Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogawiridwa kuyambira mlungu wa September 5 kufikira December 19, 1994. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Satana mwamachenjera amakopa anthu kukhutiritsa zikhumbo zachibadwa mwanjira yolakwika. [uw-CN tsa. 65 ndime 9]
2. Sheol, Hade, ndi Gehena zonse zimasonya ku manda a anthu onse. [uw-CN tsa. 72 ndime 6]
3. Popeza kuti kukwaniritsidwa kwa Salmo 110:1, 2 kumafika m’masiku otsiriza a dzikoli, mavesi ameneŵa amatithandiza kumvetsetsa kuti ulosi wa Yesu wonena za mapeto a dongosolo la zinthu sunalekezere pa chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 2/15 tsa. 12 ndime 17.]
4. Kazembe wankhondo amene mtumiki wake anadwala kwa kayakaya sanauze Yesu kuloŵa m’nyumba mwake chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro. [gt-CN mutu 36]
5. “Olamulira adziko” otchulidwa pa Aefeso 6:12 (NW), ndiwo olamulira andale olekanitsidwa ku chiyanjo cha Mulungu. [uw-CN tsa. 63 ndime 4]
6. Anthu mamiliyoni ambiri amene adzaukitsidwa kwa akufa adzaweruzidwa monga mwa ntchito zawo zimene anachita asanafe. [uw-CN tsa. 75 ndime 12]
7. Chifukwa chimene Yesu analetsera aja omwe anachiritsa kumdziŵikitsa chinali chakuti sanafune kuti iye alengezedwe mopokosera. [gt-CN mutu 33]
8. Ubatizo, weniweniwo, ndiwo chitsimikizo cha chipulumutso. [uw-CN tsa. 100 ndime 12]
9. Malangizo a Yesu ponena za kufunika kwa kupereka mapemphero mseri anasonyeza kuti anali kutsutsa mapemphero apoyera. (Mat. 6:5, 6) [gt-CN mutu 35]
10. Malinga ndi Salmo 58:4, mphiri simamva. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani it-1 tsa. 485.]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Kodi kudziŵa kuti Yehova amadyetsa mbalame ndi kuveka maluŵa mokongola kuyenera kuchotsera atumiki ake aumunthu nkhaŵa zotani? [uw-CN tsa. 88 ndime 3]
12. Monga momwe kwafotokozedwera pa Salmo 58:3-5, kodi ndimotani mmene oipa alili ngati njoka? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 10/15 tsa. 31.]
13. Mogwirizana ndi Aefeso 5:3-5, kodi ndi pachifukwa chotani chimene Mkristu wozindikira adzapeŵera nyimbo zina zimene zingakhale ndi malimba okondweretsa, mamvekedwe okoma, kapena maliridwe osonkhezera? [uw-CN tsa. 67 ndime 12]
14. Kodi Baibulo limatanthauzanji pa Chivumbulutso 20:14, pamene limanena kuti Hade “inaponyedwa m’nyanja yamoto”? [uw-CN tsa. 75 ndime 12]
15. Atamva kuti Yesu wachiritsa munthu pa Sabata amene anali wodwala kwa zaka 38, kodi nchifukwa ninji Ayuda anapita kwa Yesu? [gt-CN mutu 29]
16. Kodi nchifukwa ninji awo oimba mlandu Yesu analibe chifukwa cha kumkanira? [gt-CN mutu 30]
17. Kodi kubatizidwa m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera kumatanthauzanji? [uw-CN tsa. 98 ndime 9]
18. Asanasankhe atumwi ake, kodi Yesu anachita chiyani? [gt-CN mutu 34]
19. Kodi “ngaka yake ya Wam’mwambamwamba” yotchulidwa pa Salmo 91:1 nchiyani, ndipo kodi tiyenera kuchitanji kuti tikhalemo? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 12/15 tsa. 12; w86-CN 12/15 tsa. 30.]
20. Kodi Luka 6:24 amatanthauza kuti, kuti munthu akhale wachimwemwe afunikira kukhala wosauka? [gt-CN mutu 35]
Perekani liwu kapena mawu ofunika kukwaniritsa ndemanga zotsatirazi:
21. Monga momwe nkhani ya Yobu ikusonyezera, Satana amanena kuti ifeyo timafuna makamaka chuma ․․․․․․․, ubwino wathu ndi thanzi lathu, ndi kuti cholinga chathu potumikira Mulungu chili ․․․․․․․. [uw-CN tsa. 93 ndime 13]
22. Yesu anatsutsa ․․․․․․․, kumene mwachionekere kunali kwawo m’nyengo ya utumiki wake, akumalengeza kuti: “Dzuŵa la kuweruza, mlandu wake wa ․․․․․․․ udzachepa ndi wako.” [gt-CN mutu 39]
23. Mogwirizana ndi zimene ․․․․․․․ anafotokoza pa Luka 3:16, pa Pentekoste wa 33 C.E., ophunzira a Yesu kwa nthaŵi yoyamba anabatizidwa ndi ․․․․․․․; mu 70 C.E., Ayuda osalapa anabatizidwa ndi ․․․․․․․. [uw-CN tsa. 96 ndime 4]
24. Ubatizo wa Yesu mu ․․․․․․․ unayamba mu 29 C.E. koma sunathe kufikira ․․․․․․․ndi ․․․․․․․. [uw-CN tsa. 97 ndime 6]
25. Pamene Yesu anachiritsa dzanja la mwamuna wina patsiku la Sabata, Afarisi sanakondwere, iwo anachoka nakapangana chiŵembu panthaŵi yomweyo ndi otsatira chipani cha ․․․․․․․ kuti amuphe. Zimenezi zinaphatikizapo ziŵalo za ․․․․․․․ opembedza. [gt-CN mutu 32]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Mwachionekere, “milungu” yotchulidwa mu Salmo 82 ndiyo (Satana ndi ziŵanda; milungu yachikunja ya amitundu; amuna amene anali oweruza a Israyeli). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 12/15 tsa. 29.]
27. Yesu anatamanda Atate wake wakumwamba chifukwa chakuti Mulungu amabisa choonadi chamtengo wapatali chauzimu kwa (anthu osakhala Ayuda; anthu olemera; anzeru ndi ophunzira). [gt-CN mutu 39]
28. Ngati tadwala kapena kutayikidwa chuma chakuthupi, Mdyerekezi amafuna kuti (tilemekeze Yehova ndi kutsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza; tiimbe Mulungu mlandu ndi kukhala osakhulupirika; tipirire monga momwe Yobu anachitira). [uw-CN tsa. 60 ndime 13]
29. Yohane Mbatizi sadzakhala mu Ufumu wakumwamba chifukwa chakuti (sanasankhidwe kukhala mmodzi wa atumwi 12; anakayikira ngati kuti Yesu analidi yemwe akakhazikitsa Ufumu ndi mphamvu zoonekera; anafa Kristu asanachite pangano ndi ophunzira ake, lakuti iwo akakhale olamulira anzake mu Ufumu wake). [gt-CN mutu 38]
30. Pa Salmo 63:3, Davide kwenikweni anali kunena kuti kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova kunali (chinthu chabwino koposa chachiŵiri pa moyo; kwabwino monga moyo; kwamtengo wapatalidi kuposa moyo). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w85-CN 10/1 tsa. 4.]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Sal. 86:1, 2; Mat. 12:8; Luka 6:41, 42; Luka 6:47-49; Aheb. 13:5, 6
31. Mosasamala kanthu za kukwera kwa mitengo ndi kufalikira kwa ulova, malinga ngati tiyesayesa mwamphamvu mogwirizana ndi chikhulupiriro chathu, Yehova adzatsimikizira kuti tikupeza zimene tikufunikiradi. [uw-CN tsa. 89 ndime 6]
32. Monga Akristu oona tifunikira kupeŵa kukhala osuliza ena kwambiri, kukuza zolakwa zawo ndi kumangowafuna zifukwa, popeza kuti limeneli ndi tchimo lowopsa. [gt-CN mutu 35]
33. Ngakhale kuti tingavutike ndi nkhaŵa ndi kupsinjika maganizo chifukwa cha kupanikizika ndi mavuto, tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzatchera khutu ndi kumvetsera mapemphero athu odzichepetsa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 12/15 tsa. 9 ndime 3, 4.]
34. Kuti tikhale alankhuli apoyera abwino, tifunikira kugwiritsira ntchito zitsanzo zosavuta ndi zinthu zimene anthu amadziŵa. [gt-CN mutu 35 ndime 1-6]
35. Yesu Kristu ndiye Mfumu ya Ufumu wamtendere wa zaka chikwi. [gt-CN mutu 31]
S-97-CN-ZAM & MAL #284 12/94