Bokosi la Mafunso
◼ Kodi wofalitsa wosabatizidwa asanavomerezedwe kuti abatizidwe afunika kukhala akuchita zotani mu utumiki wa kumunda?
Amene amayenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa amakhala atasonyeza kale m’njira zambiri kuti akufunitsitsa kukhala wa Mboni za Yehova. (Sal. 110:3) Kuphunzira kwake Malemba mosamala kwasintha maganizo ake, mtima wake ndiponso moyo wake. Chifukwa chofunitsitsa ndi mtima wonse kusangalatsa Yehova ndi kuchita zofuna Zake, wophunzira Baibulo wakhamayo amasonkhana mokhazikika ndi anthu a Yehova pamisonkhano ya mpingo, yadera ndi yachigawo. (Aheb. 10:24, 25) Kuphatikiza pa kusonkhana mokhazikika pamisonkhano yachikristu imeneyi, ayenera kuti mtima wake wam’limbikitsanso kusonyeza poyera chikhulupiriro chake mwa kuyankha pamisonkhano, ndiponso mwina walembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.—Sal. 40:9, 10; om-CN tsa. 73.
Wophunzira Baibuloyo akaphunzira choonadi, ndiponso akasonyeza kuti amazindikiradi kufunika kwa uthenga wa Ufumu, angakhale ndi mwayi wogwira nawo ntchito ya utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Iyi ndi ntchito yaikulu ya Mboni za Yehova. (Mat. 24:14; 28:19, 20; om-CN tsa. 111) Zikatere, wofalitsa amene amachititsa phunzirolo pamodzi ndi akulu ali ndi udindo waukulu wotsimikizira kuti wophunzirayo akutsatira mfundo za makhalidwe abwino achikristu pamoyo wake. Ayenera kufunitsitsa kukhala wa Mboni za Yehova ndiponso kukonda ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira.—Agal. 6:6; w88-CN 11/15 tsa. 17; om-CN tsa. 98-9, 174.
Pasamadutse nthaŵi yaitali kwambiri kuchokera pamene wophunzira Baibulo wayenerera kuloŵa nafe mu utumiki kudzafika pamene akubatizidwa. Panthaŵi imeneyi ndi woti akuyesetsa kale kutsatira mfundo za makhalidwe abwino achikristu pamoyo wake, koma kuti sanazoloŵerebe kulalikira ndi mpingo. Azipatsidwa nthaŵi yokwanira yoti asonyeze kuti watsimikiza ndi mtima wonse kuti akhala mlaliki wokhazikika ndi wachangu mu utumiki wa kumunda.—Sal. 40:8; Aroma 10:9, 10, 14, 15.
Akafika poti wakonzeka kubatizidwa, mwachionekere adzakhala akulalikira mokhazikika uthenga wabwino kwa anthu ena, akuthera nthaŵi yambiri mu utumiki wa kumunda osati ola limodzi kapena aŵiri pamwezi. (w84 6/1 tsa. 8 ndime 2) Inde, moyo wa munthu aliyense wofuna kubatizidwa uyenera kupendedwa, aone zinthu monga makulidwe ake, zaka zake, zinthu zimene sangathe kuchita ndi zina zotero. Akulu adzafunika kutsatira malangizo awo a patsamba 175 m’buku la Utumiki Wathu akuti: “Chidwi chathu chili pa aja amene mitima yawo yatembenukira kwa Yehova, amenenso amvetsa kwenikweni ziphunzitso zofunika zoyambirira za choonadi cha Baibulo. Limodzi ndi chithandizo chanu chachikondi, amene akukabatizidwawo adzalimbikitsidwa ndi kuthandizidwa kuloŵa utumiki wachikristu ali okonzeka bwino kukwaniritsa ntchito yofunika imeneyo.”—Mat. 16:24; Yoh. 4:34; 1 Pet. 2:21.