Mbiri Yateokrase
Cuba: Posachedwapa boma la Cuba linalola woimira Sosaite kuchezera Cuba monga woyang’anira woyendera nthambi. Iye anachita msonkhano ndi oyang’anira madera ndi a zigawo. Tsopano abale akhoza kusonkhana m’magulu a anthu okwana 150. Iwo akuyamikira kuti tsopano ali ndi ufulu wokulirapo ndi kuti Nyumba ya Beteli ingagwiritsiridwe ntchito monga likulu la Mboni za Yehova m’Cuba.