Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
DZIŴANI IZI: M’miyezi ikubwerayi Utumiki Wathu wa Ufumu udzakhala ndi ndandanda ya Msonkhano wa Utumiki wa mlungu uliwonse. Mipingo ingasinthe moyenera kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Olengeza Ufumu Achangu.” Ngati n’koyenera, gwiritsani ntchito mphindi 15 pa Msonkhano wa Utumiki womaliza musanapite ku msonkhano wachigawo kuti muonenso malangizo oyenera a mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu uno amene akukhudza mpingo wanuwo. M’mwezi wa October, Msonkhano wina wa Utumiki udzakhala wopenda mfundo zazikulu za msonkhano wachigawo. Pokonzekera kukambiranako, tonse tikalembe notsi zofunika kumsonkhano wachigawo, komanso mfundo zenizeni zimene tikufuna kuzigwiritsira ntchito pamoyo wathu ndiponso mu utumiki wakumunda. Tikatero tidzatha kufotokoza mmene tagwiritsira ntchito mfundozo chichokereni kumsonkhano wachigawo. Zidzakhala zolimbikitsa kumva aliyense akunena momwe apindulira ndi malangizo abwino amene tinalandira.
Mlungu Woyambira July 8
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 15: “Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 3.” Ikambidwe ndi woyang’anira wotsogolera. Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: Kukonzekera Kuchita Ulaliki wa Mwamwayi. Kukambirana ndi omvetsera kuchokera m’buku la Utumiki Wathu, masamba 93-4. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba loyambirira m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002, sonyezani zitsanzo ziŵiri kapena zitatu zachidule za momwe mungachitire polalikira mwamwayi kwa munthu wosam’dziŵa, mnansi, wachibale, kapena mnzathu.
Nyimbo Na. 139 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 15
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za ulaliki za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya July 15 ndi Galamukani! ya August 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana naye, akuti “Ndife Akristu kale pano.”—Onani buku la Kukambitsirana, patsamba 19.
Mph. 15: “Kusonkhanitsa Anthu a Zinenero Zonse.” Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2002, tsamba 24. Ngati zili zofunika, fotokozani mwachidule zimene akuchita pampingopo kuti athandize anthu a m’gawolo amene amalankhula zinenero zina, ndipo sonyezani chitsanzo cha zomwe zili mu ndime 4.
Mph. 15: Zifukwa Zomwe Tiyenera Kugwiritsira Ntchito Baibulo mu Utumiki Wathu. Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvetsera. Yesu ankadziŵa Malemba ndipo nthaŵi zambiri pophunzitsa anali kuwatchula. (Luka 24:27, 44-47) Zimene ankaphunzitsa sizinali zake. (Yoh. 7:16-18) N’kofunika kuti ifenso tizigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Mawu a Mulungu ndi amphamvu kwambiri kuposa chilichonse chimene tinganene. (Yoh. 12:49, 50; Aheb. 4:12) Anthu oona mtima amakopeka ndi chilimbikitso ndi chiyembekezo cha m’Malemba. Chikhale cholinga chanu kuŵerengapo lemba pamene mukulalikira. Tchulani kuti mu zitsanzo za ulaliki wa magazini za mwezi uno aikamo kale malemba. Pemphani omvetsera ena kunena momwe akhala akugwiritsirira ntchito Baibulo mu utumiki ndi mmene apindulira pochita zimenezi komanso momwe anthu amene amawalalikirawo apindulira.
Nyimbo Na. 215 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 22
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kholo ndi mwana amene akuyendera limodzi mu utumiki asonyeze momwe tingagwiritsire ntchito mfundo za patsamba 8 pogaŵira magazini a August 1 ndi August 8. M’chitsanzo chimodzi gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda, ndipo m’chitsanzo chinacho gwiritsani ntchito Galamukani! Limbikitsani makolo kuphunzitsa ana awo pang’onopang’ono utumiki.
Mph. 17: “Kulimbikitsana Mwapadera.” Nkhani. Thandizani anthu kuyembekezera mwachidwi ndiponso mosangalala msonkhano wachigawo. Limbikitsani onse kudzapezeka pa zigawo zonse, kuyambira Lachisanu m’maŵa mpaka Lamlungu madzulo.
Mph. 18: ‘Nthaŵi Zonse Tsatirani Chokoma.’ Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani kufunika kotsatira zomwe zakonzedwa pamsonkhanowo kuti tipindule nawo. Fotokozani chifukwa chake tonse tikufunika kukhala anthu akhalidwe.
Nyimbo Na. 61 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 29
Mph. 9: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a July.
Mph. 18: “Khutiritsani Zosoŵa Zanu Zauzimu.” Nkhani komanso kukambirana ndi omvetsera. Pendani chifukwa chake tonse tifunika kumvetsera mwatcheru pamsonkhano. Gogomezerani kufunika kogwiritsa ntchito zimene taphunzira osati kungomva basi. Onani chidziŵitso chomwe chili pamwambapa chokhudza zimene akonza pa Msonkhano wina wa Utumiki mu October, pamene adzapende mfundo zazikulu za msonkhano wachigawo. Limbikitsani onse kukalemba notsi. Pemphani anthu ochepa kunena zimene anapindula pamsonkhano wachigawo wa chaka chatha.
Mph. 18: “Valani ndi Kudzikongoletsa Bwino.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Thandizani onse kuzindikira chifukwa chake kuli kofunika kusamalira maonekedwe athu kumaso kwa anthu.
Nyimbo Na. 81 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 5
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 20: “Khalani Ogwirizana.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3, phatikizanipo ndemanga za mu Galamukani! ya May 8, 2000, masamba 17-19. Pandime 4, phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995, ndime 4-6.
Mph. 15: “Funafunani Mwakhama Maphunziro a Baibulo.” Kukambirana nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Ŵerengani malemba onse osagwidwa mawu ndi kuwagwirizanitsa ndi nkhaniyi. Pendani momwe ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo yayendera pampingopo m’zaka zisanu zapitazo, ndipo konzani mawu omaliza mogwirizana ndi zosoŵa za pampingopo.
Nyimbo Na. 184 ndi pemphero lomaliza.