Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/96 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya June

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya June
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira June 3
  • Mlungu Woyambira June 10
  • Mlungu Woyambira June 17
  • Mlungu Woyambira June 24
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 6/96 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya June

Mlungu Woyambira June 3

Nyimbo Na. 181

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Longosolani lipoti la utumiki wakumunda la dziko lathu lino ndi la mpingo.

Mph. 15: “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo.” Mafunso ndi mayankho. Pendani maumboni a chikhulupiriro, otchulidwa m’bokosi patsamba 13 mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1991. Funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵiri kuona zimene zawathandiza kupitiriza ntchito yawo ya Ufumu kwa zaka zambiri.

Mph. 20: “Kufalitsa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.” (Ndime 1-3) Fotokozani ndime 1. (Phatikizanipo ndemanga zochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, masamba 12-13, ndime 11-12.) Fotokozani kuti mpangidwe watsopano wa tsamba lakumbuyo la Utumiki Wathu Waufumu unakonzedwera kutithandiza kukhala okonzekera bwino kupanga maulendo obwereza. Popeza kuti nthaŵi zonse kumakhala kwanzeru kupanga ulendo wobwereza tsiku lomwelo kapena lotsatira, m’malo moyembekeza kwa nthaŵi yaitali, tidzapenda maulaliki osonyezedwa a ulendo woyamba wa kunyumba ndi nyumba ndi ulendo wobwereza pa Msonkhano Wautumiki umodzimodziwo. Mwachidule pendani ndime 2 ndi 3, ndiyeno sonyezani chitsanzo cha uliwonse. Maulaliki otsalawo m’nkhaniyo adzapendedwa pa Misonkhano Yautumiki iŵiri yotsatira.

Nyimbo Na. 143 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 10

Nyimbo Na. 63

Mph. 7: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 8: Kuphunzitsa Ana mu Utumiki Wakumunda. Nkhani ya mkulu. Kuyambira paubwana, ana athu ayenera kukhala okangalika pamodzi nafe muutumiki. Chiphunzitso ndi chidziŵitso zimene apeza zidzawapatsa maziko olimba a chikhulupiriro chawo ndi changu m’zaka zapambuyo pake. Nkofunika kwambiri kuti azindikire kufunika kwa kuona utumiki mwamphamvu ndi kudzisungira bwino iwo eni. Ana ayenera kupeŵa makhalidwe opulupudza; utumiki si nthaŵi yoseŵera. Ndi bwino kuti iwo agwire ntchito ndi achikulire. Ayenera kuthandizidwa kupereka maulaliki malinga ndi kukhoza kwawo. (Onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 1988, tsa. 15, ndime 20.) Makolo ali ndi thayo la kuwayang’anira; sayenera kutumiza ana muutumiki popanda munthu wamkulu wowayang’anira. Yamikirani ana pamene achita bwino.

Mph. 10: “Kufalitsa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.” (Ndime 4-5) Mutakamba mawu anu oyamba achidule, sonyezani ulendo woyamba ndi wobwereza m’ndime 4 ndi 5. Limbikitsani ofalitsa kubwerera mwamsanga kulikonse kumene anasiya buku la Chidziŵitso.

Mph. 20: “Mmene Tingapangire Ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso.” Perekani ndemanga zoyambirira zachidule zozikidwa pa ndime 1-2. Kambitsiranani ndime 3-11 mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani kuti mbali yotsalayo ya mphatika idzaphunziridwa pa Msonkhano Wautumiki mu July ndi August. Limbikitsani onse kuisunga bwino.

Nyimbo Na. 92 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 17

Nyimbo Na. 157

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Bokosi la Mafunso.

Mph. 15: “Makambitsirano Aubwenzi Angafike Pamtima.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani wofalitsa mmodzi kapena aŵiri kuti asimbe zokumana nazo zolimbikitsa zosonyeza mmene anapezera chiyanjo chabwino mwa kafikidwe kaubwenzi.

Mph. 20: “Kufalitsa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.” (Ndime 6-7) Gogomezerani zonulirapo popanga ulendo wobwereza: Kukulitsa chikondwerero, kuyambitsa phunziro, kupanga makonzedwe otsimikizirika akubwererako. Mutapenda mwachidule maulaliki m’ndime 6 ndi 7, sonyezani chitsanzo cha uliwonse wa iwo, mukumasonyeza mmene tingayambitsire phunziro. Ŵerengani ndime 17 patsamba 13-14 mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996.

Nyimbo Na. 211 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 24

Nyimbo Na. 6

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Longosolani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda pa July 1 ndi 2.

Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. (Kapena perekani nkhani pa mutu wakuti “Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Choonadi,” yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya January 1, 1996, masamba 29-31.)

Mph. 20: “Athandizeni Kuyambanso Kutumikira.” Nkhani ndi kukambitsirana kochititsidwa ndi mkulu. Tchulani za kugwiritsira ntchito nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1992, yakuti “Bwererani Kudza kwa Ine, Ndipo Ine Ndidzabwerera kwa Inu” kulimbikitsira ofooka. Tchulani zina za mfundo zazikulu.

Nyimbo Na. 71 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena