Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 11/15 tsamba 13
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhondo ya Yeriko—Nthano Kapena Yeniyeni?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi “Chipangano Chakale” Nchokhulupirika Motani?
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Tizikhulupirira Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wathu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/15 tsamba 13
Ansembe akuimba nyanga za nkhosa, Yoswa akufuula ndipo mzinda wa Yeriko ukugwa

MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA

Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti mzinda wakale wa Yeriko unagonjetsedwa m’kanthawi kochepa?

Lemba la Yoswa 6:10-15, 20 limasonyeza kuti Aisiraeli anayenda mozungulira mzinda wa Yeriko kamodzi pa tsiku kwa masiku 6. Koma pa tsiku la 7, anauzungulira maulendo 7. Ndiyeno Mulungu anachititsa kuti mpanda wake wolimba ugwe ndipo Aisiraeli analowa n’kugonjetsa mzindawo. Koma kodi zimene akatswiri ofukula zinthu zakale apeza zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi?

Kale, adani akafuna kugonjetsa mzinda, ankamanga misasa mozungulira mpanda wa mzindawo. Ndiyeno akaulanda ankatenga chuma chonse ndiponso chakudya chimene chatsala. Koma ngati anazungulira mzindawo kwa nthawi yaitali asanaugonjetse, ankapeza kuti chakudya chimene chatsala n’chochepa. Ndiye n’chifukwa chake akatswiri ofukula zinthu zakale sapeza chakudya kapena amapeza chochepa kwambiri m’mabwinja a mizinda ya ku Palesitina. Koma magazini ina inafotokoza kuti: “Kuwonjezera pa mapale, akatswiri anapeza chakudya chambiri ku Yeriko.” Inanenanso kuti: “N’zodabwitsa kwambiri kupeza chakudya chambiri m’mabwinja.”

Baibulo limasonyeza kuti Aisiraeli sanatenge chakudya mumzinda wa Yeriko chifukwa Yehova anawaletsa kutenga chilichonse. (Yos. 6:17, 18) Limasonyezanso kuti Aisiraeli anagonjetsa mzinda wa Yeriko anthu atangokolola kumene. N’chifukwa chake kunali chakudya chambiri. (Yos. 3:15-17; 5:10) Choncho akatswiri ofukula zinthu zakale anapezanso chakudya chambiri kumeneko. Izi zikusonyeza kuti zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi ndi zoona. Aisiraeli anagonjetsadi mzinda wa Yeriko m’kanthawi kochepa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena