Zamkatimu
August 15, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAGAZINI YOPHUNZIRA
SEPTEMBER 29, 2014–OCTOBER 5, 2014
Akazi Amathandiza Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova
TSAMBA 6 • NYIMBO: 86, 104
OCTOBER 6-12, 2014
Muzigwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu Chifukwa Ndi Amoyo
TSAMBA 11• NYIMBO: 114, 101
OCTOBER 13-19, 2014
Zimene Yehova Wachita Kuti Tiyandikane Naye
TSAMBA 16 • NYIMBO: 51, 91
OCTOBER 20-26, 2014
Muzimva Mawu a Yehova Nthawi Zonse
TSAMBA 21 • NYIMBO: 26, 89
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Akazi Amathandiza Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova
M’nkhaniyi muona kuti zimene zinachitika m’Munda wa Edeni zakhudza amuna ndi akazi onse. Muonanso zimene akazi oopa Mulungu akale anakumana nazo. Komanso muona zimene akazi achikhristu masiku ano amachita pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.
▪ Muzigwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu Chifukwa Ndi Amoyo
Wofalitsa aliyense amafunitsitsa kuti aziphunzitsa mogwira mtima mu utumiki. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zina zomwe zingatithandize kugwiritsa ntchito Baibulo ndiponso timapepala pokambirana ndi anthu. Tikatero tiziwafika pamtima ndi Mawu a Yehova, omwe ndi amoyo.
▪ Zimene Yehova Wachita Kuti Tiyandikane Naye
Timafunikira kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wathu. Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova wapereka dipo komanso Mawu ake chifukwa chofunitsitsa kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino.
▪ Muzimva Mawu a Yehova Nthawi Zonse
Tiyenera kumvetsera mawu a Yehova kuti tiziyenda m’njira ya choonadi. M’nkhaniyi tiphunzira zimene tingachite kuti tizimvetsera mawu a Yehova ngakhale kuti Satana akuyesetsa kutisokoneza komanso tikulimbana ndi zilakolako zoipa. Nkhaniyi itithandizanso kudziwa kuti kupemphera kwa Mulungu woona n’kofunika kwambiri.
M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI
3 Kodi Mukulandira “Chakudya pa Nthawi Yoyenera?”
26 ‘Ubwerere Ukalimbikitse Abale Ako’
29 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
31 Kale Lathu
PATSAMBA LOYAMBA: Alongo akulalikira mu Chirasha m’mphepete mwa nyanja mumzinda wa Tel-Aviv. Kumbuyo kwawo kuli mapiri a m’dera la Jaffa kumene kunali doko lakale la Yopa
ISRAEL
KULI ANTHU
8,050,000
CHIWERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OFALITSA MU 2013
1,459
OPEZEKA PA CHIKUMBUTSO MU 2013
2,671