Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa May 1 kufikira August 21, 1995. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Kulambira Mulungu ndi nkhani yaumwini ndipo siimadalira konse paunansi wathu ndi ena. (1 Yoh. 4:20) [uw-CN tsa. 134 ndime 7]
2. Uphungu wa bungwe lolamulira kwa Akristu Akunja wa kusala kupembedza mafano, mwazi, ndi dama unazikidwa pa Chilamulo cha Mose. (Mac. 15:28, 29) [uw-CN tsa. 149 ndime 8]
3. Poyamba, Chilamulo cha Mose chinafunikira kugwira ntchito kwa anthu onse. (Sal. 147:19, 20) [uw-CN tsa. 147 ndime 5]
4. Bungwe Lolamulira silimamangika ndi zivomerezo zoika anthu pamathayo zopangidwa ndi bungwe lililonse la akulu a mpingo. [om-CN tsa. 41 ndime 1]
5. Mawu a Solomo pa Mlaliki 3:1, 2 amangonena za kuchitika kosalekeza kwa moyo ndi imfa, osati za kuikiratu za mtsogolo mwa munthu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 10/15 tsa. 5.]
6. Kulibe kwina kulikonse padziko kumene kungachokere uphungu wanzeru wolingana ndi umene Baibulo limapereka pankhani za banja. [uw-CN tsa. 144 ndime 11].
7. Lerolino, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene Yesu Kristu anati akagaŵira chakudya panthaŵi yake ali Mkristu mmodzi. [om-CN tsa. 25 ndime 2]
8. Makolo amene amalola ana awo kuonerera zilizonse pa wailesi yakanema, kwenikweni amakhala akuwalekerera. (Miy. 29:15) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 8/1 tsa. 11 ndime 8.]
9. Pamene mavuto abuka m’banja, Mkristu weniweni samapanga zolakwa za mnzake wa muukwati kukhala chodzikhululukira chonyalanyazira mathayo ake. [uw-CN mas. 140-1 ndime 4, 5]
10. Oyang’anira nkhosa za Mulungu oyenerera sayenera kudera nkhaŵa za mayendedwe awo m’chitaganya, malinga ngati amadzisungira bwino m’banja lawo. [om-CN tsa. 33 ndime 1]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Kodi ndi chiphunzitso chotani chimene chili pa Eksodo 20:7? [uw-CN tsa. 152]
12. Kodi wochititsa Phunziro Labuku Lampingo ali ndi mathayo aakulu aŵiri ati? [om-CN tsa. 44 ndime 1, 2]
13. Monga momwe kwafotokozedwera pa Yesaya 14:4, 12-14, kodi mfumu ya Babulo inaonetsa kaimidwe ka maganizo ka yani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w85-CN 9/1 tsa. 16 ndime 2.]
14. Malinga ndi kunena kwa Eksodo 19:10, 11, kodi Yehova amafunanji kwa alambiri ake? [uw-CN tsa. 152]
15. Kodi mlonda wamakono ndani, ndipo kodi akulengezanji? (Yes. 21:8, 12) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 3/1 tsa. 19 ndime 10.]
16. Kodi nchifukwa ninji Mlaliki 12:12 amapereka lingaliro losayanja za mabuku? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 9/15 tsa. 25.]
17. Pogwira mawu Salmo 68:18, kodi mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito lembalo pachiyani kulinga ku mpingo Wachikristu? [om-CN tsa. 24 ndime 3]
18. Kodi Paulo anatanthauzanji pamene analangiza Akorinto kuti ‘akulitsidwe’? (2 Akor. 6:13) [uw-CN tsa. 137 ndime 14]
19. Kodi chikondi “chilimba ngati imfa” motani? (Nyimbo 8:6, 7) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 11/15 tsa. 25.]
20. Kodi kukalimira udindo wa woyang’anira kumatanthauzanji? [om-CN tsa. 39 ndime 1]
Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Ngakhale kuti sitili pansi pa Chilamulo cha Mose, tapindula nacho chifukwa cha chidziŵitso cholongosoka cha ․․․․․․․ amene chazikidwapo ndi zitsanzo ․․․․․․․ zimene chili nazo. [uw-CN tsa. 153 ndime 14]
22. Lamulo la pa Eksodo 20:4-6 limaletsa ․․․․․․․, ndipo lembalo limasonyeza kuti lamulo limeneli lazikidwa pa chilangizo chakuti Yehova amafuna ․․․․․․․. [uw-CN tsa. 152]
23. Chilangizo cha pa Deuteronomo 7:1-4 chimasonyeza bwino lomwe kuti mtumiki wa Mulungu sayenera ․․․․․․․ ndi munthu wosatumikira ․․․․․․․ . [uw-CN tsa. 152]
24. Pa Nyimbo ya Solomo 2:1-3, pakutchulidwa mawu okuluŵika osonyeza kudzichepetsa ndi kufatsa kwa ․․․․․․․, limodzinso ndi makhalidwe abwino ndi maluso a ․․․․․․․ wake wokondedwa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 11/15 tsa. 24.]
25. Atumiki a Yehova okhulupirika amapeŵa kufunsira za ․․․․․․․ kwa ․․․․․․․, chifukwa chakuti kulankhulana koteroko kuli kukambitsiranadi ndi ․․․․․․․. (Yes. 8:19) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 3/15 tsa. 20 ndime 11.]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Malinga ndi kunena kwa Miyambo 26:20, 21, ngati tikhala (ofulumira kuyankha; olankhula kwambiri; oleza mtima), m’malo mwa ‘kuwonjezera nkhuni pamoto’ ndi kuputa ena, tidzakhala (osamvana nawo; olephera kulankhulana nawo bwino; nawo paunansi wabwino). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 10/15 tsa. 13 ndime 16.]
27. Malinga ndi kunena kwa Miyambo 27:6, munthu amene amakukondani (sadzanena kanthu kokupwetekani mtima; adzachita mantha kukuuzani zoona ponena za inu; adzakupatsani uphungu pamene uli wofunika kwa inu). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 9/15 tsa. 28.]
28. Miyezo ya Malemba ya oyang’anira Achikristu ili (yotsika; yokwera; yosadetsa nkhaŵa) kwenikweni popeza kuti amuna ameneŵa ali ndi thayo lalikulu la kutsogolera pakulambira Yehova ndi kukhala chitsanzo m’mayendedwe Achikristu. [om-CN tsa. 30 ndime 1]
29. Anthu amene amaganiza kuti kalingaliridwe kamakono kosadziletsa kakuti, zinthu zonse nzololeka ndiko kupita patsogolo (sali owononga; ali ololera; ali mumdima wauzimu) kwenikweni. (Yes. 5:20) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 3/1 tsa. 11.]
30. Kuti akhale wolama m’maganizo, munthu amene ayeneretsedwa kutumikira monga woyang’anira ayenera (kuzindikira bwino ziphunzitso za Yehova ndi mmene zimagwirira ntchito; kukhala wotengeka maganizo; wonena paŵiri). [om-CN tsa. 35 ndime 1]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Miy. 22:3; Mlal. 7:21, 22; Yes. 13:19, 20; Mat. 5:23, 24; Akol. 3:18-20, 23, 24
31. Ngakhale kuti Yehova samangotetezera anthu ake ku ngozi, mikangano ya nkhondo, kapena upandu, kugwiritsira ntchito nzeru yeniyeni ya Baibulo kungakhale kopindulitsa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 1/1 tsa. 17 ndime 23.]
32. Pali umboni wokwanira wosakayikirira kukwaniritsidwa kwa ulosi wouziridwa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 5/15 tsa. 6.]
33. Mkristu weniweni amachitapo kanthu kuti akulitse maunansi amtendere ndi abale ake. [uw-CN tsa. 135 ndime 10]
34. Kupititsa patsogolo maunansi abwino m’banja sikumachitika mwa kuyembekezera ena kuti achitepo kanthu, koma aliyense ayenera kuthandiza, mwakutero amasonyeza kudzipereka kwaumulungu panyumba. [uw-CN tsa. 143 ndime 10]
35. Musayembekezere ungwiro kwa inu mwini kapena kwa anthu anzanu opanda ungwiro. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 3/1 tsa. 8.]
S-97-CN-MAL & ZAM #286b 8/95