Misonkhano Yautumiki ya June
Mlungu Woyambira June 5
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kambani nkhani yakuti “Kodi Mudzatamanda Yehova m’Nyimbo?”
Mph. 15: “Yehova Amapereka Mphamvu.” Mafunso ndi mayankho. Simbani chokumana nacho cha mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1992, tsamba 32.
Mph. 18: “Kulitsani Chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene munthu angagwiritsirire ntchito maulaliki osonyezedwawo. Phatikizanipo malingaliro ena achidule onena za mmene munthu angapangire ulendo wobwereza, kwa amene anagaŵirako Uthenga wa Ufumu mu April ndi May.
Nyimbo Na. 17 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 12
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 17: “Kristu Monga Chitsanzo cha Achichepere.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanimo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1986, masamba 4-6.
Mph. 18: “Thandizani Awo Amene Ali Opanda Chikhulupiriro.” Wochititsa Phunziro Labuku Lampingo akukambitsirana nkhaniyo ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu ndiyeno akulongosola mmene angagwiritsirire ntchito nkhaniyi. Akuyeseza maulalikiwo mwa kulalikirana.
Nyimbo Na. 122 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 19
Mph. 8: Zilengezo za pamalopo. Sonyezani maulaliki achidule aŵiri kapena atatu amagazini amene angagwiritsiridwe ntchito mu utumiki wakumunda mlungu uno.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa 1995 wa ‘Atamandi Achimwemwe.’” Kufola ndime 1-17 mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 17: “Gwiritsirani Ntchito Bwino Nthaŵi Yanu.” Mafunso ndi mayankho. Pamene mufotokoza za nthaŵi imene imatheredwa kuonerera TV, fotokozani malingaliro a pamutu waung’ono wakuti “Kulamulira,” patsamba 25 la Galamukani! wa June 8, 1991.
Nyimbo Na. 208 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 26
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo. Pendani mabuku ogaŵira mu July. Fotokozani mbali zapadera za mabrosha amene mpingo uli nawo m’sitoko. Itanani ofalitsa ena kudzasonyeza chitsanzo cha mmene angagaŵiridwire pakhomo. Zitsanzo: Kodi Mulungu Amatisamaliradi? (Tsegulani pamasamba 26-7, sonyezani zithunzithunzi, ndipo kambitsiranani za lemba limodzi lonena za Paradaiso amene akudzayo.) Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? (Tsegulani pamasamba 30-1, kambitsiranani za limodzi la malemba ogwidwa mawuwo, ndipo fotokozani za chithunzithunzi.) Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. (Tembenukirani pamafunso odzutsidwa patsamba 2, ndiyeno kambani pang’ono pa malingaliro otonthoza a m’Malemba opezedwa patsamba 31.) Dziŵitsani mpingo za mabrosha amene ali m’stoko pakali pano.
Mph. 13: Bokosi la Mafunso. Mafunso ndi mayankho, yokambidwa ndi wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Fotokozani mfundo zina zozikidwa mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 91-2.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa 1995 wa ‘Atamandi Achimwemwe.’” Kufola ndime 18-29 mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani za “Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo.” Ngati nthaŵi ilola, fotokozani mfundo zofunika kuchokera mu nkhani yakuti “Kufeŵetsa Zinthu pa Msonkhano,” imene inali mu Utumiki Wathu Waufumu wa March 1995.
Nyimbo Na. 225 ndi pemphero lomaliza.