Funafunani Mwakhama Maphunziro a Baibulo
1 Pali umboni wowonjezereka wakuti nthaŵi ya dziko lakale lino ikutha. (2 Tim. 3:1-5) Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti miyoyo ya anthu ili pangozi. Komabe, tingathe kuthandiza ena kuti akapulumuke. (Miy. 3:27) Pachifukwa chimenechi tiyenera kuyesayesa mwakhama kuyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo.
2 Pachitika zinthu zambiri zabwino chifukwa chogaŵira mabuku athu ofotokoza za m’Baibulo. Koma chimene anthu akufunika kwambiri ndicho kuwathandiza mwachindunji mwa kuchita nawo phunziro la Baibulo mokhazikika. Kodi tingawathandize motani kuzindikira zimenezi?
3 N’kofunika kumuloŵetsa mwininyumba m’makambiranowo. Khalani atcheru kuzindikira zimene zimam’detsa nkhaŵa. Zokamba zanu zizikhudza zimene amakonda kapena zimene zimam’detsa nkhaŵa. M’sonyezeni mawu a m’buku, bulosha, magazini, kapena thirakiti amene akufotokoza njira yothetsera mavuto a anthu imene Baibulo limanena. Musanachoke, funsani funso limodzi kapena aŵiri amene mukukhulupirira kuti amupangitsa kuyembekeza mwachidwi ulendo wanu wotsatira. Mukadzabweranso, onetsetsani kuti mwamukumbutsa mafunso ameneŵa, ndiyeno gwiritsirani ntchito mabuku kum’thandiza kupeza mayankho a Baibulo.
4 Kuyambitsa kwathu maphunziro ndi kuwachititsa mokhazikika kungasinthe miyoyo ya anthu. Tifunikira kuchita chidwi chenicheni ndi zochita za amene timakumana nawo m’munda kapena mwamwayi. Pamafunika kukonzekera bwino kuti tikulitse pang’onopang’ono chidwi chawo. Pamafunika kuleza mtima kuti tipitirizebe kubwererako kufikira mutawazoloŵeretsa kadyedwe kauzimu. Pamafunika kukonda anthuwo. Tiyenera kufuna ndi mtima wonse kuwathandiza kuti akapulumuke chiwonongeko chimene chili pafupichi. Ntchito yathu yochititsa phunziro la Baibulo tiziitchula m’pemphero nthaŵi zonse kuchokera pansi pa mtima.—1 Ates. 5:17.
5 N’zolimbikitsa kwambiri kuona kuti anthu pafupifupi 11,614 akhala ophunzira obatizidwa m’zaka zitatu zapitazi. (Mat. 28:19, 20) Tsopano tikuchititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 39,756 mwezi uliwonse, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti tikudera nkhaŵa miyoyo ya anthu ena. Bwanji ponena za inu? Kodi mukuyesayesa mwakhama kuchita nawo ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo apanyumba? Kumbukirani kuti, miyoyo yathu ndi ya anthu ena imadalira kukhulupirika kwathu pankhaniyi.—Ezek. 3:17-19.