Misonkhano Yautumiki ya August
Mlungu Woyambira August 7
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Fotokozani mfundo zokondweretsa za m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha zimene zingasonyezedwe m’maulaliki.
Mph. 15: “Lemekeza Yehova ndi Chuma Chako.” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: “Khalani Aphunzitsi a Mawu a Mulungu—Mwa Kugwiritsira Ntchito Mabrosha.” Mbale wopatsidwa nkhani imeneyi adzakambitsirana ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu ponena za mbali zosiyanasiyana za mabrosha. Ndiyeno adzachita chitsanzo cha kulalikirana.
Nyimbo Na. 137 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 14
Mph. 5: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 10: Gwiritsirani Ntchito Bwino Koposa Mwaŵi wa ku Sukulu. Mkulu akusonyeza mmene kholo lingakambitsirane ndi mwana wamwamuna kapena wamkazi wachinyamata ponena za kusankha makosi amene angaphunzire kusukulu. Fotokozani kufunika kwa kusankha maphunziro amene adzakhala othandiza pa ntchito ya utumiki.—Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1992, masamba 16-18, ndime 3-11.
Mph. 15: “Makolo Amene Amakondwera!” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1987, masamba 13-15, ndime 14-23.
Mph. 15: “Khalidwe Lachikristu ku Sukulu.” Mafunso ndi mayankho. Limbikitsani makolo kuŵerenganso Nsanja ya Olonda ya July 15, 1991, masamba 23-6, ndi ana awo, makamaka mbali zonena za nkhani zimene ana angakumane nazo.
Nyimbo Na. 157 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 21
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. “Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.” Lengezani deti la msonkhano wapadera wotsatira ngati mukulidziŵa. Limbikitsani onse kudzafikapo.
Mph. 15: “Kudzipereka Ife Eni Mwaufulu Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino.” Nkhani yotentha yoperekedwa ndi mkulu pandime 1-9.
Mph. 20: “Kudzipereka Ife Eni Mwaufulu Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino.” Kukambitsirana kwa ndime 10-15 kwa mafunso ndi mayankho. Tchulani zosoŵa za pamalopo ndi mmene onse angaperekere thandizo.
Nyimbo Na. 156 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 28
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo.
Mph. 15: “Maulendo Obwereza Achipambano Amafuna Kuphunzitsa Kogwira Mtima.” Fotokozani mfundo zazikulu ndipo konzani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zachidule. Chitsanzo chachiŵiri chiyenera kukhala chogwiritsira ntchito buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.
Mph. 20: Gaŵirani Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha mu September. Fotokozani mmene bukuli limaperekera thandizo lofunika popereka uthenga wachiweruzo wa Yehova. (Onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 1988, masamba 25-6, ndime 17-18.) Simbani chokumana nacho cha mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1992 patsamba 15, ndime 3-4. Sonyezani zithunzithunzi zochititsa chidwi zimene zili pamasamba 3, 11-13, ndi 156-8 a bukulo. Fotokozani za mmene zithunzithunzi zimenezi zingagwiritsidwire ntchito kuyambitsira makambitsirano. Wofalitsa wokhoza bwino achite chitsanzo cha ulaliki wachidule akumagwiritsira ntchito limodzi la mavesi a Malemba opezedwa pamasamba 156-8. Gogomezerani chonulirapo cha kuyesayesa kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Kumbutsani onse kudziwombolera makope okagwiritsira ntchito kutha kwa mlungu uno.
Nyimbo Na. 178 ndi pemphero lomaliza.