Zamkatimu
January 15, 2015
© 2015 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAGAZINI YOPHUNZIRA
MARCH 2-8, 2015
Yamikani Yehova Ndipo Adzakudalitsani
TSAMBA 8 • NYIMBO: 2, 75
MARCH 9-15, 2015
N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
TSAMBA 13 • NYIMBO: 8, 109
MARCH 16-22, 2015
Limbitsani Banja Lanu Kuti Likhale Losangalala
TSAMBA 18 • NYIMBO: 36, 51
MARCH 23-29, 2015
Lolani Kuti Yehova Alimbitse Ndiponso Kuteteza Banja Lanu
TSAMBA 23 • NYIMBO: 87, 50
MARCH 30, 2015–APRIL 5, 2015
Kodi N’zotheka Kukondana Mpaka Kalekale?
TSAMBA 28 • NYIMBO: 72, 63
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Yamikani Yehova Ndipo Adzakudalitsani
Kuti tikhalebe ndi mtima woyamikira, tiyenera kuganizira madalitso amene Yehova watipatsa ndiponso kumuthokoza. Mtimawu ukhoza kutisiyanitsa ndi anthu osayamika komanso ungatithandize kuti tipirire mavuto. Lemba la chaka cha 2015 litithandiza kuti tizikumbukira kuyamika Yehova.
▪ N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
Nkhaniyi ikufotokoza bwino chifukwa chimene timachitira mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Kodi mkate ndi vinyo zimaimira chiyani? Kodi munthu angadziwe bwanji kuti ndi woyenera kudya mkate ndiponso kumwa vinyo? Nanga tingakonzekere bwanji mwambowu? Nkhaniyi iyankha mafunso onsewa.
▪ Limbitsani Banja Lanu Kuti Likhale Losangalala
▪ Lolani Kuti Yehova Alimbitse Ndiponso Kuteteza Banja Lanu
Mabanja ambiri akukumana ndi mavuto komanso amayesedwa. Koma Yehova akhoza kuthandiza anthu kukhala ndi banja lolimba komanso losangalala. Nkhani yoyamba ikufotokoza zinthu 5 zimene zingathandize kuti banja likhale lolimba komanso losangalala ndipo ikusonyeza kuti chikondi n’chofunika kwambiri m’banja. Nkhani yachiwiri ikusonyeza zimene mwamuna ndi mkazi angachite kuti ubwenzi wawo m’banja komanso ndi Yehova ukhale wolimba.
▪ Kodi N’zotheka Kukondana Mpaka Kalekale?
Kodi mungafotokoze bwanji chikondi chenicheni chimene chimakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi? Kodi n’zotheka kukondana mpaka kalekale? Kodi anthu angasonyezane bwanji chikondichi? Nkhaniyi ikufotokoza chikondi chenicheni ndipo yachokera m’buku la Nyimbo ya Solomo.
M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IYI
PATSAMBA LOYAMBA: Akugwiritsa ntchito Baibulo polalikira ku Grindelwald, ndipo mapiri okongola akuoneka chapafupi
SWITZERLAND
KULI ANTHU
7,876,000
KULI OFALITSA
18,646
OPEZEKA PA CHIKUMBUTSO (2013)
31,980