Lingalirani za Kumwamba
1 Pothirira ndemanga za mbadwo wotizungulirawu ndi kaonedwe kake ka mtsogolo, nkhani ina mu The New York Times ya December 31, 1994, inati: “Iwo akuopa mtsogolo. Ali ndi mantha onena za kusowa kwa ntchito, za matenda, za zachuma, za mikhalidwe ya dziko.” Kulikonse kumene tiyang’ana, anthu ali osatsimikiza ponena za moyo. Utumiki wathu monga Mboni za Yehova umatichititsa kukumana ndi anthu amalingaliro otere tsiku ndi tsiku. Pamene kuli kwakuti timakumana ndi mavuto amodzimodziwo monga iwo, chikhulupiriro chathu ndi chidaliro chathu m’malonjezo otsimikizirika a Mawu a Mulungu zimatichititsa kukhala ndi kaonedwe kosiyana kwambiri ka moyo ndi mtsogolo mwa anthu.—Yes. 65:13, 14, 17.
2 Kutsimikiza ndi kaonedwe kathu ka chiyembekezo chotsimikizirika kumapangitsa anthu oona mtima ambiri kumvetsera uthenga umene timawaperekera. Anthu ambiri amene amachita tondovi ndi othodwa amakuona kukhala kotonthoza kulankhula nafe. Chifukwa chakuti amakonda zimene amamva, ena amavomera kuphunzira nafe Baibulo. Komabe, nthaŵi zina, anthu angafune kutitulira choyamba katundu wa mavuto awo aumwini. Pamene kuli kwakuti tingapatule nthaŵi ya kumvetsera nkhaŵa zaumwini za winawake, sitiyenera kuiŵala chifuno chathu, chimene chili kuphunzitsa anthu choonadi chabwino cha Mawu a Mulungu.
3 Timafuna kuchitira chifundo awo amene ali othodwa. Monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 11:28, Yesu anapereka chitsanzo pamene anati: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa.” Tikufuna kulimbikitsa anthu m’njira imodzimodziyo. Komabe, onani mathedwe a vesi 28, Yesu anati: “Ine ndidzakupumulitsani inu.” Chimenecho chiyenera kukhala chonulirapo chathu. Timachita zimenezo mwa kuuza ena malonjezo otsitsimula a m’Mawu a Mulungu. Kukhala womvetsera wabwino kumasonyeza chikondwerero ndi kukhudzidwa kwathu kwaumwini ndipo nkofunika kwambiri kuti tikwaniritse ntchito yathu ya kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, tikumathandiza ena kuzindikira kuti Ufumuwo ndiwo mankhwala otsimikizirika okha a mavuto a anthu.—Mat. 24:14.
4 Ntchito yathu si ija ya akatswiri a zaumoyo. M’malo mwake, ili monga mmene mtumwi Paulo anafotokozera, monga momwe kwalembedwera pa 1 Timoteo 4:6, utumiki umene umasumika pa “malangizo abwino,” malangizo amene amapezeka m’Mawu a Mulungu. Awo okhala ndi mavuto aumwini kapena mavuto a malingaliro afunikira kulimbikitsidwa kudalira pa Yehova. Aphunzitseni ‘kulingalira za kumwamba’—zinthu zogwirizana ndi chiyembekezo cha Ufumu. (Akol. 3:2) Pamene anthu asumika chisamaliro chawo pa Mawu a Mulungu, angalimbitsidwe monga chotulukapo cha chisonkhezero champhamvu chimene mawuwo amapereka m’moyo wawo.—Aheb. 4:12.
5 Motero chonulirapo chathu ndicho kuthandiza anthu kusumika maganizo awo pa zinthu zimene zili ‘zolungama, zoyera, zokongola, zachitamando.’ (Afil. 4:8) Ngati iwo asumika chisamaliro chawo pa chiyembekezo cha Ufumu, adzadalitsidwa monga mmene zakhalira kwa ife. Iwonso adzakhala ndi chimwemwe chomwe chimadza ndi chidziŵitso chakuti potsirizira pake Yehova adzathetsa mavuto awo onse kupyolera mwa Ufumu wake.—Sal. 145:16.