Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 March tsamba 32
  • Dzina la M’Baibulo Linapezeka Pamtsuko Wakale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dzina la M’Baibulo Linapezeka Pamtsuko Wakale
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2017
  • Dzina la Mulungu Mkati mwa Nyengo
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Dzina la Mulungu Ndi Ndani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 March tsamba 32
Pamtsuko winawake womwe unaumbidwa zaka 3,000 zapitazo panali mawu achikanani okhala ndi dzina la m’Baibulo

Dzina la M’Baibulo Linapezeka Pamtsuko Wakale

Mtsuko womwe unaumbidwa zaka 3, 000 zapitazo

Mu 2012 anthu ofukula zinthu zakale anapeza mapale a mtsuko winawake womwe unaumbidwa zaka 3,000 zapitazo. Anthuwa anasangalala kwambiri ataona zimene zinalembedwa pamapalewo.

Atalumikiza mapalewo anapeza kuti pamtsukowo panalembedwa mawu achikanani. Mawu ake anali oti: “Esibaala Ben Beda” kutanthauza kuti “Esibaala mwana wa Beda.” Aka kanali koyamba kuti anthu apeze dzinali m’zinthu zakale.

Baibulo limatchulanso munthu wina dzina lake Esibaala. Munthuyu anali mwana wa Mfumu Sauli. (1 Mbiri 8:33; 9:39) Pulofesa wina amene anali m’gulu la ofukulawa anati: “N’zochititsa chidwi kuti dzina loti Esibaala, lomwe limapezeka m’Baibulo lapezekanso pamapalewa ndipo zikusonyeza kuti linkagwiritsidwa ntchito pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Davide.” Apanso zinthu zimene ofukula zakale apeza zatsimikizira kuti Baibulo ndi lolondola.

M’Baibulo, mwana wa Sauli dzina lake Esibaala amatchedwanso Isi-boseti. Izi zikusonyeza kuti mawu oti “baala” anawasintha n’kuika oti “boseti.” (2 Sam. 2:10) N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Ofufuza zinthu zakale amanena kuti wolemba buku la 2 Samueli sanafune kugwiritsa ntchito dzina loti Esibaala poopa kuti anthu aziganizira za mulungu wa mphepo wa Akanani dzina lake Baala. Koma dzina loti Esibaala limapezeka m’buku la 1 Mbiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena