Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu August: Buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kapena lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32 lingagwiritsiridwe ntchito: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” September: Tidzagwiritsira ntchito buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Tiyenera kuyambitsa maphunziro a Baibulo. October: Masabusikripishoni a Galamukani! kapena Nsanja ya Olonda kapena zonse ziŵiri. November: Gaŵirani buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene siinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambazo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Tili okondwa kulengeza kuti kuyambira pa September 1, 1995, Ofesi ya Nthambi idzayamba kugwira ntchito muno m’Malaŵi ndipo idzakhala mu Lilongwe ku Area 10 plot 390. Makalata onse opita ku Sosaite ayenera kulemberedwa ku Watch Tower Society, Box 30749 Lilongwe 3. Pa Ofesi ya Nthambi padzakhala chipinda cha mabuku odzitengera.
◼ Kuyambira pa August 28 mpaka September 3, Sosaite idzakhala ikuŵerengera mabuku onse m’sitoko ku Beteli. Chifukwa cha kuŵerengera kumeneku, palibe maoda ampingo alionse amene adzakonzedwa kuti atumizidwe kapena kudzatengedwa m’masikuwo. Chonde dziŵaninso kuti Chipinda cha Mabuku cha Beteli chidzatsekedwa pa masikuwo, motero mabuku sadzagulitsidwa kwa abale amene adzafika.
◼ Mafomu okwanira ogwiritsira ntchito m’chaka chautumiki cha 1996 akutumizidwa kumpingo uliwonse. Mafomu ameneŵa sayenera kugwiritsiridwa ntchito mosasamala. Ayenera kugwiritsiridwa ntchito pa chifuno chake chabe.
◼ Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-AB-18). Mlembi wa mpingo ayenera kuonana ndi mtumiki wa mabuku kuchiyambi kwa August ndi kuika tsiku la kuŵerengera mabuku a m’sitoko ya mpingo kumapeto kwa mweziwo. Kuŵerenga kwenikweni kuyenera kuchitidwa pa mabuku onse amene ali m’sitoko, ndipo ziwonkhetso ziyenera kulembedwa pa fomu ya Kuŵerengera Mabuku. Chiwonkhetso cha magazini amene alipo chingapezedwe kwa mtumiki wa magazini. Chonde tumizani kope loyamba ku Sosaite mosapyola pa September 6. Sungani kope lachiŵiri m’faelo yanu. Kope lachitatu lingagwiritsiridwe ntchito monga loŵerengererapo. Kuŵerengerako kuyenera kuyang’aniridwa ndi mlembi, ndipo fomu yodzazidwa iyenera kupendedwa ndi woyang’anira wotsogoza. Mlembi ndi woyang’anira wotsogoza adzasaina fomuyo.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1996 pa oda yawo ya mabuku ya September. Makalendawo adzakhalapo m’Chicheŵa, Chingelezi ndi Chiŵemba.
◼ Mu August mpingo uliwonse udzalandira makope aŵiri a Lipoti la Kulongosola Ntchito za Mpingo (S-10). Komiti Yautumiki iyenera kutsimikizira kuti mafomu ameneŵa adzazidwa molondola ndi kutumizidwa ku Sosaite isanafike September 10. Chaka chatha mipingo 247 siinatumize malipoti awo.
◼ Tikufuna kudziŵitsa pasadakhale apainiya okhazikika onse amene akhala pampambo kuchokera pa October 1, 1994, kapena kumbuyoko, ndipo sanaloŵebe Sukulu Yautumiki Waupainiya kuti sukuluyo idzachitidwa mu October 1995. Chonde pangani makonzedwe otsimikizirika akudzaloŵa Sukulu Yautumiki Waupainiya mu October. Kumbuyoku, ena anaphonya makonzedwe ameneŵa popanda chifukwa chenicheni. Sitikufuna kuti mpainiya aliyense adzaphonye sukulu imeneyi. Tidzakutumizirani chidziŵitso chowonjezereka kupyolera mwa woyang’anira dera.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Imbirani Yehova Zitamando (Lalikulu ndi laling’ono)—Chicheŵa
Kumamvetsera Mphunzitsi Wamkulu’yo—Chicheŵa
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi (Lalikulu ndi laling’ono)—Chicheŵa
New World Translation of the Holy Scriptures (Deluxe la m’thumba; DLbi25b), lakuda—Chingelezi
◼ Makaseti Omwe Alipo:
Kingdom Melodies Na. 1, 3, ndi 4 (Imodziimodzi)
Sing Praises to Jehovah (Alabamu ya makaseti 8)