Anthu Amtundu Uliwonse Adzapulumutsidwa
1 Chifuniro cha Yehova “nchakuti anthu amtundu uliwonse apulumuke nafike pa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi.” (1 Tim. 2:4, NW) Ngakhale kuti anthu amasonkhezereka kuchita zinthu zina ndi chibadwa, makulidwe awo, ndi malo, iwo ali ndi ufulu wodzisankhira ndipo akhoza kusankha okha mmene afuna kugwiritsirira ntchito moyo wawo. Akhoza kuchita chabwino ndi kukhala ndi moyo, kapena kuchita choipa ndi kuwonongeka. (Mat. 7:13, 14) Kodi lingaliro limeneli likukhudza motani kaonedwe kathu ka anthu omwe timawafikira ndi uthenga wabwino wa Ufumu?
2 Tisalingalire kuti zimene zimachititsa munthu kukhala ndi chidwi pa choonadi ndizo zinthu monga fuko lake kapena makulidwe kapena malo m’chitaganya. Choonadi chimakopa anthu ophunzira pang’ono ndi ophunzira kwambiri omwe, olondola nkhani zandale, ndi akatswiri, okana Mulungu, okayikira Mulungu, ndipo ngakhale ochita zoipitsitsa. Anthu amakulidwe osiyanasiyana ndi a malo osiyanasiyana asintha mayendedwe awo akale ndipo tsopano ali panjira ya ku moyo m’dziko latsopano la Mulungu. (Miy. 11:19) Chifukwa chake, tisazengereze kufikira anthu amtundu uliwonse ndi uthenga wa Ufumu.
3 Talingalirani Zitsanzo Izi: Mwamuna wina anafuna kuti aphe atate wake opeza koma sanatero. Pambuyo pake anaganiza zodzipha yekha komanso analephera. Ataponyedwa m’ndende chifukwa cha kuba ndi kuzembetsa anamgoneka, ukwati wake unalephera. Lerolino munthuyu akukhala ndi moyo woona mtima ndipo akusangalala ndi ukwati wachimwemwe limodzinso ndi unansi wabwino ndi atate wake opezawo. Kodi nchiyani chinampangitsa kusintha chonchi? Anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndi kugwiritsira ntchito zimene anaphunzira. Yehova sanamuone monga munthu wosatheka kuwomboledwa.
4 Kutchuka kwa mtsikana wina monga wochita maseŵero pa TV sikunampatse chimwemwe. Koma pokopeka ndi makhalidwe abwino a Mboni, anavomereza phunziro la Baibulo, ndipo posapita nthaŵi iyenso anali kuthandiza anthu ena kuphunzira za uthenga wabwino wa Ufumu. Kulikonse kumene anapitako mu utumiki wa kukhomo ndi khomo anthu anamzindikira, koma iye anali wokondwa kufotokoza kuti anafuna kudziŵika monga mmodzi wa Mboni za Yehova m’malo mwa wamaseŵero.
5 Pamene Mboni ina inalinganiza phunziro la Baibulo ndi wina wolembetsa Nsanja ya Olonda, mnansi wapafupi anamva zimenezo ndipo anadzakhalapo paphunzirolo. Nthaŵi yomweyo mnansiyo anazindikira choonadi chomwe ankafunafuna nthaŵi yonseyo! Limodzi ndi mwamuna wake anakafafanizitsa chikalata cha chisudzulo chimene anali atapatsidwa kotero kuti abwererane. Mkaziyo anali wozama m’zakupenda nyenyezi ndipo ankagwirizana ndi kagulu ka mizimu, koma mosataya nthaŵi anataya mabuku a ndalama zambiri ndi kalikonse komwe anali nako kogwirizana ndi ziŵanda. Posapita nthaŵi anayamba kufika pamisonkhano ndi kumalankhula kwa achibale ndi mabwenzi ake za chikhulupiriro chake chatsopano. Tsopano akulalikira kwa ena mosangalala ndithu.
6 Tisaweruziretu munthu aliyense. M’malo mwake, tiyeni tilalikire mwachangu uthenga wabwino kwa anthu kulikonse. Tili ndi chifukwa chokwanira chakuti Yehova, amene “ayang’ana mumtima,” adzakhala “Mpulumutsi wa anthu onse.”—1 Sam. 16:7; 1 Tim. 4:10.