Zamkatimu
September 15, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAGAZINI YOPHUNZIRA
OCTOBER 27, 2014–NOVEMBER 2, 2014
N’chiyani Chimakutsimikizirani Kuti Muli M’gulu la Yehova?
TSAMBA 7 • NYIMBO: 28, 107
NOVEMBER 3-9, 2014
Tumikirani Mulungu Mokhulupirika Pokumana ndi “Masautso Ambiri”
TSAMBA 12 • NYIMBO: 135, 133
NOVEMBER 10-16, 2014
Makolo, Muzisamalira Bwino Ana Anu
TSAMBA 17 • NYIMBO: 88, 24
NOVEMBER 17-23, 2014
Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa
TSAMBA 23 • NYIMBO: 111, 109
NOVEMBER 24-30, 2014
Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse
TSAMBA 28 • NYIMBO: 95, 100
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ N’chiyani Chimakutsimikizirani Kuti Muli M’gulu la Yehova?
Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zimene zimachititsa anthu ambiri kutsimikizira kuti Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni. Tionanso zimene zimachititsa abale ndi alongo ena kutsimikizira kuti alidi m’gulu la Yehova.
▪ Tumikirani Mulungu Mokhulupirika Pokumana ndi “Masautso Ambiri”
M’dziko la Satanali timakumana ndi masautso ambiri. Masautso ena amabwera chifukwa cha kuzunzidwa koma ena ndi ovuta kuwazindikira. Nkhaniyi itithandiza kuzindikira masautsowa komanso kukonzekera misampha ya Satana.
▪ Makolo, Muzisamalira Bwino Ana Anu
Makolo ayenera kulera ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zitatu zimene angachite kuti azisamalira bwino ana awo.
▪ Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa
Kodi imfa inayamba bwanji? Nanga mdani ameneyu adzawonongedwa bwanji? (1 Akor. 15:26) Nkhaniyi ikuyankha mafunso amenewa ndipo ikusonyeza kuti Yehova ndi wachilungamo, wanzeru komanso wachikondi.
▪ Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse
Pali anthu ambiri amene akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse ngakhale kuti amakumana ndi mavuto m’dziko loipali. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakumbukira ‘ntchito zawo zachikhulupiriro ndiponso zachikondi’?—1 Ates. 1:3.
M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI
PATSAMBA LOYAMBA: Abale awiri akulalikira msodzi m’mphepete mwa nyanja mumzinda wa Negombo ku Sri Lanka
SRI LANKA
KULI ANTHU
20,860,000
KULI OFALITSA
5,600
APAINIYA OKHAZIKIKA
641