Makolo Amene Amakondwera!
1 Ngati muli wachinyamata amene akukhala pa nyumba Yachikristu, pali njira yapadera imene mungachititsire makolo anu kukhala achimwemwe. Ngati mulondola njira yolungama, ‘atate wanu ndi amanu adzakondwera.’ (Miy. 23:22-25) Mwachibadwa makolo anu amakufunirani zabwino koposa. Palibe chinthu chimene chingawakondweretse kwambiri kuposa kukuonani mukupanga choonadi kukhala chanu ndi kupatulira moyo wanu kwa Yehova.
2 Muyenera kuthokoza pokhala ndi makolo amene ali m’choonadi. Kuyambira pa kubadwa kwanu, akudyetsani, kukuvekani, ndi kukupezerani pokhala ndiponso kukusamalirani panthaŵi za kudwala. Chofunikadi koposa nchakuti, iwo ayesayesa kukuphunzitsani za Yehova ndi njira zake zolungama; ameneŵa ndi maphunziro amene angakuchititseni kupeza moyo wosatha. (Aef. 6:1-4) Kodi mungasonyeze motani chiyamikiro chanu?
3 Pangani Choonadi Kukhala Chanu: Makolo anu ayesayesa kukuphunzitsani kuona choonadi mwamphamvu, kupita patsogolo kwauzimu, ndi kumamatira ku gulu la Yehova. Mungasonyeze chiyamikiro mwa kukhala ndi chikondwerero m’phunziro labanja popanda kuumirizidwa. Sonyezani chikhumbo cha kufika pamisonkhano, mukumayambirira inu mwininu kukonzekera kotero kuti banja lanu lifikepo panthaŵi yake. Khalani ndi makolo anu mkati mwa misonkhano, ndipo mvetserani mosamalitsa mwa kutsatira zofalitsidwa zimene zikuphunziridwa. Kalimirani pa kukhala ndi phande m’misonkhano mwa kupereka ndemanga. Sonyezani kukhala wophunzira wakhama pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki, mukumalandira nkhani ndi kuyesayesa kuzikamba bwino. Dziperekeni pa kuthandiza kugwira ntchito zina pa Nyumba Yaufumu, pamene thandizo lanu lingakhale lofunika. Kutengamo mbali m’zochitika zotero kungachititse mtima wanu kukhalabe pa zinthu zabwino kaamba ka mkhalidwe wanu wauzimu.
4 Ikani Zonulirapo Zopita Patsogolo: Kalimirani pa kukhala ndi phande latanthauzo mu utumiki wakumunda, mukumasonyeza chikhumbo chakuti muyenerere kukhala wofalitsa. Tsatirani kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu, ndiponso kuti mupindule kwambiri, ŵerengani pa nokha Baibulo lonse. Tsimikizirani kuti mudzakwaniritsa zofunika za kudzipatulira ndi ubatizo. Makolo anu angakuthandizeni kulinganiza makosi anu a kusukulu mosamalitsa, ndi cholinga chakuti mupeze maphunziro amene adzakukonzekeretsani kukhala ndi phande lokwanira mu utumiki wa Yehova. Yesayesani kukulitsa mkhalidwe umene udzachititsa ena kukulimbikitsani kutenga mwaŵi wapadera monga upainiya kapena utumiki wa pa Beteli. (Mac. 16:1, 2) Kufikira zonulirapozo kungakuthandizeni ‘kutsimikizira zinthu zofunika koposa, kotero kuti . . . mukadzazidwe ndi zipatso za chilungamo.’—Afil. 1:10, 11, NW.
5 Unyamata ndi nthaŵi ya kuphunzira, kupeza chidziŵitso, ndi kupeza maluso pochita ndi ena. Ndiyo nthaŵi imene mungasangalale ndi moyo popanda zitsenderezo ndi mathayo amene amakhalapo pamene munthu akula. Solomo anati: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako.” (Mlal. 11:9) Ngati muika mtima wanu pa kutumikira Yehova mu unyamata wanu, mudzalandira madalitso amene adzakhala kosatha.—1 Mbiri 28:9.
6 Ngati ‘mutsata chilungamo’ m’malo mwa “zilakolako za unyamata,” simudzachititsa makolo anu nkhaŵa yaikulu ndi kuwavutitsa. (2 Tim. 2:22) Mudzachititsa mtima wanu kukhala wokondwera. (Miy. 12:25) Koposa zonse, mudzakondweretsa Mlengi wanu, Yehova Mulungu.—Miy. 27:11.