Misonkhano Yautumiki ya May
Mlungu Woyambira May 2
Mph. 5: Zilengezo za pampingo ndi Zilengezo zoyenerera zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani makonzedwe alionse ofutukulira ntchito ya utumiki wakumunda, onga ntchito ya m’khwalala kapena umboni wa madzulo.
Mph. 15: “Lingalirani za Kukhala ndi Sabusikripishoni Yaumwini.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani ofalitsa aŵiri amene ali ndi sabusikripishoni yanthaŵi yonse kufotokoza mmene ziliri zotheka kwa iwo kukhala ndi masabusikripishoni.
Mph. 10: “Kodi Ndifunikira Kumasinthasintha?” Kukambitsirana kwa akulu aŵiri. Gogomezerani mapindu a kukhala ndi phande nthaŵi zonse muutumiki wakumunda.
Mph. 15: “Gwiritsirani Ntchito Magazini Kuuza Ena Choonadi.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Fotokozani chimene chimachititsa magazini athu kukhala osiyana ndi chifukwa chake zimenezi ziyenera kutisonkhezera kuwagaŵira pa mpata uliwonse. Konzani zitsanzo zachidule ziŵiri.
Nyimbo Na. 128 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 9
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Tiyenera kuzindikira msanga mipata ya kupeza masabusikripishoni. Tingawagaŵire pa nthaŵi iliyonse kwa awo amene timakumana nawo. Nthaŵi zina mungagaŵire masabusikripishoni amiyezi isanu ndi umodzi. Fotokozani mmene mungadzadzire makope atatu a mafomu a sabusikripishoni.
Mph. 20: “Konzekeretsani Ophunzira Baibulo Kaamba ka Utumiki.” Mafunso ndi mayankho. M’ndime 4 ndi 5, khalani ndi chitsanzo chachidule chosonyeza njira yothandizira wophunzira kukonzekera kuchitira umboni pa khomo. Wophunzira ayamba ndi ulaliki wapafupi akumagwiritsira ntchito Salmo 37:11. Mphunzitsi amdula mawu, akumati: “Ndili ndi chipembedzo changa.” Wophunzirayo saali wotsimikiza zoti anene. Aŵiriwo atsegula buku la Kukambitsirana, pa masamba 18-19, kupenda mayankho osonyezedwa, ndi kusankhapo limodzi limene wophunzirayo sakuvutika nalo. Wophunzirayo ayambanso, akuyankha bwino, ndipo alimbikitsidwa ndi zotsatirapo.
Mph. 15: Pindulani ndi 1994 Yearbook. Akumagwiritsira ntchito chidziŵitso chili mu 1994 Yearbook, pa masamba 10-18, mkulu ndi mtumiki wotumikira akukambitsirana nsonga zolimbikitsa zimene zingagwiritsiridwe ntchito kukulitsa chiyamikiro kaamba ka gulu lateokratiki.
Nyimbo Na. 139 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 16
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Ŵerengani lipoti la maakaunti ndi kuyamikira zopereka zilizonse. Perekani lipoti la chiŵerengero cha masabusikripishoni opezedwa m’nyengo imeneyi ya mkupiti. Ngati nthaŵi ilola, funsani mwachidule ena amene anapeza masabusikripishoni. Tchulani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda a pa May 25.
Mph. 17: “Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera.” Mafunso ndi mayankho. Khalani ndi chitsanzo cha ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri osonyezedwa.
Mph. 18: “Kupindula Kwambiri ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu ndi kukambitsirana ndi omvetsera. Limbikitsani onse kulandira ndi kukwaniritsa magawo awo. Gogomezerani kufunika kwa kusaphonya kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu. Fotokozani mmene mpingo wonse ungapindulire ndi uphungu woperekedwa kwa ophunzira.
Nyimbo Na. 53 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 23
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pendani nkhani zapadera m’magazini atsopano, ndipo konzani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri za kugaŵira masabusikripishoni.
Mph. 10: “Kodi Mumalemekeza Ena Popereka Uphungu?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1994, masamba 25-9.
Mph. 25: “Kutumikira Monga Asodzi a Anthu.” Nkhani ndi zitsanzo yokambidwa ndi mkulu wachidziŵitso yochokera mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1992, masamba 12-16. Ofalitsa aŵiri okonzekera bwino achite chitsanzo cha ntchito ya kunyumba ndi nyumba. Pa nyumba yawo yoyamba mwininyumba akuti n’ngwotanganitsidwa, akupita ku misonkhano ya chipembedzo chake. Pa nyumba yawo yachiŵiri mwininyumba akukana kulandira uthengawo chifukwa cha kuganiza kuti iwo amadza kaŵirikaŵiri. Pogwetsedwa ulesi ndi mayankhidwe a anthu m’gawo lawo, ofalitsawo asankha kupereka vutolo kwa mmodzi wa akulu. Mkuluyo akambitsirana nawo nsonga za m’ndime 20 ndi 21 zonena za nthaŵi yoyenerera kusodza anthu ndi zimene ayenera kukumbukira ngati gawo limafoledwa kaŵirikaŵiri.
Nyimbo Na. 19 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 30
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mbiri Yateokratiki.
Mph. 15: Pendani buku logaŵira m’June: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Sumikani maganizo pa zithunzithunzi zokopa. Khalani ndi wofalitsa wokhoza kuti achitire chitsanzo ulaliki wachidule wozikidwa pa tsamba 307, ndime 2, kapena tsamba 310, ndime 1, akumagwiritsira ntchito Chivumbulutso 21:4. Tchulani makonzedwe a utumiki wakumunda a mlungu wotsatira.
Mph. 20: Nkhani pamutu wakuti “Ukwati,” yochokera m’buku la Kukambitsirana, masamba 383-8. Wokamba nkhani ayenera kusankha chabe nsonga zokwanira bwino zimene zingafotokozedwe bwino lomwe m’nthaŵi yogaŵiridwayo.
Nyimbo Na. 12 ndi pemphero lomaliza.