Zilengezo
◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. January: Lililonse la mabuku otsatirawa a masamba 192 amene mipingo ingakhale nawo m’sitoko pa 40t limodzi: Boma Lathu Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu; Commentary on the Letter of James; Is the Bible Really the Word of God?; Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?; Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo; Life Does Have a Purpose; Mbiri Yabwino Yokusangalatsani ndi Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo! MUSAODE alionse a mabuku ameneŵa m’Chingelezi ku Sosaite pakuti kulibe m’sitoko. Komabe, Sosaite ili ndi mtokoma waung’ono wa mabuku a Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo! m’Chicheŵa ndipo ameneŵa angaodedwe. Ngati mipingo ilibe alionse a mabuku ali pamwambawo m’sitoko, ingagaŵire buku la Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? February: Buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi lidzagwiritsiridwa ntchito. Mutagaŵira buku limeneli muyenera kupanga maulendo obwereza, ndipo muyenera kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo. March: Revelation—Its Grand Climax At Hand! CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Order (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye angasankhe ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Lengezani ku mpingo mutachita zimenezi.
◼ Chikumbutso cha mu 1996 chidzakhalako pa Lachiŵiri, April 2, dzuŵa litaloŵa. Chilengezo chapasadakhale chimenechi cha tsiku la phwando la Chikumbutso la 1996 chaperekedwa kuti abale apange makonzedwe ofunika a kubwereka maholo ngati pali mipingo ingapo imene imagwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu ndipo ngati afunikira kupeza malo ena.
◼ Kuyambira ndi January 1, 1995, Nsanja ya Olonda ya Chibengali, Chigujarati, Chihindi, ndi Chinepali idzasintha kukhala yakaŵiri pamwezi m’malo mwa kamodzi pamwezi.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda mabaundi voliyumu a The Watchtower ndi Awake! a 1994 pa oda yawo ya mabuku ya December. Mabaundi voliyumu adzakhalako m’Chingelezi. Kufikira atakhalapo ndi kutumizidwa, mabaundi voliyumu ameneŵa adzasonyezedwa monga “Zoyembekezeredwa” pa mainvoisi a mpingo. Mabaundi voliyumu ali zinthu zoodedwa mwapadera.—Onani Mpambo wa Mitengo ya Watch Tower, ndime 19-20.
◼ Mipingo imene imalandira mabuku awo otumizidwa palole ikukumbutsidwa kumapinda ndi kubwezera makatoni opanda kanthu kumene amalandirira mitokoma yawo mwezi uliwonse. Makatoniwo adzagwiritsiridwanso ntchito ndi Sosaite.
◼ Patsogolopa masabusikripishoni onse otumizidwa ku mipingo palole kapena papositi adzalongedzedwa monga magazini ogaŵira. Masabusikripishoni sadzaikidwanso mu envulopu paokhapaokha monga momwe zinaliri kale. Komabe, magazini aliwonse adzakhala ndi dzina la wolembetsa wake. Mtumiki wa magazini adzakhala ndi thayo la kutsegula mtokoma wa masabusikripishoni ndi kuwagaŵira kwa olembetsa.
◼ Zofalitsidwa Zomwe Zilipo:
Chicheŵa: Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona; Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Chingelezi: Watchtower Publications Index 1991-93; Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
◼ Mavidiyo Kaseti Atsopano Omwe Alipo:
Chipwitikizi: The Bible—Accurate History, Reliable Prophecy.