Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA DECEMBER 26, 2016–JANUARY 1, 2017
4 Tipitirize Kulimbikitsana Tsiku ndi Tsiku
Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolimbikitsa ena. Mtumwi Paulo ankaonanso kuti kulimbikitsana n’kofunika kwambiri. Chitsanzo chawo chingatithandize kuti tizikondana komanso kulimbikitsana kunyumba kwathu komanso ku Nyumba ya Ufumu.
MLUNGU WA JANUARY 2-8, 2017
9 Mawu a Mulungu Amatithandiza Kuti Tizichita Zinthu Mwadongosolo
MLUNGU WA JANUARY 9-15, 2017
14 Kodi Mumaona Kuti Baibulo Ndi Buku Lapadera?
M’nkhanizi tipeza mayankho a mafunso awa: N’chiyani chimathandiza anthu Yehova kuti azichita zinthu mwadongosolo? Kodi tingatani kuti Mawu a Mulungu azitithandiza kuti tizichita zinthu mogwirizana? Nanga tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Yehova ndipo timathandiza gulu lake?
MLUNGU WA JANUARY 16-22, 2017
21 Anthu a Mulungu Anaitanidwa Kuchoka mu Mdima
MLUNGU WA JANUARY 23-29, 2017
26 Anatuluka mu Babulo Wamkulu
Nkhani ziwirizi zikufotokoza nthawi imene anthu a Mulungu anali mu ukapolo wa Babulo wamkulu. Ikufotokozanso zimene odzozedwa anachita cha m’ma 1800 n’cholinga choti amvetse bwino Mawu a Yehova. Tikambirananso zimene Ophunzira Baibulo anachita kuti atuluke mu Babulo Wamkulu. Tionanso nthawi imene ukapolowo unatha.
31 Kale Lathu