Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu October: Masabusikripishoni a Galamukani! kapena Nsanja ya Olonda kapena zonse ziŵiri. November: Gaŵirani buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha pamkupiti wapadera. Mipingo imene ilibe buku limeneli m’sitoko idzagaŵira New World Translation ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? December: Buku latsopano lakuti Knowledge That Leads to Everlasting Life lidzagaŵiridwa, ndipo tiyenera kuyesetsa kupanga maulendo obwereza, ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. January: Gaŵirani buku la Moyo wa Banja pamkupiti wapadera. Mipingo imene ilibe mabukuwo ingagaŵire buku lililonse la masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene siinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambazo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Mphatika imene ili m’kope lino la Utumiki Wathu Waufumu ndi “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996” ndipo iyenera kusungidwa kuti muzionamo chaka chonse cha 1996.
◼ Malinga ndi kalata yathu ya SK May 17, 1995, yotumizidwa ku mipingo yonse, tikukumbutsa oyang’anira utumiki onse kuti, October 1995, udzakhala mwezi wapadera wogaŵira magazini. Chotero, ayenera kukonza tsiku la magazini m’mweziwo, ndiko kuti tsiku lopatulidwa kaamba ka umboni wa magazini.
◼ Popeza mabuku a Moyo wa Banja ndi Kukhala ndi Moyo Kosatha tilibe kuno ku nthambi, mungagwiritsire ntchito zogaŵira zina m’miyezi yonse imene mabukuŵa ayenera kugaŵiridwa. Mabuku otchulidwawo amene tilibe angapezekebe m’mipingo koma sayenera kuodedwa ku Sosaite.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Good News for All Nations—Chingelezi
Mboni za Yehova ndi Maphunziro—Chicheŵa, Chingelezi
Knowledge That Leads to Everlasting Life—Chingelezi
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona—Chicheŵa, Chifrenchi, Chingelezi, Chipwitikizi, Chiswahili
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1996 paoda yawo ya mabuku ya October. Timabuku timeneti tidzakhalako m’Chicheŵa, ndi Chingelezi. Tidzasonyezedwa kuti “Zoyembekezeredwa” pampambo wolongedzera katundu kufikira titakhalako ndi kutumizidwa. Timabuku ta Kusanthula Malemba tili zinthu za oda yapadera.