Lemba Lililonse Lipindulitsa pa Chiphunzitso
1 Malingaliro onena za kufunika kwa Baibulo ngambiri ndipo ngosiyanasiyana. Komabe, timakhulupirira kuti m’masamba ake muli mayankho a mavuto othetsa nzeru a anthu pamodzinso ndi chitsogozo chodalirika cha njira yathu yamoyo. (Miy. 3:5, 6) Nzeru ya uphungu wake njosayerekezereka. Miyezo yake ya makhalidwe abwino amene limachirikiza njopambana. Uthenga wake ngwamphamvu, wokhoza ‘kuzindikiritsa zolingilira ndi zitsimikizo za mtima.’ (Aheb. 4:12) Kodi tingathandize ena motani kuona kufunika kwa kutsitsa buku limeneli pa shelufu ndi kulipenda mosamalitsa? Mwina mungakonde kuyesa zina za njira zotsatirapozi pogaŵira New World Translation pamodzi ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? m’November.
2 Popeza anthu ambiri amada nkhaŵa ponena za zofunikira zawo zazikulu, mwinamwake mafikidwe awa akhoza kuwakopa:
◼ “Anthu ambiri amene ndimalankhula nawo masiku ano ali ndi nkhaŵa ya mmene angapezere ndalama. Ambiri agwidwa mu msampha wa kufunafuna zinthu zakuthupi, ndipo zimenezi zimachititsa kupsinjika maganizo. Kodi nkuti kumene kuli malo abwino kwambiri koti titembenukireko kaamba ka uphungu pankhani zotero? [Yembekezerani yankho.] Ndapeza kuti Baibulo limapereka uphungu wogwira ntchito umene ungatithandize kupeŵa mavuto osayenera. Ndiloleni ndikuonetseni chitsanzo.” Tsegulani patsamba 163 m’buku lakuti Baibulo—Kodi ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi kuŵerenga 1 Timoteo 6:9, 10, logwidwa mawu m’ndime 3. Fotokozani ndemanga zowonjezereka za pandime 4, ndiyeno gaŵirani bukulo.
3 Nayi njira ina imene mungaigwiritsire ntchito:
◼ “Nthaŵi zonse pamene tiŵerenga nyuzipepala kapena kumvetsera nkhani za pawailesi timamva za vuto lina losautsa maganizo limene limatichititsa kuda nkhaŵa. [Tchulani chochitika chosokoneza maganizo chaposachedwa chotchulidwa pankhani za pawailesi.] Kodi tingachite motani ndi mavuto onga ameneŵa? [Yembekezerani yankho.] Kale mu 1983, yemwe anali pulezidenti wa United States panthaŵiyo [Ronald Reagan] ananena kuti Baibulo lili ndi uthenga waukulu kuposa wonse umene unalembedwapo ndi kuti ‘m’masamba ake muli mayankho a mavuto onse amene munthu anadziŵapo.’ Zimene ananena zimatikumbutsa zimene Baibulo lenilenilo limanena. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:16, 17.] Ndiloleni ndikusonyezeni chifukwa chimene tingakhalire ndi chidaliro pa Baibulo.” Sonyezani nsonga zina m’trakiti lakuti Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo. Lonjezani kudzabweranso kuti mudzakambitsirane mmene kukwaniritsidwa kwa maulosi m’zochitika za dziko zamakono kulili kwapadera.
4 Ngati muli anthu ambiri osapembedza m’gawo lanu, mungayese mafikidwe awa:
◼ “Anthu ambiri m’dera lino amaona mabuku ena opatulika monga ngati otsutsa ndipo monga ngati nthano chabe. Iwo aona zinthu zambiri zoipa zochitidwa m’dzina la chipembedzo kwakuti ngakhale Baibulo sakulidalira. Kwenikweni, anthu owonjezerekawonjezereka akukayikira kuti kaya Baibulo ndilo Mawu a Mulungu kapena a munthu. Kodi lingaliro lanu nlotani?” Yembekezerani yankho. Modalira pa yankho la mwininyumba, tsegulani patsamba la buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? pamene pamafotokoza za mfundo ya mwininyumba, ndipo kambitsiranani mfundo imodzi kapena ziŵiri. Mwachitsanzo, mungakhale ndi mwaŵi wa kugwiritsira ntchito ndime 27-9 kuyambira patsamba 66, pakamutu kakuti “Yesu—Munthu Weniweni.”
5 Mlangizi wathu Wamkulu watsimikiza kuti chidziŵitso cha chifuno chake chipezeke kwa onse amene akufuna kuphunzira. Kuthandiza ena kudziŵa kufunika kwenikweni kwa Baibulo kuli chimodzi cha zinthu zabwino koposa zimene tingachite kuwathandiza; kungapulumutse miyoyo yawo.—Miy. 1:32, 33.