Misonkhano Yautumiki ya July
CHIDZIŴITSO: Utumiki Wathu Waufumu udzandandalitsa Msonkhano Wautumiki wa mlungu uliwonse m’nyengo ya msonkhano wachigawo. Mipingo ingapange masinthidwe ofunikira kuloleza ofalitsa kukafika pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Mantha Aumulungu” ndiyeno kukhala ndi programu ya mphindi 30 ya kupenda mfundo zazikulu pa mlungu wotsatirawo. Kupenda mfundo za tsiku ndi tsiku za programu ya msonkhano wachigawo kumeneko kuyenera kugaŵiridwa pasadakhale kwa abale aŵiri kapena atatu oyenerera amene adzakhala okhoza kusonyeza mfundo zazikulu. Kupenda mfundo zazikulu kumeneku kokonzedwa bwino kudzathandiza mpingo kukumbukira mfundo zazikulu zimene zingagwiritsiridwe ntchito ndi munthu mwini ndi muutumiki wakumunda. Ndemanga za omvetsera ndi zokumana nazo zosimbidwa ziyenera kukhala zachidule ndi zolunjika.
Mlungu Woyambira July 4
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani mitu ya timabuku, ngati tilipo, timene mpingo uli nato mu sitoko; limbikitsani ofalitsa kutipeza kuti akagwiritsire ntchito muutumiki. Ngati mpingo ulibe timabukuto, tchulani mabrosha amene angagwiritsiridwe ntchito.
Mph. 17: “Kunyumba ndi Nyumba Mosalekeza.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani ndemanga zoyamikira za omvetsera ena amene anafikiridwa poyamba kupyolera mu ntchito ya kukhomo ndi khomo.
Mph. 18: “Thandizani Ena Kuphunzira Choonadi.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Linganizani ofalitsa okhoza bwino kuchitira chitsanzo maulaliki aŵiri kapena atatu osonyezedwa. Gogomezerani mapindu a kafikidwe kachidule ndi kosavuta.
Nyimbo Na. 120 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 11
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo. Ŵerengani lipoti la maakaunti ndi ziyamikiro za zopereka zilizonse za ku Sosaite. Yamikirani zoperekazo. (Eks. 35:29) Limbikitsani ofalitsa kulingalira za umboni wamadzulo—nthaŵi yabwino kwambiri ya ntchito ya kukhomo ndi khomo kapena maulendo obwereza.
Mph. 15: Mbali ya Mafunso. Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho. Ndiponso pendani mfundo zazikulu za nkhani yakuti “Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Tchulani madeti a msonkhano wadera wotsatira ngati alipo.
Mph. 18: “Kodi Adzamva Bwanji Ngati Sitibwererako?” Kambitsiranani ndi omvetsera. Chitirani chitsanzo malingaliro a m’ndime 3 ndi 4. Perekani ndemanga zina zosonyeza chifukwa chake maulendo obwereza ayenera kupangidwa ndi chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro.
Nyimbo Na. 123 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 18
Mph. 5: Zilengezo za pamalopo. Fotokozani makonzedwe a utumiki wakumunda a kutha kwa mlungu, ndipo limbikitsani kukhala ndi phande m’kugaŵira magazini.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo Wakuti ‘Mantha Aumulungu’ wa 1994.” Mphatika. Mafunso ndi mayankho pa ndime 1-11, yokambidwa ndi mkulu. Sumikani maganizo kwambiri pa “Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo.”
Mph. 20: “Kupeza Okondwerera Kupyolera mu Umboni wa m’Khwalala Wogwira Mtima.” Woyang’anira utumiki kapena mkulu wina wokhoza amene ali wogwira mtima mu umboni wa m’khwalala akambitsirana nkhaniyo ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu amenenso ali ndi chidziŵitso m’kuchitira umboni wa m’khwalala. Makambitsiranowo angaphatikizepo zokumana nazo ziŵiri kapena zitatu zachidule. Sonyezani mafikidwe ndi magazini atsopano.
Nyimbo Na. 134 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 25
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Mbiri Yateokratiki. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki wa kugaŵira makope atsopano a magazini. Limbikitsani onse kukhala ndi phande m’kugaŵira magazini.
Mph. 15: “Ocheperapo Msinkhu Amafuna Chitsanzo Chabwino.” Mafunso ndi mayankho. Funsani munthu wachichepere mmodzi kapena aŵiri amene ali achitsanzo chabwino. Achititseni kufotokoza kuti ndi zonulirapo zauzimu zotani zimene adziikira ndi mmene zoyesayesa zawo zabweretsera madalitso owonjezereka.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo Wakuti ‘Mantha Aumulungu’ wa 1994.” Mphatika. Nkhani ya pa ndime 12-25, yokambidwa ndi mlembi wa mpingo.
Nyimbo Na. 187 ndi pemphero lomaliza.