Magazini Yophunzira
MAY 2019
NKHANI ZOPHUNZIRA KUYAMBIRA: JULY 1–AUGUST 4, 2019
© 2019 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Ngati mukufuna kupereka pitani pa donate.jw.org.
Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lolembedwa m’Chichewa chamakono, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.
CHITHUNZI PATSAMBA LOYAMBA:
Makolo ayenera kuteteza ana awo kuti asagwiriridwe. Angachite zimenezi, powaphunzitsa nkhani zokhudza kugonana zogwirizana ndi msinkhu wawo. Iwo ayenera kugwiritsa ntchito zinthu zimene gulu la Mulungu latipatsa pa nkhaniyi. (Onani nkhani yophunzira 19, ndime 19-22)