Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 11/15 tsamba 14-15
  • Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHITSANZO CHABWINO KWAMBIRI PA NKHANI YA KUPATSA
  • “Ntchitoyi Ndi Yaikulu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Zochuluka Zimene Anali Nazo Zinathandiza Anthu Osowa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/15 tsamba 14-15
Mzimayi akuika khadi la ku banki pamashini otumizira ndalama

Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa

YEHOVA amatipatsa zinthu zambiri. (Yak. 1:17) Timaona umboni wa zimenezi tikayang’ana nyenyezi kumwamba komanso zinthu zokongola padzikoli.—Sal. 65:12, 13; 147:7, 8; 148:3, 4.

Wolemba masalimo wina ankayamikira kwambiri zinthu zimene Mulungu analenga moti anaimba nyimbo yomutamanda. Nanunso muyenera kuti mungagwirizane kwambiri ndi zimene ananena m’nyimboyi, yomwe ili mu Salimo 104. Mawu ena amene ananena ndi akuti: “Ndidzaimbira Yehova moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.” (Sal. 104:33) Kodi inunso mumafunitsitsa kutamanda Yehova?

CHITSANZO CHABWINO KWAMBIRI PA NKHANI YA KUPATSA

Yehova amafuna kuti ifenso tizikhala ndi mtima wopatsa. Iye anatiuzanso zifukwa zomveka zotichititsa kukhala ndi mtima umenewu. Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito mtumwi Paulo kuti alembe malangizo akuti: “Lamula achuma a m’nthawi ino kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale. Uwalamule kuti azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawira ena, ndiponso asunge maziko abwino a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 Tim. 6:17-19.

M’kalata yachiwiri imene Paulo analembera mpingo wa ku Korinto, anafotokoza za maganizo oyenera amene tiyenera kukhala nawo pa nkhani ya kupatsa. M’kalatayo analemba kuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” (2 Akor. 9:7) Kenako, anafotokoza kuti anthu amene amapatsidwa zinthu amathandizidwa ndipo nawonso amene amapereka zinthuzo amadalitsidwa kwambiri.—2 Akor. 9:11-14.

Pomaliza kalata yakeyi, Paulo ananena za umboni wamphamvu wosonyeza kuti Mulungu ali ndi mtima wopatsa. Iye anati: “Tikuyamika Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akor. 9:15) Mphatso imene Paulo ankanenayi ikuphatikiza zinthu zonse zabwino zimene Mulungu watipatsa pogwiritsa ntchito Yesu Khristu. Kunena zoona, timasowa chonena tikaganizira mphatso yamtengo wapatali kwambiri imeneyi.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Yehova ndi Mwana wake amatichitira? Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kukhala ndi mtima wopatsa pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso chuma chathu potumikira Yehova.—1 Mbiri 22:14; 29:3-5; Luka 21:1-4.

Zimene Ena Amapereka Pa Ntchito Yapadziko Lonse

Mofanana ndi nthawi ya Paulo, Akhristu ambiri masiku ano amapanga bajeti kapena kuika kandalama “kenakake pambali” kuti akaponye m’mabokosi a zopereka za “Ntchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse mipingo imatumiza zopereka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha zopereka zanu kumaofesi ngati amenewa. Mungafunse ku ofesi ya nthambi m’dziko lanu kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi. Adiresi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org/ny. Mungapereke zopereka zanu m’njira izi:

ZOPEREKA MWACHINDUNJI

  • Mukhoza kupempha banki yanu kuti ichotse ndalama mu akaunti yanu n’kutumiza ku akaunti imene ofesi ya nthambi imagwiritsa ntchito. M’mayiko ena mukhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito jw.org kapena webusaiti ina.

  • Mukhoza kupereka ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali monga ndolo, mphete ndiponso zibangiri. Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti zinthuzo ndi zopereka.

ZONGOBWEREKA

  • Mungapereke ndalama n’kufotokoza kuti ngati nthawi ina mungadzazifune, mudzaziitanitsa.

  • Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti ndalamazo mwangowabwereka.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mwachindunji, pali njira zinanso zoperekera zinthu zothandiza pa ntchito ya Ufumu padziko lonse. Njira zimenezi zili m’munsimu. Musanasankhe njira iliyonse, muyenera kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziwe njira zimene ndi zotheka m’dziko lanu. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenera kufunsanso anthu odziwa bwino za malamulo ndiponso misonkho.

Inshulansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandire ndalama za inshulansi kapena za penshoni.

Maakaunti a Kubanki: Mukhoza kupereka zinthu monga maakaunti anu a kubanki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, gululi lidzatenge zinthuzi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke ku gulu la Yehova masheya amene muli nawo m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandire masheyawo mukadzamwalira.

Malo Kapena Nyumba: Mungapereke ku gulu la Yehova malo kapena nyumba zoti zingagulitsidwe. Ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.

Kodi mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatsozi? Mungaimbe foni kapena kulemba kalata ku ofesi ya nthambi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena