Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/96 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 8/96 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu August: Lililonse la mabrosha otsatirawa amasamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”. Kumene kuli koyenera, mabrosha monga Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Problems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? angagaŵiridwe. September: Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Mipingo imene ili ndi Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kapena Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe m’stoko ingagaŵire mabuku ameneŵa. October: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda kapena ya Galamukani! kapena ya magazini onse aŵiri. November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kuyesayesa kwapadera kudzachitidwa kubwerera kulikonse kumene tinagaŵira zofalitsa, ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.

◼ Mtokoma wokwanira wa mafomu ogwiritsira ntchito m’chaka chautumiki cha 1997 ukutumizidwa ku mipingo yonse. Chonde gwiritsirani ntchito mafomu ameneŵa mwanzeru. Ayenera kugwiritsiridwa ntchito kokha pachifuno chawo.

◼ Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-AB-18). Mlembi wa mpingo ayenera kukumana ndi mtumiki wa mabuku kuchiyambi kwa August ndi kuika deti la kuŵerengera mabuku amene ali m’stoko ya mpingo pakutha kwa mwezi. Mabuku onse amene ali m’stoko ayenera kuŵerengedwa, ndipo ziwerengero zonse ziyenera kulembedwa pa fomu ya Kuŵerengera Mabuku. Chiŵerengero chonse cha magazini amene alipo chingatengedwe kwa mtumiki wa magazini. Chonde tumizani kope loyamba ku Sosaite mosapyola pa September 6. Sungani kope lachiŵiri m’mafaelo anu. Kope lachitatu mungaligwiritsire ntchito monga lowonkhetserapo. Kuŵerengerako kuyenera kuyang’aniridwa ndi mlembi, ndipo fomu yodzazidwa iyenera kupendedwa ndi woyang’anira wotsogoza. Mlembi ndi woyang’anira wotsogoza adzasaina fomuyo.

◼ Mu August mpingo uliwonse udzalandira makope aŵiri a Lipoti la Kulongosola Ntchito za Mpingo (S-10). Komiti Yautumiki iyenera kutsimikizira kuti mafomu ameneŵa adzazidwa molongosoka ndi kubwezeredwa ku Sosaite mosapyola pa September 10.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1997 pa oda yawo ya mabuku ya September. Makalendawo adzakhalako m’Chicheŵa ndi Chingelezi.

◼ Kuyambira pa August 26, 1996, kufika pa August 31, 1996, Sosaite idzakhala ikuŵerengera mabuku onse amene aliko ku Zambia. Chifukwa cha kuŵerengera kumeneku, palibe maoda a mipingo amene adzatumizidwa kapena kutengedwa pa masiku amenewo. Chonde dziŵaninso kuti Chipinda Chamabuku cha pa Beteli chidzakhala chotseka pa masiku amenewo choncho mabuku sadzagulitsidwa kwa abale odzacheza.

◼ Makonzedwe otsatiraŵa ayenera kupangidwa pa maphunziro Abuku Ampingo onse mkati mwa mlungu wa msonkhano wachigawo: Nkhani yophunziridwa ya mlunguwo yiyenera kugaŵidwa pakati ndipo theka la iyo iyenera kuphunziridwa pamodzi ndi nkhani ya mlungu wotsatiridwa ndi msonkhano wachigawo pamene theka linalo liyenera kuwonjezeredwa pa nkhani ya mlungu wa pambuyo pa msonkhano wachigawo. Ngati kuli koyenera musaŵerenge ndime. Mipingo ikukumbutsidwa kuti pakhala kuyesa kugaŵira chiŵerengero chaching’ono cha masamba mlungu uliwonse kuti kuŵerenga malemba onse opezeka m’phunzirolo kukhale kotheka.

◼ Tikufuna kudziŵitsa pasadakhale onse amene anakhala pampambo monga apainiya okhazikika kuyambira pa October 1, 1995 kapena detilo lisanafike, ndipo amene sanaloŵebe Sukulu Yautumiki Waupaniya kuti sukuluyo idzakhalako mu October 1996. Chonde pangani makonzedwe otsimikiza a kukapezeka pa Sukulu Yautumiki Waupaniya mu October. Ena kumbuyoku aphonya makonzedwe ameneŵa popanda zifukwa zabwino. Sitikufuna kuti mpainiya aliyense akaphonye sukuluyo. Chidziŵitso chowonjezereka chidzatumizidwa kwa inu ndi woyang’anira dera.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Mabaundi Voliyumu a Watchtower a 1956 ndi 1957—Chingelezi

◼ Ma Vidiyokaseti Atsopano Omwe Alipo:

The New World Society in Action—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena