kuti zikumbukire imfa ya Yesu. Chaka chino, mwambowu udzachitika Lolemba pa April 14, dzuwa litalowa.

Tikukuitanani kuti mudzapezeke pa mwambo umenewu. Padzakambidwa nkhani imene idzafotokoze kufunika kwa nsembe ya Yesu. Simudzalipira chilichonse pa mwambowu, ndipo sipadzayendetsedwa mbale ya zopereka. Mungafunse munthu amene wakupatsani magaziniyi kuti mudziwe nthawi komanso malo amene mwambowu udzachitikire m’dera lanu, kapena mungapite pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Tikukupemphani kuti mulembe deti limene mwambo umenewu udzachitike kuti musadzalephere kupezekapo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena